Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

▪ “Atsikana oposa 30 pa 100 aliwonse ku United States amatenga mimba asanakwanitse zaka 20.”—CENTERS FOR DISEASE CONTROL AND PREVENTION, U.S.A.

▪ Akatswiri ena ku United States anachita kafukufuku wokhudza amuna 420 kuti aone ngati “amachitidwa nkhanza kunyumba kwawo.” Iwo anapeza kuti “pafupifupi amuna atatu pa 10 aliwonse, anamenyedwapo kapena kuchitidwa nkhanza inayake.”—AMERICAN JOURNAL OF PREVENTIVE MEDICINE.

Ana Angathe Kuphunzira Zilankhulo Zambiri

Makolo ambiri amaganiza kuti ngati ataphunzitsa ana awo chilankhulo china, anawo angamalephere kulankhula bwino chilankhulo cha makolo awo. Koma katswiri wina, dzina lake Laura-Ann Petitto, pamodzi ndi anzake ena anapanga kafukufuku ku Toronto, Canada ndipo anapeza kuti zimenezi si zoona. Iye anati: ‘Mwana akamabadwa ubongo wake umakhala ndi zonse zomuthandiza kuphunzira zilankhulo zambiri.’ Kusukulu, ana amene amalankhula zinenero ziwiri amakhoza bwino kuposa ana amene amalankhula chinenero chimodzi. Komabe, nyuzipepala ya Toronto Star, inanena kuti “makolo ndi amene ayenera kuchita khama kuphunzitsa ana awo chilankhulo china kuti anawo akhale ndi nzeru.”

Zithunzi Zolaula Zimasokoneza Ana

Ana ambiri amayamba kuonera zithunzi zolaula ndiponso masewera achiwawa a pa Intaneti ali aang’ono kwambiri. Heinz-Peter Meidinger, yemwe ndi mkulu wa bungwe lina lofufuza zilankhulo ku Germany, ananena kuti ana ambiri oyambira zaka 12 amadziwa kumene angapeze zithunzi zolaula kapena masewera achiwawa pa Intaneti. Ngakhale kuti anawo angaoneke kuti zimene akuonera sizikuwasokoneza, ana ambiri amasokonezedwa kwambiri. Meidinger analangiza makolo kuti ayenera kudziwa zimene ana awo akuganiza komanso zinthu zimene anawo akusunga mu kompyuta mwawo.

Kukonzekera Kuthetsa Banja

Nyuzipepala ya Sunday Telegraph ya ku Sydney inanena kuti anthu ambiri ku Australia amene akufuna kukwatira akumakambirana ndi munthu amene akufuna kudzakwatirana nayeyo za zinthu zimene ayenera kumadzachita akadzakwatirana. Poyamba anthu ankangokambirana za mmene angadzagawanirane katundu kapena ndalama banja lawo likadzatha, koma panopa akukambirananso za zinthu zimene mkazi kapena mwamuna ayenera kudzachita kuti banja lidzapitirire. Akumakambirananso za amene azidzaphika chakudya, kukonza m’nyumba, kuyendetsa galimoto, kukathamanga ndi agalu, kukataya zinyalala, ndiponso za makilogalamu amene mwamuna ndi mkazi ayenera kulemera. Katswiri wina wa zamalamulo, dzina lake Christine Jeffress, ananena kuti “anthu ambiri akukayika ngati ukwati wawo ungapitirire.”

Makolo Akufuna Malangizo Owathandiza Kukonda Ana Awo

Magazini ya Newsweek Polska ya ku Poland inati: “Makolo ambiri akufuna malangizo owathandiza kulera ana awo chifukwa zikuoneka kuti sadziwa mmene angakondere anawo.” Makolo afunika kuphunzitsidwa zinthu monga kukumbatira ana awo, kusewera nawo, ndi kuwaimbira nyimbo. Zinthu zimenezi n’zofunika kwambiri kuti ana akule bwino. Komabe, ofufuza apeza kuti “makolo a ku Poland amakonda kwambiri kuonera TV ndi ana awo, komanso kupita nawo kokagula zinthu.” Makolowa sakonda kusewera ndi ana awo.