Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhula Momasuka ndi Makolo Anga?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhula Momasuka ndi Makolo Anga?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhula Momasuka ndi Makolo Anga?

“Ndinkayesetsa kwambiri kufotokozera makolo maganizo anga pankhani inayake, koma ankangondidula mawu. Zinali zovuta kwambiri kuti ndilimbe mtima n’kuwauza mmene ndikumvera, koma ngakhale nditayesetsa sizinkathandiza ngakhale pang’ono.”—Rosa. *

N’KUTHEKA kuti muli mwana, munkakonda kufunsira nzeru kwa makolo anu. Munkawauza chilichonse, ndi nkhani yaing’ono yomwe. Munkawafotokozera momasuka zakukhosi kwanu ndipo munkaona kuti malangizo awo ndi othandiza.

Koma mwina masiku ano mumaona kuti iwo samakumvetsetsani. Mtsikana wina, dzina lake Edie, anati: “Tsiku lina tikudya chakudya chamadzulo, ndinayamba kulira kwinaku ndikufotokoza maganizo anga. Makolo anga ankaoneka ngati akumvetsera, koma sankandimvetsetsa.” Mtsikanayu anapitiriza kuti: “Kenako ndinangopita kuchipinda changa n’kukapitiriza kulira.”

Mwina mumaonanso kuti ndi bwino kubisira makolo anu nkhani zina. Mnyamata wina, dzina lake Christopher, anati: “Ndimauza makolo anga nkhani zambiri, koma ndimaona kuti ndi bwino asamadziwe chilichonse chimene ndikuganiza.”

Kodi n’kulakwa kubisira makolo anu nkhani zina? Nthawi zina sikulakwa, makamaka ngati zimene mukubisazo si zolakwika. (Miyambo 3:32) Komabe, kaya makolo anu amaoneka kuti sakumvetsetsani kapena safuna kulankhula nanu, dziwani mfundo iyi: Mufunika kumalankhula ndi makolo anu ndipo iwo amafunika kudziwa maganizo anu.

Musaleke Kulankhula Nawo

Kulankhula ndi makolo anu tingakuyerekezere ndi kuyendetsa galimoto. Ngati mutapeza chikwangwani chosonyeza kuti msewu watsekedwa, simungabwerere koma mukhoza kungodzera msewu wina. Taganizirani chitsanzo chili pamwambachi komanso patsamba 20.

Vuto Loyamba: Inuyo mukufuna kulankhula ndi makolo anu, koma iwo akuoneka kuti sakufuna. Mtsikana wina dzina lake Leah anati: “Zimandivuta kulankhulana ndi bambo anga. Nthawi zina ndikalankhula nawo kwa kanthawi, amanena kuti, ‘Pepa, kodi umalankhula ndi ine?’”

FUNSO: Kodi Leah angatani ngati akufuna kuwauza vuto linalake? Iye angatsatire imodzi mwa njira zitatu izi:

Njira Yoyamba Njira Yachiwiri Njira Yachitatu

Kuwalusira bambo Kusiya kulankhula Kudikira kaye

akewo. Leah akhoza ndi bambo akewo. n’kudzawauza nkhaniyo

kunena mokalipa Leah akhoza nthawi ina. Leah

kuti, “Tamvetserani, kungosiya kuuza angalankhule ndi bambo

ndikufuna ndikuuzeni makolo ake mavuto akewo pamasom’pamaso

zinthu zofunika.” amene akukumana kapena angawalembere

nawo. kalata yofotokoza za

vuto lake.

Kodi mukuganiza kuti njira yabwino yomwe Leah angasankhe ndi iti? ․․․․․

Tiyeni tiganizire njira zonsezi kuti tione zotsatira zake. Bambo a Leah akuganiza zinthu zina ndipo sakudziwa kuti mwana wawoyo wakhumudwa. Choncho Leah atasankha Njira Yoyamba, iwo sangadziwe chifukwa chimene mwana wawoyo walusira. Ndipo kuchita zimenezi sikungapangitse bambo akewo kugwirizana ndi maganizo ake. Komanso zingasonyeze kuti salemekeza makolo ake. (Aefeso 6:2) Choncho, njira imeneyi singathandize ngakhale pang’ono.

Pamene Njira Yachiwiri ingakhale yosavuta koma si yanzeru. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti “zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.” (Miyambo 15:22) Kuti athandizidwe pa vuto lake, Leah afunika kulankhula ndi makolo ake, koma n’zovuta kumuthandiza ngati iwo sakudziwa zimene zikumuchitikira pamoyo wake. Choncho, kusiya kulankhula nawo n’kosathandiza.

