Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tili ndi Moyo?

N’chifukwa Chiyani Tili ndi Moyo?

N’chifukwa Chiyani Tili ndi Moyo?

BAIBULO limanena kuti Mulungu, yemwe dzina lake ndi Yehova, ndi wanzeru kwambiri. Iye ndi amene anaika mphamvu zimene zili m’chilengedwechi komanso ndi Mlengi wa zinthu zonse. (Salmo 83:18; 92:5) Chaputala choyamba cha m’Baibulo chimati: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Kenako Mulungu anapanga munthu “m’chifanizo” chake, kutanthauza kuti wokhala ndi makhalidwe ofanana ndi a Mulungu. Ndipo Mulungu anauza munthuyo kuti abereke ana ndi kudzaza dziko lapansi.—Genesis 1:1, 26, 28.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti cholinga cha Mulungu popanga chilengedwechi, kuphatikizapo dziko lapansili komanso nyama ndi zomera, chinali chakuti anthu akhalemo basi? Kodi cholinga chake n’choti tingokhala ndi moyo zaka zochepa, kudya, kumwa ndiponso kubereka ana basi?

Kodi Mulungu Anali ndi Cholinga Chotani Potilenga?

Yehova Mulungu analenga anthu pofuna kusonyeza chikondi chake. Iye ankafuna kugawira ena moyo kuti azisangalala ngati iyeyo. N’zosakayikitsa kuti Mulungu anasangalala kwambiri atalenga zinthu zosiyanasiyana komanso zokongola n’cholinga choti anthu asangalale nazo. Ndipo koposa zonse, anthuwo anali ndi mwayi wokhala naye paubwenzi n’kumalankhulana naye. Anthu analengedwa kuti akhale ndi moyo kwamuyaya ndiponso kuti azikhala mwamtendere.—Genesis 3:8, 9; Salmo 37:11, 29.

Yehova anawapatsanso anthu ntchito yofunika komanso yosangalatsa. Mulungu anauza anthu oyambirira kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: Mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Choncho, banja loyambirira limeneli linapatsidwa ntchito yopanga dziko lonse lapansi kukhala malo okongola komanso osangalatsa kwambiri.

Panthawiyi zinthu sizinayende mogwirizana ndi mmene Yehova ankafunira. * Komabe, cholinga chimene Mulungu anali nacho polenga anthu chidzakwaniritsidwa.—Yesaya 46:9-11; 55:11.

Panopa anthu amafunitsitsa kudziwa Mulungu ndiponso kukhala naye paubwenzi ndipo zimenezi ndi umboni wakuti moyo wawo uli ndi cholinga. Anthu analengedwa ndi nzeru zotha kufufuza zinthu zatsopano. Ndipo Baibulo limanena kuti anthu adzapitirizabe kuphunzira za Mulungu ndi chilengedwe kwamuyaya.

Munthu wina amene analemba nawo Baibulo anafotokoza cholinga cha Mulungu polenga anthu. Iye anati: “Ndaona vuto limene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti avutidwe nalo. Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro. Ndidziwa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.” (Mlaliki 3:10-13) Choncho anthu sadzamaliza kuphunzira za Yehova komanso zinthu zimene iye analenga.

Muyenera Kuphunzira za Mulungu

Mungathe kumudziwa Yehova mwa kuona ndi kuganizira mozama zinthu zimene analenga. Munthu wina amene analemba nawo Baibulo ananena kuti “makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino lomwe. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga.” (Aroma 1:20) Ndithudi, zinthu zimene Yehova analenga zimasonyeza kuti iye ndi wachikondi, wanzeru komanso wamphamvu.

Chinthu china chimene chingatithandize kwambiri kuti timudziwe Mulungu ndi Baibulo. Buku louziridwa limeneli limatiuza zambiri zokhudza Yehova zomwe sitingazidziwe poyang’ana chilengedwe chake. Baibulo limatiuza za maganizo ake, makhalidwe ake komanso cholinga chake.

Baibulo limafotokoza za cholinga cha Mulungu kuti: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” (Salmo 115:16) Apa zikusonyeza kuti m’chilengedwe chonsechi, ndi dziko lapansi lokha limene lili malo abwino oti anthu angakhalepo. Ndipo Yehova analilengadi ndi cholinga choti anthu akhalepo.

Nanga bwanji za thambo lopanda malireli? Kodi nyenyezi zambirimbiri zimene timaonazi zinangokhalapo kuti zithandize kuti dzikoli likhale m’malo ake ndiponso kuti likhale ndi zamoyo? Kodi zinthu zimene timaona usiku zinangokhalapo ngati zokongoletsera thamboli? Tiyenera kuzindikira kuti pali zinthu zambiri zimene sitikuzidziwabe. Komabe ndi bwino kuti zinthu zina sitikuzidziwa. Kodi n’chifukwa chiyani tikutero?

Moyo wamuyaya sudzakhala wotopetsa chifukwa tidzakhala tikuphunzira zimene Mulungu wachita komanso zolinga zake ndipo sitidzazimaliza. Iye akufuna kuti tidzapitirize kuphunzira ndi kusangalala ndi zinthu zatsopano zimene tazitulukira. Moyo wosatha udzapereka mwayi wokwanira kwa anthu okhulupirika wophunzira zinthu zambiri zokhudza chilengedwechi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Zinthu zoipa zimene zimachitika komanso mavuto amene anthufe timakumana nawo, zimachititsa anthu ambiri kukayikira zoti pali Mlengi amene amatikonda. Pankhani imeneyi, onani mutu 11 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Anthu analengedwa ndi nzeru zotha kufufuza zinthu zatsopano

[Zithunzi patsamba 10]

Baibulo limasonyeza kuti dziko lapansili linalengedwa n’cholinga choti anthu akhalepo mosangalala