Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa Kapena Zinangokhalapo Zokha?
Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa Kapena Zinangokhalapo Zokha?
M’chaka cha 1802, m’busa wina wa ku England, dzina lake William Paley, anafotokoza mwatsatanetsatane zinthu zimene zimam’pangitsa kukhulupirira kuti kuli Mlengi. Iye ananena kuti atakhala kuti akudutsa m’munda n’kupeza mwala, angaganize kuti mwalawo unafikapo wokha. Koma ngati atapeza wotchi, sangaganize kuti inafikapo yokha. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti wotchi ili ndi tizipangizo tosonyeza kuti inachita kupangidwa ndi winawake amene anali ndi cholinga poipanga.
MFUNDO za Paley zinakhudza kwambiri wasayansi wina wa ku England, dzina lake Charles Darwin. Komabe kenako, mosiyana ndi zimene Paley ankanena, Darwin anayamba kunena kuti zamoyo zinachita kusintha pang’onopang’ono kuchokera ku mtundu wina wa zamoyo. Mfundo za Darwin zinachititsa anthu ambiri kusiya kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa.
Kuchokera nthawi ya Paley ndi Darwin, anthu alemba mabuku ambiri okhudza nkhaniyi. Ena akhala akunena kuti zinthu zimene timaziona zinachita kulengedwa, pamene ena amanena kuti zinachita kusintha pang’onopang’ono kuchokera ku zinthu zina. Mfundo ziwiri zonsezi zakhala zikusinthidwa mwina ndi mwina ndipo zachititsa anthu ena kukhulupirira kuti moyo uli ndi cholinga ndiponso
ena kukhulupirira kuti moyo ulibe cholinga. Zimene inuyo mumakhulupirira pa nkhaniyi zingachititse kuti muziona moyo wanu kukhala wofunika kapena ayi. N’chifukwa chiyani tikutero?Mfundo za Darwin N’zosathandiza
Mfundo za Darwin zachititsa anthu ambiri kuyamba kuona kuti moyo wawo ulibe cholinga chenicheni. Iwo amaona kuti ngati dziko komanso zinthu zonse zimene zili m’dzikoli zinangokhalapo mwangozi, bwenzi moyo ulibe cholinga chenicheni. Wasayansi wina amene analandirapo mphoto ya Nobel, dzina lake Jacques Monod, anati: “Tsopano anthu azindikira kuti anangokhalapo mwangozi padzikoli, ndipo palibe aliyense wowasamalira. Iwo samadziwa kuti moyo wawo ukuchokera kuti kapena ukulowera kuti.”
Pulofesa wina wa pa yunivesite ya Lincoln ku Oxford, dzina lake Peter William Atkins, ananena zofanana ndi zimenezi. Iye anati: “Ndimaona kuti chilengedwe n’chachikulu komanso chokongola mogometsa. Koma kukula ndiponso kukongola kwake n’kopanda phindu.”
Koma dziwani kuti pali asayansi ena amene sagwirizana ndi maganizo amenewa, ndipo iwo ali ndi zifukwa zomveka zochitira zimenezi.
Umboni Woti Zinthu Zinachita Kulengedwa
Asayansi ambiri akaunika malamulo a m’chilengedwe amaona kuti n’zosatheka kuti zinthu za m’chilengedwe zingokhalapo zokha. Mwachitsanzo, iwo amachita chidwi ndi mphamvu zimene zimachititsa kuti zinthu zam’chilengedwe ziziyenda mwadongosolo. Malamulo amene mphamvu zimenezi zimayendera amaoneka kuti anakonzedwa bwino n’cholinga choti padzikoli pakhale zamoyo. Paul Davies, yemwe ndi katswiri wa zinthu zakuthambo, ananena kuti: “Kusintha malamulo amenewa, ngakhale pang’ono chabe, kungachititse kuti padzikoli pasakhalenso zamoyo.” Mwachitsanzo, mapulotoni amakhala opepuka poyerekeza ndi manyutuloni, koma ngati atakhala olemera kuposa manyutuloni, ndiye kuti mapulotoni onse angasinthe n’kukhala manyutuloni. Kodi zimenezi zingakhale ndi vuto lotani? Davies anati: “Popanda mapulotoni, sipangakhalenso maatomu amene amapanga zinthu zimene timaziona.”
