Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo 2: Khalani Wokhulupirika

Mfundo 2: Khalani Wokhulupirika

Mfundo 2: Khalani Wokhulupirika

“Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mateyo 19:6.

Mungachite bwanji? Kuti banja lanu liziyenda bwino, nonse muyenera kudziwa kuti banja ndi mgwirizano wa moyo wonse. M’banja mukakhala mavuto, nonse muyenera kuyesetsa kuwathetsa, m’malo mothetsa banjalo. Mwamuna ndi mkazi akamaona kuti banja ndi mgwirizano wa moyo wonse, amadziwa kuti banja lawo silingathe mwachisawawa. Aliyense amakhulupirira kuti mnzake sangaganize zothetsa banjalo.

Kufunika kwake. Kukhulupirika kumathandiza m’njira zosiyanasiyana kuti banja likhale lolimba. Komabe ngati mwamuna ndi mkazi amangokhalira kukangana, amaona kuti banja ndi lopanikiza. Ndipo munthu akakumbukira mawu amene analumbira patsiku la ukwati wake akuti “mpaka imfa idzatilekanitse,” mtima umamupweteka kwambiri moti amalakalaka anthu atakhala ndi ufulu wothetsa banja mmene akufunira. Mwina anthu oterewa sangathetsedi ukwati wawo, koma amachita zinthu zosonyeza kuti banja sakulifuna. Mwachitsanzo, amakana kukambirana ndi mkazi kapena mwamuna wawo pakabuka mavuto.

Yesani izi. Yankhani mafunso otsatirawa kuti mudziwe ngati muli wokhulupirika m’banja.

Tikakumana ndi mavuto, kodi ndimadandaula kuti ndinakwatirana ndi munthu wolakwika?

Kodi nthawi zambiri ndimasirira mkazi kapena mwamuna wina?

Kodi nthawi zina ndimauza mkazi kapena mwamuna wanga kuti, “Ndikusiya” kapena “Ndipeza mkazi kapena mwamuna wina amene angamandikonde”?

Chitani izi. Ganizirani chinthu chimodzi kapena ziwiri zimene mungachite kuti mukhale wokhulupirika kwambiri kwa mwamuna kapena mkazi wanu. (Mwachitsanzo, kulemberana timakalata tachikondi, kuika zithunzi za mwamuna kapena mkazi wanu pamalo amene mumagwirira ntchito ndiponso kuimbirana foni.)

Ganizirani zinthu zina zimene zingakuthandizeni ndipo funsani mkazi kapena mwamuna wanu kuti akuuzeni chinthu chimene chingamusangalatse kwambiri.

[Chithunzi patsamba 4]

Kukhulupirika kumateteza banja lanu ngati mmene zitsulo za m’mbali mwa msewu zimatetezera galimoto kuti isasiye msewu

[Mawu a Chithunzi]

© Corbis/age fotostock