Koma potsatira Njira Yachitatu, Leah sakulola kuti kusamvetsera kwa bambo ake kumupangitse kuti asalankhule nawonso. M’malomwake iye wasankha kulankhula nawo panthawi ina. Ndipo kulembera kalata bambo akewo kungamuthandize kumva bwino. Komanso iye angalembe ndendende zimene angauze bambo akewo atakhala kuti akumvetsera. Iwo atawerenga kalatayo angadziwe zimene mwana wawo amafuna kuwauza, zomwe zingachititse kuti amvetse vuto lakelo. Choncho njira yachitatuyi ingathandize Leah komanso bambo ake.

Kodi pali njira inanso imene Leah angatsatire? Yesani kuganizira njira imodzi ndipo lembani njirayo m’munsimu. Kenako lembani zimene zingachitike atatsatira njira imeneyi.

․․․․․

Vuto Lachiwiri: Makolo anu akufuna kulankhula nanu koma inuyo simukufuna. Mtsikana wina, dzina lake Sarah, anati: “Palibe chimandipweteka kuposa kufunsidwa mafunso ambirimbiri pambuyo pakuti ndatopa ndi za kusukulu. Ndikufuna nditaiwalako za kusukulu, koma nthawi yomweyo makolo akuyamba kundifunsa kuti, ‘Zinali bwanji kusukulu? Unakumana ndi vuto lililonse?’” Makolo a Sarah ayenera kuti amafunsa mafunso amenewa chifukwa chomukonda. Koma iye akudandaula kuti, “Sindimafuna kulankhula za sukulu nditatopa.”

FUNSO: Kodi Sarah angatani? Mofanana ndi chitsanzo choyamba chija, iye angatsatire imodzi mwa njira zitatu izi:

Njira Yoyamba Njira Yachiwiri Njira Yachitatu

Kukana kulankhula Kulankhula nawobe. Kusiya kulankhula

nawo. Iye anganene Ngakhale kuti za kusukulu koma

kuti: “Bwanji watopa, Sarah n’kuyambitsa nkhani

mundisiye kaye? angalankhule ina. Sarah angapemphe

Sindikufuna nawobe makolo makolo ake kuti

kulankhula ndi akewo koma akambirane nawo za

munthu aliyense mokakamizika. kusukulu nthawi ina

panopa.” yomwe akuona kuti

ingakhale yabwino kwa

iyeyo. Kenako, Sarah

anganene mochokera

pansi pa mtima kuti:

“Zinthu zinali bwanji

pakhomo pano?”

Kodi mukuganiza kuti njira yomwe ingathandize Sarah ndi iti? ․․․․․

Tiyeni tiganizirenso njira zonsezi kuti tione zotsatira zake.

Sarah asanasankhe Njira Yoyamba, ankaona kuti ali ndi mantha ndipo sankafuna kulankhula. Atasankha njirayi, angakhalebe ndi mantha, koma angamadzimve kuti walakwa powalusira makolo akewo.—Miyambo 29:11.

Makolo a Sarah angakhumudwe kuona mwana wawo atawalusira kapena kumuona atasiya kulankhula nawo. Iwo angaganize kuti iye akuwabisira chinachake. Ndipo angayesetse kwambiri kuti mwana wawoyo amasuke kulankhula zimene zili kukhosi kwake, zomwe zingachititse kuti iye akhumudwe kwambiri. Motero, njira imeneyi siingathandize makolowo komanso mwanayo.

Njira Yachiwiri ndi yabwinopo kuyerekeza ndi Njira Yoyamba. Tikutero chifukwa onse akulankhulana. Komabe, kulankhulana kwawo n’kosathandiza chifukwa akungolankhula modzikakamiza.

Koma Njira Yachitatu, ndi yothandiza chifukwa Sarah ayamba wasiya kaye nkhani ya sukulu. Ndipo makolo ake angasangalale kwambiri kuti wayesetsa kulankhula nawo. Njira imeneyi ingathandize kwambiri chifukwa aliyense akuyesetsa kutsatira mfundo ya pa Afilipi 2:4 yakuti: “Musasamale zofuna zanu zokha, koma musamalenso zofuna za ena.”

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha mayina ena.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi kudziwa nthawi yoyenera kulankhulana kungathandize bwanji?—Miyambo 25:11.

