Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo 3: Muzichita Zinthu Mogwirizana

Mfundo 3: Muzichita Zinthu Mogwirizana

Mfundo 3: Muzichita Zinthu Mogwirizana

“Awiri aposa mmodzi . . . Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake.”—Mlaliki 4:9, 10.

Mungachite bwanji? Kuti banja liziyenda bwino, mwamuna ndi mkazi safunika kunyalanyaza mfundo ya m’Baibulo yakuti mwamuna ndiye mutu wa banja. (Aefeso 5:22-24) Komabe, mufunika kuchita zinthu mogwirizana, m’malo moti aliyense azichita zake. Mwamuna ndi mkazi akamachita zinthu mogwirizana amasonyeza kuti iwo ndi “thupi limodzi.” Baibulo likamanena kuti mwamuna ndi mkazi wake ndi “thupi limodzi” limatanthauza kuti banjalo siliyenera kutha. Koma si zokhazo, limatanthauzanso kuti anthuwo ayenera kuchita zinthu mogwirizana.—Genesis 2:24.

Kufunika kwake. Ngati mwamuna ndi mkazi wake sagwirizana, mavuto ang’onoang’ono amakula. Ndipo zimenezi zingachititse kuti ayambe kulozana zala m’malo mothetsa vutolo. Mwamuna ndi mkazi amene amachita zinthu mogwirizana ali ngati woyendetsa ndege ndi womuthandiza wake amene akuyendetsa ndege mogwirizana. Koma banja losagwirizana lili ngati anthu awiri amene akuyendetsa ndege imodzi koma akuchita zosiyana, zomwe zingachititse ngozi. Mukasemphana maganizo pamafunika kupeza njira yothetsera vutolo, m’malo mowononga nthawi ndi kuimbana mlandu.

Yesani izi. Yankhani mafunso otsatirawa kuti mudziwe ngati inuyo mumaona kuti kuchita zinthu mogwirizana ndi mwamuna kapena mkazi wanu n’kofunika.

Kodi ndimaona ndalama zimene ndimalandira ngati zandekha chifukwa chakuti ndine amene ndimagwira ntchito?

Kodi ndimadana ndi achibale a mwamuna kapena mkazi wanga, ngakhale kuti iyeyo amagwirizana nawo kwambiri?

Kodi ndimasangalala kwambiri ndikakhala ndekha, osati pamene ndili ndi mwamuna kapena mkazi wanga?

Chitani izi. Ganizirani chinthu chimodzi kapena ziwiri zomwe zingakuthandizeni kuti mukhale ogwirizana.

Mungachite bwino kufunsa mkazi kapena mwamuna wanu kuti akuuzeni maganizo ake pankhaniyi.

[Chithunzi patsamba 5]

Mwamuna ndi mkazi amene amachita zinthu mogwirizana ali ngati woyendetsa ndege ndi womuthandiza wake amene akuyendetsa ndege mogwirizana