Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

▪ Kafukufuku waposachedwapa wasonyeza kuti “anthu 6 mwa anthu 10 alionse a ku Britain amaona kuti chipembedzo chikugawanitsa kwambiri anthu.”—THE CATHOLIC HERALD, BRITAIN.

▪ M’dziko la Portugal mwakhazikitsidwa makina aakulu kwambiri opanga mphamvu ya magetsi kuchokera ku dzuwa. Makinawa atenga malo aakulu mahekitala 250 ndipo azipanga magetsi omwe angagwiritsidwe ntchito m’nyumba 30,000.—EL PAÍS, SPAIN.

▪ Padziko lonse, achinyamata okwana 900,000 amafa pa ngozi zosiyanasiyana. Zimenezi zikutanthauza kuti tsiku lililonse achinyamata amene amafa amaposa 2,000. Achinyamatawa amafa pa ngozi zapamsewu, kumira m’madzi ndiponso kupsa ndi moto.—DIE WELT, GERMANY.

“Ngakhale kuti m’zaka za posachedwapa chiwerengero cha mitengo imene imadulidwa m’nkhalango chachepa, padziko lonse nkhalango zokwana masikweya kilomita 200 zikudulidwabe tsiku lililonse.”—FOOD AND AGRICULTURE ORGANIZATION OF THE UNITED NATIONS, ITALY.

Mu January 2009, anthu asanu amene analanda sitima yonyamula mafuta ya ku Saudi Arabia, anamira gulu lawo litalandira ndalama zokwana madola 3 miliyoni kuchokera kwa eniake a sitimayi. Mmodzi mwa anthuwa anakokoloka ndi madzi mpaka kugombe, komwe anapezeka ndi ndalama zokwana madola 153,000 m’thumba lake, zomwe zinali mu pepala la pulasitiki.—ASSOCIATED PRESS, SOMALIA.

Achinyamata Akuona Kuti Anzawo Akulekereredwa

Malinga ndi nyuzipepala ina ya ku Netherlands, achinyamata kumeneko “akuona kuti achinyamata anzawo akulekereredwa” ndipo “amasasatitsidwa, zomwe zimachititsa kuti azichita zinthu zosaganizira ena.” Pa achinyamata a zaka zoyambira 16 mpaka 24, “achinyamata awiri pa atatu alionse . . . amaona kuti ufulu umene achinyamata amapatsidwa umachuluka kuposa zinthu zimene achinyamatawo amayembekezeredwa kuchita.” Anthu ambiri akuona kuti “achinyamata amafuna ufulu wambiri . . . koma saganizira zimene angachite kuti athandize anthu ena.”

Ana a Sukulu Akumaphika Okha Chakudya

Mphunzitsi wamkulu wa pa sukulu ina ku Japan anapeza njira yothandiza makolo ndi ana awo kuthera nthawi yaitali ali limodzi. Njira yake inali yakuti anawo aziphika okha chakudya tsiku limodzi mwezi uliwonse. Sukulu yake inayamba kuchita zimenezi ndipo panopa sukulu zina zambiri zayambanso kuchita zimenezi. Nyuzipepala ina ya ku Japan inati: “Sikuti anawo amayembekezeredwa kuchita zonse okha pophika chakudya chawo. Koma m’kupita kwa nthawi amayamba kuchita zambiri okha. Ana a kalasi iliyonse amapatsidwa zochita mogwirizana ndi msinkhu wawo. Ana a makalasi oyambirira amapempha makolo kapena abale awo kuti awathandize kusankha chakudya chimene angaphike komanso zinthu zimene angafunike kugula. . . . Pamene ana a m’makalasi akuluakulu amauzidwa kuphika chakudya cha magulu onse chimene angakonde.” Kodi zimenezi zathandiza? “Sukulu zambiri zanena kuti zimenezi zathandiza kuti chakudya chambiri chisamawonongeke, kuti ana adziwe kuphika, komanso zathandiza kuti ana azicheza ndi makolo awo.” Ana nawonso ananena kuti zimenezi “zawathandiza kuyamikira zimene makolo awo amawachitira.”—IHT Asahi Shimbun

Ntchito Yochotsa Zinyalala ku South Pole

Chaka chatha, akatswiri a ku Russia anachotsa zinyalala zokwana matani 360 ku Antarctica n’cholinga choteteza zinthu zachilengedwe. Zinyalala zimene zinatayidwa pamalo enaake opangira kafukufuku ku South Pole zikuphatikizapo zipangizo zomangira, makina owonongeka ndiponso migolo ya mafuta yopanda kanthu. Magazini ya Itogi ya ku Russia inanena kuti: “Malinga ndi malamulo oteteza zachilengedwe kum’mwera kwambiri kwa dziko lapansi, dziko lililonse liyenera kuchotsa zinyalala zake. Anthu a ku Japan ndi amene akudzipereka kwambiri pochotsa zinyalala zawo.”