Zimene Mukufuna Zili M’Baibulo
Zimene Mukufuna Zili M’Baibulo
▪ Mwamuna ndi mkazi wake omwe amalankhula Chifalansa ndipo ndi a Mboni za Yehova anapita m’dera lina mu mzinda wa Ajaccio, womwe uli pachilumba cha Corsica m’nyanja ya Mediterranean. Ali kumeneko, anatola envulopu imene inali ndi ndalama zokwana mayuro 400. Envulopuyi sinalembedwe dzina kapena adiresi. Mkaziyo anafotokoza kuti: “Tinalemba pa bolodi la chidziwitso kuti aliyense amene wataya envulopu angatiimbire foni.”
Madzulo a tsiku lotsatira, mayi wina anaimbira foni banjali. Iye anafotokoza zinthu zimene zinasonyeza kuti ndalamazo ndi zake ndipo anakonza ulendo wokakumana ndi banjali. Mayiyo anatenga maluwa okongola kuti akapatse banjali ngati mphatso, chifukwa sanamvetse kuti munthu angafune kubweza ndalama zambiri choncho. Envulopu imene anatayayo munali malipiro ake, ndipo tsiku lotsatira amayembekezera kupita ku tchuthi.
Mayiyo atapita ku tchuthi, anatumiza kadi lothokoza banjali chifukwa cha mtima wawo wabwino. Ndipo atabwera ku tchuthi, banja la Mboni lija linapita kukacheza kunyumba kwake. Iwo anafotokozera mayiyo ubwino wotsatira mfundo za m’Baibulo m’banja komanso pa zochita zathu za tsiku ndi tsiku. Mayiyo anachita chidwi kwambiri ndi nkhani imeneyi.
Pogwiritsa ntchito buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? banjali linayamba kukambirana ndi mayiyo mfundo zingapo kuchokera pa mutu wakuti “Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Likhale ndi Moyo Wosangalala.” Mayiyo anasangalala kwambiri ndi zimene anaphunzira, ndipo ananena mokuwa kuti: “Sindimadziwa kuti zonse zimene ndimafuna zili m’Baibulo!” Kenako iye anavomera kuti azimuphunzitsa Baibulo.
Kuwonjezera pa nkhani yokhudza banja, buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani limafotokozanso zoona zenizeni pankhani ya Mulungu ndi Yesu Khristu. Limafotokozanso chimene chimachitika munthu akafa, chifukwa chake Mulungu amalola kuti anthu azivutika ndi nkhani zina zofunika. Mukhoza kuitanitsa bukuli polemba adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera pa tsamba 5 la magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire buku limene lasonyezedwa panoli.
□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.