▪ Kodi kuyesetsa kulankhulana ndi makolo anu n’kofunika chifukwa chiyani?—Yobu 12:12.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]

KODI MUKULEPHERA KUMVETSETSANA?

Kodi zikukuvutani kulankhulana ndi makolo anu? N’kutheka kuti samvetsetsa zimene mukufuna.

Inu mukanena kuti . . .

“Sindikufunanso kulankhula nkhani imeneyi.”

Makolo anu akuganiza kuti mwanena kuti  . . .

“Ndikakhala ndi nkhani ndiziuza anzanga, inuyo si oyenera kuti ndizikuuzani zakukhosi kwanga.”

Inu mukanena kuti . . .

“Simungandimvetse.”

Makolo anu akuganiza kuti mwanena kuti  . . .

“Inuyo mwakalamba ndipo mumaganiza mwachikale. Simungamvetse zimene ndikufuna pamoyo wanga.”

[Bokosi/Zithunzi patsamba 21]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

“Ndinauza makolo anga za vuto limene ndinkakumana nalo kusukulu, ndipo ndinadabwa kuona kuti ankamvetsera mwachidwi. Chifukwa cha thandizo lawo, vutolo ndinalithetsa mosavuta.”—Natalie.

“Kulankhulana ndi makolo kumavuta nthawi zina, koma ukalimba mtima n’kulankhula nawo, umapepukidwa kwambiri.”—Devenye.

[Bokosi patsamba 21]

MAWU KWA MAKOLO

Mwina inunso mumaona kuti ana anu zimawavuta kulankhula nanu. Taganizirani zimene achinyamata ena anauza olemba Galamukani! atafunsidwa kuti afotokoze zomwe zimawalepheretsa kulankhula ndi makolo awo. Kenako, dzifunseni mafunso amene ali mbali inayo ndipo werengani malembawo.

Zimandivuta kulankhula ndi bambo anga chifukwa amatanganidwa kwambiri kuntchito komanso kumpingo. Zimaoneka kuti sakhala ndi mpata woti ndingalankhule nawo.—Andrew.

‘Kodi nthawi zina ndimachita zinthu zosonyeza kuti ndilibe nthawi yolankhula ndi ana anga? Ngati ndimachita zimenezi, kodi ndingatani kuti ana anga azimasuka nane? Nanga ndingasankhe nthawi yanji yoti ndizicheza nawo?’—Deuteronomo 6:7.

Ndinauza mayi anga kwinaku ndikulira kuti kusukulu ndakangana ndi winawake. Ndinkafunitsitsa kuti mayi anga anditonthoze koma m’malomwake anangondikalipira. Kuyambira nthawi imeneyi sindimawauzanso nkhani iliyonse.”—Kenji

‘Kodi ndimatani ana anga akafuna kuti ndiwathandize vuto linalake? Ngakhale patafunika kuwalangiza, kodi sindingachite bwino kumawamvetsera kaye ndisanawapatse malangizo?’—Yakobe 1:19.

Zimaoneka kuti nthawi iliyonse imene makolo auza mwana wawo kuti sakhumudwa iye akawauza nkhani inayake, makolowo amakhumudwabe. Zikatero, mwanayo amaona kuti makolo akewo amunamiza.”—Rachel.

‘Ngati mwana wanga wandiuza nkhani inayake yomwe yandikhumudwitsa, kodi ndingachite chiyani kuti asadziwe zoti ndakhumudwa?’—Miyambo 10:19.

Nthawi zambiri ndinkati ndikawauza mayi nkhani inayake yachinsinsi, nthawi yomweyo ankauza anzawo. Zimenezi zinachititsa kuti papite nthawi ndisakuwakhulupirira.—Chantelle.

‘Kodi ndimasonyeza kuti ndimamulemekeza mwana wanga popewa kufalitsa nkhani zachinsinsi zimene wandiuza?’—Miyambo 25:9.

Pali zinthu zambiri zimene ndikufuna kukambirana ndi makolo anga. Ndikungoyembekezera kuti iwowo ayambitse kukambiranako.—Courtney.

‘Kodi sizingakhale bwino ngati ineyo nditayambitsa kukambirana ndi mwana wanga? Kodi nthawi yabwino kukambirana ndi iti?’—Mlaliki 3:7.

[Chithunzi patsamba 19]

Ngati njira yoyamba yolankhulirana ndi makolo anu sinathandize, pezani njira ina