Pali mphamvu inayake mu atomu imene imachititsa kuti maelekituloni azikokedwa ndi mapulotoni, ndipo zimenezi zimachititsa kuti mamolekyu apangidwe. Mphamvu imeneyi ikanakhala yocheperapo, sibwenzi atomu ikukhala ndi maelekituloni, ndipo zimenezi zikanachititsa kuti mamolekyu asamapangidwe. Komanso ngati mphamvu imeneyi ikanakhala yochulukirapo, bwenzi maelekituloni akukokedwa n’kukhala pakati penipeni pa atomu. Zimenezi zikanachititsa kuti makemiko osiyanasiyana asamapangidwe. Choncho, sibwenzi tili ndi moyo chifukwa thupi lathu limadalira makemiko amenewa.
Komanso ngati mphamvu ya mu atomu itasinthidwa, ngakhale pang’ono chabe, zingachepetse kwambiri kapena kuwonjezera kwambiri mphamvu ya dzuwa imene imafika padziko lapansi. Ndipo zimenezi zingachititse kuti zomera zizilephera kupanga chakudya chawo. Choncho, mlingo woyenerera wa mphamvu imene imakhala mu atomu umachititsa kuti padzikoli pakhale zamoyo.Buku lina la sayansi (Science & Christianity—Four Views) linafotokoza mochititsa chidwi mmene mphamvu komanso zinthu zina za m’chilengedwe zinalinganizidwira bwino. Wolemba bukuli anapempha owerenga kuti ayerekezere kuti akuona katswiri wofufuza ali “m’chipinda chimene amachunira mphamvu zonse za m’chilengedwe.” Wofufuzayo akuona zopotokorera zambirimbiri zimene angathe kuzisintha mmene akufunira. Kenako iye akuzindikira kuti zopotokorerazo ziyenera kuchunidwa bwinobwino kuti padziko pakhale zamoyo. Chopotokorera chimodzi ndi cha mphamvu yokoka ya dziko, china ndi cha mphamvu yokoka ya mu atomu, china ndi chosinthira kulemera kwa manyutuloni ndi mapulotoni, ndiponso pali zopotokorera zina zambiri. Pamene wofufuzayo akuonetsetsa zopotokorerazi, akuzindikira kuti zinali zotheka kuzichuna mosiyana ndi mmene zilili. Koma kenako atapanga masamu akuona kuti kungosintha pang’ono ngakhale chopotokorera chimodzi chokha, zinthu zambiri m’chilengedwe zikhoza kusokonekera moti zamoyo zonse zingafe. Komano chopotokorera chilichonse anachichuna bwino kwambiri kuti zinthu zonse za m’chilengedwe zizichitika mwadongosolo komanso kuti padzikoli pakhale zamoyo. Kodi munthuyu angaganize kuti zopotokorerazi zinangochunika mwangozi, kapena alipo anazichuna?
Wasayansi wina wa zinthu zakuthambo, dzina lake George Greenstein, anati: “Tikaunika umboni
wonse womwe ulipo, timaona kuti pali chinachake kapena winawake wanzeru amene anachuna zinthu zimenezi. Kodi zimenezi sizingatichititse kuganiza kuti tapeza umboni wa sayansi wotsimikizira kuti kuli Mlengi?”Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinthu zimenezi zinangochitika mwangozi kapena winawake anachita kuzichuna?
Kodi ‘Zinangochitika Kuti Tili ndi Moyo’?
Anthu amene sakhulupirira kuti kuli Mulungu ali ndi mfundo zawo. Ena amaona kuti kuchunidwa bwino kwa zinthu za m’chilengedwe si umboni woti kuli Mlengi. Iwo amati: ‘N’zoona kuti zinthu za m’chilengedwe zimathandiza kuti tikhale ndi moyo, komabe zikanapanda kulinganizidwa mmene zililimu sitikanadandaula chifukwa sitikanakhala ndi moyo. Choncho, kuchunidwa bwino kwa zinthu si nkhani chifukwa zinangochitika kuti tili ndi moyo.’ Koma kodi inuyo mukuona kuti mfundo imeneyi ndi yomveka?
