Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo 7: Muzitsatira Malangizo Odalirika

Mfundo 7: Muzitsatira Malangizo Odalirika

Mfundo 7: Muzitsatira Malangizo Odalirika

Mungachite bwanji? Banja lili ngati nyumba. Kuti nyumba ikhale yolimba imafunika kumangidwa pamaziko abwino. Nalonso banja kuti likhale lolimba, mwamuna ndi mkazi wake amafunika kutsatira malangizo odalirika.

Kufunika kwake. Malangizo a m’banja akupezeka paliponse monga m’mabuku, m’magazini, ndiponso m’mapulogalamu a pa TV. Alangizi ena amauza anthu amene ali ndi mavuto a m’banja kuti asathetse ukwati wawo pamene ena amawauza kuti angothetsa ukwatiwo. Ndiponso akatswiri amasinthasintha maganizo awo. Mwachitsanzo m’chaka cha 1994, dokotala wina wotchuka, yemwe ndi katswiri pankhani za achinyamata, analemba kuti atangoyamba ntchito yake, ankaona kuti “ana amasangalalako banja likatha n’kumakhala ndi bambo kapena mayi okha kuyerekeza ndi kukhala ndi makolo onse awiri amene sagwirizana.” Iye anati: “Ndinkaganiza kuti kuthetsa banja ndi kwabwino kuyerekeza ndi kukhalabe m’banja lamavuto.” Koma patapita zaka ziwiri dokotalayu anasintha maganizo ake ndipo ananena kuti: “Ukwati ukatha ana amavutika kwambiri.”

Maganizo a anthu amatha kusintha, koma malangizo abwino kwambiri ayenera kugwirizana ndi mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Pamene mumawerenga nkhanizi mwina mwaona kuti mfundo ya m’Baibulo yalembedwa pamwamba, kuyambira tsamba 3 mpaka 8. Mfundo zimenezi zathandiza mabanja ambiri kuti aziyenda bwino. N’zoona kuti mabanja amenewa amakumananso ndi mavuto, komabe amayenda bwino chifukwa amatsatira malangizo odalirika a m’Baibulo. Malangizo a m’Baibulo ndi odalirika chifukwa Baibulo linalembedwa ndi Yehova Mulungu yemwenso anayambitsa banja.—2 Timoteyo 3:16, 17.

Yesani izi. Lembani penapake malemba amene ali pamwamba pa tsamba 3 mpaka 8. Mungawonjezerenso malemba ena amene akuthandizani. Asungeni kuti muziwagwiritsa ntchito.

Chitani izi. Yesetsani kutsatira mfundo za m’Baibulo m’banja lanu.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Kuti nyumba ikhale yolimba imafunika kumangidwa pamaziko abwino. Maziko abwino a banja ndi malangizo odalirika a m’Baibulo