Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo 6: Muzikhululukirana

Mfundo 6: Muzikhululukirana

Mfundo 6: Muzikhululukirana

“Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana wina ndi mnzake ndi mtima wonse.”—Akolose 3:13.

Mungachite bwanji? Kuti banja liziyenda bwino, pamafunika kuphunzira pa zimene zakhala zikuchitika m’mbuyomu. Koma si bwino kusunga zinthu zimene munalakwirana kale n’cholinga chomupezera mnzanuyo zifukwa. Mwachitsanzo, si bwino kunena kuti, “Nthawi zonse umachedwa” kapena, “Nthawi zonse sumamvetsera.” Mwamuna ndi mkazi amafunika kuzindikira kuti ‘kukhululukirana’ kumabweretsa “ulemerero.”—Miyambo 19:11.

Kufunika kwake. Mulungu “ndi wokhululukira” ngakhale kuti anthu zimawavuta kuchitira ena chifundo. (Salmo 86:5) Ngati mwamuna ndi mkazi wake sakambirana akalakwirana, zolakwazo zimangounjikana ndipo zingavute kuti akhululukirane. Aliyense angamalephere kunena mmene akumvera mumtima mwake, ndipo sizingam’khudze ngati mnzake akufuna kulankhula naye. Ngati m’banja mulibe chikondi, mwamuna kapena mkazi angamaone kuti akupanikizika.

Yesani izi. Onani zithunzi zakale za mwamuna kapena mkazi wanu zimene munajambulitsa mutangokwatirana kumene kapena muli pachibwenzi. Yesetsani kukumbukira chikondi chimene munali nacho banja lanu lisanayambe kukumana ndi mavuto. Ganizirani makhalidwe abwino a mkazi kapena mwamuna wanu amene anakusangalatsani. Nanga panopa mumaona kuti mkazi kapena mwamuna wanu ali ndi makhalidwe abwino ati?

Kodi mkazi kapena mwamuna wanu ali ndi makhalidwe ati amene inuyo mumawasirira?

Ganizirani zinthu zabwino zimene ana anu angaphunzire kwa inu ngati mumakhululukira ena.

Chitani izi. Ganizirani chinthu chimodzi kapena ziwiri zimene zingakuthandizeni kuti musamaphatikize zolakwa zakale ndi zatsopano za mwamuna kapena mkazi wanu.

Mungachite bwino kuyamikira mkazi kapena mwamuna wanu chifukwa cha makhalidwe ake abwino.—Miyambo 31:28, 29.

Ganizirani zinthu zimene ana anu angachite zomwe mungafunike kuwakhululukira.

Mungachite bwino kukambirana ndi ana anu za kukhululuka ndiponso mmene kungathandizire ena m’banja lanu.

[Chithunzi patsamba 8]

Mukakhululukira ena, nkhani iyenera kuthera pomwepo ndipo simuyenera kuwakumbutsanso