Zipangizo Zamakono Zikuchuluka Masiku Ano
Zipangizo Zamakono Zikuchuluka Masiku Ano
KU Albania si zachilendo kuona munthu wokalamba atakwera bulu, kwinaku akulankhula pa foni yam’manja. Ndipo ku India, si zachilendo kuona munthu wopemphetsa akusiya kaye kupemphetsako kuti aimbe kapena kuyankha foni. Masiku ano zipangizo zamakono monga mafoni am’manja, makompyuta ndiponso TV zikupezeka ndi aliyense, kaya wolemera kapena wosauka, ndipo anthu ambiri sangathe kukhala opanda zipangizo zimenezi.
Pa zipangizo zimenezi, mafoni am’manja ndi amene achuluka kwambiri ndipo ambiri mwa mafoniwa si mafoni wamba. Mwachitsanzo, pogwiritsa ntchito mafoni am’manja, munthu angathe kufufuza zinthu pa Intaneti, kutumiza ndi kulandirira mauthenga, kuonera TV, kumvetsera nyimbo, kujambula zithunzi, kufufuza malo amene akufuna kupita, ndiponso kuimba foni kumene.
Malinga ndi nyuzipepala ya Washington Post, masiku ano pali mafoni ena “amphamvu kwambiri kuposa makompyuta omwe asilikali a ku United States ndi Canada ankagwiritsa ntchito mu 1965.” Nyuzipepalayi inanenanso kuti: “Chiwerengero cha mafoni am’manja padziko lonse n’chachikulu kuwirikiza kawiri chiwerengero cha anthu,” ndipo m’mayiko ena 30, chiwerengero cha mafoni am’manja n’chachikulu kwambiri kuposa cha anthu. Nyuzipepalayi inanenanso kuti “palibe chipangizo china chomwe chafala kwambiri padziko lonse m’kanthawi kochepa kuposa foni yam’manja.”
Padziko lonse, anthu 60 pa 100 aliwonse amene ali ndi mafoni am’manja amakhala m’mayiko amene akungotukuka kumene. Zimenezi zikusonyeza kuti mafoni am’manja ndi chipangizo choyamba kugwiritsidwa ntchito kwambiri m’mayiko amenewa kuposa zipangizo zina zonse zimene zatuluka m’mbuyomu. Mwachitsanzo, ku Afghanistan chiwerengero cha anthu okhala ndi mafoni am’manja chinkawonjezereka ndi 140,000 mwezi uliwonse m’chaka cha 2008. Ndipo ku Africa, chiwerengero cha anthu omwe ali ndi mafoni am’manja chakhala chikuwonjezereka ndi 50 peresenti chaka chilichonse.
Koma kupita patsogolo ndiponso kufala kwa zipangizo zamakono zotumizira mauthenga kulinso ndi mavuto ake. Mafoni am’manja, mapeja, ndi makompyuta amachititsa kuti anthu azitha kutumizirana uthenga kapena kulankhulana nthawi ina iliyonse. Choncho ena amaona kuti zimenezi zimawasokoneza. Komanso ena amangokhalira kulankhula pafoni kapena kugwiritsa ntchito Intaneti n’cholinga choti azidziwa zimene zikuchitika, zomwe zimawawonongera nthawi yambiri.
Mavuto ambiri amene abwera chifukwa cha zipangizo zamakono zotumizira mauthenga ndi monga kusokonezedwa ndi anthu ena poimbiridwa foni nthawi ina iliyonse, kapena kulephera kukhala popanda kugwiritsa ntchito zipangizozi. * Komabe, zipangizozi zilinso ndi ubwino wake. Ndiyeno kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito zipangizozi mwanzeru? Nkhani zotsatirazi ziyankha funso limeneli.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 M’nkhanizi tikufotokoza kwambiri za mafoni am’manja, makompyuta, TV ndi Intaneti. Choncho, mawu akuti “zipangizo zamakono” akunena za zinthu zimenezi.