Anthu amene sakhulupirira kuti kuli Mlengi amanenanso kuti nthawi ina anthu adzazindikira kuti pali kachunidwe kamodzi kokha ka malamulo a m’chilengedwe kamene kamagwira ntchito. Zimenezi zikutanthauza kuti zopotokorera zonse zinayenera kuchunidwa moyenera, apo ayi dzikoli silikanakhalapo n’komwe. Ena amati, ‘Kungoti ndi mmene zinayenera kukhalira basi ndipo panalibenso njira ina yochunira malamulowa.’ Ngakhale maganizo amenewa akanakhala kuti ndi oona, sakufotokoza momveka chifukwa chake tili ndi moyo. Mwachidule, iwo amaganiza kuti zinangochitika mwangozi kuti dziko likhalepo komanso kuti dzikolo likhale ndi zinthu zothandiza kuti pakhale zamoyo. Koma kodi zimenezi n’zoona?
Anthu ena ali ndi njira ina yofotokozera kuti zinangochitika kuti mphamvu za m’chilengedwe zinachunidwa bwino. Iwo amanena kuti palinso zilengedwe zina kuwonjezera pa chomwe timachidziwachi. Malinga ndi zimene anthuwa amanena, chilengedwe chimene timaonachi ndi chimodzi mwa zilengedwe zambirimbiri zimene zilipo. Zilengedwe zonsezi ndi zosiyanasiyana koma zonse zinangokhalapo mwangozi. Choncho,
malinga ndi maganizo amenewa komanso malamulo a masamu okhudza zinthu zongochitika mwamwayi, ngati pali zilengedwe zambirimbiri, n’zotheka kuti chilengedwe chimodzi chikhale ndi zonse zofunikira kuti pakhale zamoyo. Komabe palibe umboni uliwonse wa sayansi wotsimikizira kuti pali zilengedwe zambirimbiri.Atafotokoza kuti sakugwirizana ndi maganizo amenewa, wasayansi wina amene anapatsidwapo mphoto ya Nobel, dzina lake Christian de Duve, anati: “Ndikuona kuti kaya pali zilengedwe zina zambiri kapena ayi, zomwe zilibe zinthu zofunikira kuti pakhale zamoyo, ubongo ndiponso moyo wa munthu ndi zodabwitsa ndipo ziyenera kuti zinachita kupangidwa ndi winawake. Mfundo yakuti pali zilengedwe zina zambiri siingatipangitse kuona chilengedwe chathuchi mopepuka. Zimene ndimaona m’chilengedwechi zimanditsimikizira kuti alipo anazipanga.”
Ubongo wa Munthu
Anthufe tili ndi nzeru zodabwitsa zotha kufotokoza zinthu zosiyanasiyana zokhudza mmene chilengedwe chinakhalira. Ngati chilengedwe chinakhalapo mwangozi, ndiye kuti nzeru zimenezi zinakhalaponso mwangozi. Kodi inuyo mukuona kuti mfundo imeneyi ndi yomveka?
Akatswiri amafotokoza kuti ubongo wa munthu “ndi wodabwitsa kwambiri komanso wovuta kuulongosola kuposa zinthu zina zonse za m’chilengedwe.” Ngakhale luso la sayansi litapita patsogolo motani, n’zosatheka kufotokoza momveka bwino chimene chimachititsa anthu kukhala ndi nzeru zodabwitsa komanso chidwi chofuna kudziwa cholinga cha moyo.
Kodi kwa inuyo mfundo yomveka ndi iti pakati pa mfundo yakuti ubongo wa munthu, kuphatikizapo chidwi chofuna kudziwa zinthu, zinapangidwa ndi munthu winawake wanzeru, kapena yakuti zinangokhalapo mwangozi?
Kodi Ndani Angatiuze Zolondola?
