Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungathetse Bwanji Njala Yanu Yauzimu?

Kodi Mungathetse Bwanji Njala Yanu Yauzimu?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mungathetse Bwanji Njala Yanu Yauzimu?

MWACHIBADWA, anthufe timamva njala ya chakudya chauzimu mofanana ndi mmene timamvera njala ya chakudya chakuthupi. Pankhani ya chakudya chakuthupi, pali zakudya zabwino zambirimbiri zimene tingasankhe. Koma kodi zimenezi n’zofanana ndi chakudya chauzimu? Pali miyambo yambiri ya chikhalidwe komanso ya chipembedzo imene anthu amanena kuti ingatithandize kuthetsa njala yathu yauzimu.

Anthu ambiri amaona kuti ngati munthu amachita zinthu zauzimu, zilibe kanthu kaya munthuyo amakhulupirira zotani kapena amalambira Mulungu motani. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi njira iliyonse yothetsera njala yathu yauzimu ndi yovomerezeka? Kodi Baibulo limati chiyani pankhani imeneyi?

Kodi Munthu Wauzimu Amakhala Wotani?

Palemba la Genesis 1:27, Baibulo limafotokoza chifukwa chake anthufe timakhala ndi njala yauzimu. Lembali limati: “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adam’lenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” Popeza kuti Yehova Mulungu ndi mzimu, anthufe timafanana ndi Mulungu mwa makhalidwe osati mwa maonekedwe. Mofanana ndi Mlengi wake, munthu woyamba, Adamu, akanatha kukhala ndi makhalidwe monga chikondi, kukoma mtima, chifundo, chilungamo ndiponso kudziletsa. Iye anapatsidwanso chikumbumtima n’cholinga choti azisankha zinthu mwaufulu koma mogwirizana ndi malamulo a Mulungu. Choncho, anthu analengedwa mosiyana ndi nyama ndipo akhoza kuchita zinthu zimene Mlengi wawo amafuna.—Genesis 1:28; Aroma 2:14.

Baibulo limafotokoza chinthu chofunikira kwambiri chimene chingatithandize kukhala anthu auzimu. Palemba la 1 Akorinto 2:12-15, Baibulo limafotokoza kuti munthu wauzimu amakhala ndi mzimu wochokera kwa Mulungu. Mzimu umenewu ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito ndipo mphamvu imeneyi ndi imene imatithandiza kudziwa zinthu zauzimu. Imathandiza anthu kufufuza ndi kumvetsa zinthu malinga ndi mmene Mulungu amazionera. Koma munthu amene alibe mzimu wa Mulungu amatchedwa munthu wakuthupi, ndipo munthu wotere amaona zinthu zauzimu ngati zosafunikira. Pachifukwa chimenechi, iye sadziwa zambiri.

Choncho, ngakhale kuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu, sitingakhale anthu auzimu mwa kudzidziwa tokha, kuphunzira kwambiri, kapena kupeza zinthu zimene timafuna pamoyo wathu. Kuti tikhale anthu auzimu, tifunika kutsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Ndipotu anthu amene safuna kutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu ndipo amatsatira zofuna za thupi lawo ndiponso zinthu zimene Mulungu amadana nazo, amatchedwa anthu akuthupi.—1 Akorinto 2:14; Yuda 18, 19.

Mmene Mungapezere Zosowa Zanu Zauzimu

Kuti tithetse njala yathu yauzimu, choyamba tiyenera kuzindikira kuti Yehova ndi Mlengi wathu. (Chivumbulutso 4:11) Kenako tiyenera kuzindikira kuti moyo wathu sungakhale ndi cholinga pokhapokha ngati tikuchita chifuniro cha Mulungu. (Salmo 115:1) Kuchita chifuniro cha Mulungu kumatithandiza kuti tikhale ndi moyo wosangalala, mofanana ndi mmene timasangalalira tikadya chakudya. N’chifukwa chake Yesu, yemwe ankakonda kwambiri zinthu zauzimu, ananena kuti: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha iye amene anandituma ine.” (Yohane 4:34) Kuchita chifuniro cha Mulungu kunkamupatsa mphamvu, ndipo kunkamuthandiza kukhala wosangalala.

Popeza kuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu, kuti tikhale okhutira ndi moyo wathu wauzimu tiyenera kukhala ndi makhalidwe ogwirizana ndi a Mulungu. (Akolose 3:10) Ndipo tiyenera kupewa khalidwe limene lingatichotsere ulemu kapena kuwononga ubwenzi wathu ndi iye. (Aefeso 4:24-32) Kutsatira malamulo a Mulungu kumatithandiza kukhala ndi khalidwe labwino komanso mtendere wa m’maganizo, chifukwa timakhala ndi chikumbumtima chabwino.—Aroma 2:15.

Yesu ananenanso chinthu china chofunika kwambiri chimene chingatithandize kuthetsa njala yathu yauzimu. Iye anati: “Munthu asakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mateyo 4:4) Nthawi zonse tifunika kuonetsetsa kuti tikulimbikira kuchita zinthu zauzimu. Kudzera m’Baibulo, Yehova amayankha mafunso okhudza moyo amene anthu ambiri amakhala nawo.—2 Timoteyo 3:16, 17.

Zimene Mungachite Kuti Mukhale ndi Moyo Wosangalala

N’zotheka munthu kuthetsa njala podya chakudya chokoma koma chosapatsa thanzi. Choncho, ifenso tingachite zinthu kapena kuphunzira zinthu zomwe ena amaganiza kuti zingathetse njala yathu yauzimu koma zili zosathandiza kwenikweni. Chakudya chosapatsa thanzi chingachititse munthu kuyamba kutupikana, kudwala kapena kufa kumene. N’chimodzimodzinso ndi zinthu zauzimu. Kulephera kudya chakudya chauzimu choyenera n’koopsa kwambiri.

Koma ngati titapanga ubwenzi wolimba ndi Yehova Mulungu, n’kumayesetsa kutsatira malamulo ake, tidzazindikira kuti Baibulo limanena zoona pamene limati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyo 5:3.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi n’chifukwa chiyani anthufe timakhala ndi njala ya zinthu zauzimu?—Genesis 1:27.

▪ Kodi n’zotheka kuthetsa njala yathu yauzimu patokha?—1 Akorinto 2:12-15.

▪ Kodi tingatani kuti tithetse njala yathu yauzimu?—Mateyo 4:4; Yohane 4:34; Akolose 3:10.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

Kulephera kudya chakudya chauzimu choyenera n’koopsa kwambiri