Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Lekani Kuda Nkhawa’

‘Lekani Kuda Nkhawa’

‘Lekani Kuda Nkhawa’

“Ndalama zathu zonse zimene zinali kubanki zinatha, kuphatikizapo zimene tinasungira ana athu. Kwa miyezi yambiri tinalibe ndalama.”

● Ndinali ndi sukulu kudera linalake la kumudzi ku India, ndipo inkachita bwino kwambiri. Panthawi ina ndinali ndi ana a sukulu okwana pafupifupi 500. Kenako sukulu inayake yotchuka ya kutauni inayamba kutumiza mabasi ake kudera kwathu. Zimenezi zinachititsa kuti ana ambiri achoke kusukulu yanga n’kumakaphunzira kusukulu imeneyo. Ndipo chiwerengero cha ana pasukulu yanga chinatsika kuchoka pa 500 n’kufika pa 60. Kuwonjezera apa, munthu wina yemwe ankagwira ntchito pasukulu yanga analephera kusunga pangano limene tinagwirizana ndipo mpaka pano ali ndi ndalama zanga zambiri. Popeza kuti ndinali ndi anthu ambiri oti ndiziwalipira, zinthu zinayamba kundivuta.

Ndinakambirana ndi banja langa za nkhaniyi. Tinagwirizana zotsatira chitsanzo cha Yesu chokhala ndi moyo wosafuna zambiri komanso kukhala ndi ‘diso lolunjika chimodzi.’ Sitinkawononga ndalama zambiri kuposa zimene tinkapeza. (Mateyo 6:22, 25) Kwa kanthawi ndithu, tinasiya kuyendera galimoto yathu n’cholinga chakuti tisawononge ndalama pogula mafuta komanso pokonzetsa ikawonongeka. Tinkakagula zakudya zathu madzulo chifukwa panthawiyi zakudya zambiri zimakhala zotsala ndipo zimatchipirapo. Komanso tinasiya kugula zakudya zina zimene poyamba tinkakonda kudya.

Ndife a Mboni za Yehova ndipo timaona kuti kusonkhana ndi okhulupirira anzathu n’kofunika kwambiri. (Aheberi 10:25) Choncho ngakhale kuti tinalibe ndalama zambiri, tinatsimikiza kuti tisamalephere kupita kumisonkhano ya mpingo komanso ikuluikulu, ngakhale kuti nthawi zina tinkayenda ulendo wautali. Utumiki wathu umaphatikizapo kuphunzitsa anthu Baibulo, ndipo nthawi zina timafunikira kupita kutali kwambiri. Pa maulendo ngati amenewa, tinkagwiritsa ntchito njinga m’malo mwa galimoto. Tinkayendera njinga ngakhale kuti sizinkatheka kukwera njingayi anthu oposa awiri.

Komabe zimenezi sizinachititse kuti tizilalikira nthawi yochepa. M’malo mwake mkazi wanga komanso mwana wathu wamkazi ankaphunzitsa anthu ambiri Baibulo kuposa poyamba. Nthawi zina iwo ankayenda ulendo wa makilomita 6 kapena 8 akamapita kokaphunzitsa anthu Baibulo. Inenso ndi mwana wathu wamwamuna tinkathanso nthawi yambiri tikuphunzitsa anthu Baibulo.

Panopa zinthu zayambanso kutiyendera bwino. Komabe zimene zinatichitikirazi zatiphunzitsa kuti si bwino kudalira kwambiri chuma. Taphunziranso kuti si bwino kuda nkhawa kwambiri ndi zinthu zimene sitingazisinthe. Taona kuti lemba la Salmo 55:22 ndi lolimbikitsa kwambiri. Lembali limati: “Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” Panthawi yonse imene tinali pa mavuto azachuma, taona kuti mawu onse a m’lembali ndi oona.—Nkhaniyi tachita kutumiziridwa.