N’zoona kuti sayansi yatiphunzitsa zambiri zokhudza mmene zinthu zakuthambo, zapadziko lapansi komanso zamoyo, zimagwirira ntchito. Koma anthu ena amaona kuti akamaphunzira zambiri kuchokera kwa asayansi, “m’pamenenso amaona kuti zinali zosatheka kuti tikhale ndi moyo.” Zimenezi zikusonyeza kuti ngati tinachita kusintha kuchokera ku zamoyo zina, ndiye kuti zinali zosatheka kuti tikhale ndi moyo. Komabe, malinga ndi zimene ananena wasayansi wina, dzina lake John Horgan, “chilichonse chimene timaona chimasonyeza kuti chinapangidwa mwaluso kwambiri ndipo n’zokayikitsa kuti zinangokhalapo mwangozi.” Katswiri wina wa sayansi, dzina lake Freeman Dyson, ananena zofanana ndi zimenezi. Iye anati: “Ndikamafufuza mozama mmene zinthu za m’chilengedwe zinapangidwira, ndimaona umboni wamphamvu wosonyeza kuti dzikoli linakonzedwa kuti anthu adzakhalemo.”
Malinga ndi zimene takambirana zokhudza zinthu zogometsa zimene zili m’chilengedwe, kuchunidwa bwino kwa mphamvu za m’chilengedwe, ndiponso ubongo wa anthu, kodi si zomveka kuganiza kuti kuli Mlengi? Kuchita zimenezi n’kothandiza chifukwa iye ndi amene angatiuze mmene moyo unayambira komanso cholinga cha moyo wathu. Asayansi sangathe kutiuza zomveka pankhani imeneyi.
Nkhani yokhudza chilengedwe komanso mmene moyo unayambira inafotokozedwa bwino m’Baibulo, limene olemba ake amanena kuti anachita kuuziridwa ndi Mlengi. Mungachite bwino kufufuza zimene Baibulo limanena pankhaniyi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 12 Kuti mudziwe zambiri pankhani imeneyi, werengani nkhani imene ili patsamba 10 mpaka 26 m’buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 8]
Kodi n’zomveka kunena kuti ubongo wa munthu unakhalapo mwangozi?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]
Kodi N’chiyani Chimathandiza Asayansi Kufufuza Zinthu?
Asayansi amatha kufufuza zinthu za m’chilengedwe chifukwa choti zinalinganizidwa bwino komanso zimayenda motsatira malamulo. Malamulowa amatha kulembedwa n’kumagwiritsidwa ntchito ndi akatswiri a masamu ndi sayansi. Popanda malamulo amenewa, ntchito za sayansi ndi luso sizingatheke, ndipo bwenzi anthufe ndi zamoyo zonse palibe.
Choncho tingafunse kuti: Kodi ndani anakhazikitsa malamulo amenewa? Ndipo n’chifukwa chiyani amagwira ntchito mwanjira imeneyi? Ambiri amakhulupirira kuti kuli winawake wanzeru amene anapanga zonsezi. Kodi inuyo mumakhulupirira zotani?
[Bokosi/Zithunzi patsamba 7]
Kodi DNA inangokhalapo mwangozi?
Selo iliyonse ya munthu kapena nyama imakhala ndi DNA. Ndipo mu DNA mumakhala malangizo onse ofunikira okhudza mmene ziwalo za munthu zidzaonekere. DNA tingaiyerekezere ndi zinthu zimene zimajambulidwa mu DVD, ngakhale kuti mu DNA muli zinthu zambiri zovuta kumvetsa. Munthu akaika DVD mu wailesi kapena kompyuta, amatha kuonera kapena kumvetsera zimene zajambulidwazo. Mofanana ndi zimenezi, mu DNA mumakhala tizinthu topotana tooneka ngati makwerero timene timakhala ndi malangizo onse amene amathandiza kuti nyama ndi zomera zizioneka mosiyana ndi zinzake, nthochi zizisiyana ndi nyemba, mbidzi zizisiyana ndi nyerere, ndipo anthu azisiyana ndi anangumi.
Palibe angaganize kuti zinthu zimene zimakhala mu DVD zinangokhalamo mwangozi. Ndiye kodi ndi zomveka kuganiza kuti malangizo amene amakhala mu DNA anangokhalapo mwangozi?
[Mawu a Chithunzi patsamba 6]
Sombrero Galaxy: NASA and The Hubble Heritage Team (STScI/AURA)