Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Musamafune Zambiri Pamoyo Wanu

Musamafune Zambiri Pamoyo Wanu

Musamafune Zambiri Pamoyo Wanu

KUKHALA ndi moyo wosafuna zambiri n’kothandiza kwambiri. Koma kodi mungatani kuti mukhale ndi moyo wotere? Muyenera kukhala ndi cholinga chokwaniritsa zinthu zimene mumaona kuti ndi zofunika kwambiri pamoyo wanu. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

Dzifunseni kuti: ‘Kodi panopa ndakwanitsa kuchita chiyani? Nanga chatsala n’chiyani?’ Lembani m’munsimu zinthu zimene mukufuna kuchita:

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

Masiku ano anthu ambiri saganizira za m’tsogolo. Iwo amangoganizira zokhala ndi chuma basi. Tinganene kuti iwo amati: “Tiyeni tidye ndi kumwa, popeza mawa tifa.” (1 Akorinto 15:32) Iwo amakhulupirira kuti chinthu chofunika kwambiri pamoyo ndi kugwira ntchito kuti akhale ndi ndalama zambiri. Koma Baibulo limasonyeza kuti maganizo amenewa ndi olakwika.

M’fanizo lake lina, Yesu anafotokoza za munthu amene anadzikundikira chuma koma anafa asanadyerere chuma chakecho. Yesu anati: “Umu ndi mmene zimakhalira kwa munthu amene wadziunjikira yekha chuma, koma amene sali wolemera kwa Mulungu.” (Luka 12:16-21) Kodi munthuyu analakwa kugwira ntchito mwakhama kuti apeze zimene amafuna pamoyo wake? Ayi. Vuto lake linali lakuti ankakonda kwambiri chuma ndipo sankaganizira Mulungu pa zochita zake. N’zomvetsa chisoni kuti chifukwa cha zimenezi, chuma chonse chimene anachivutikiracho chinali chopanda phindu.—Mlaliki 2:17-21; Mateyo 16:26.

Mosiyana ndi zimenezi, Yesu anatilangiza kuti tizigwira ntchito kuti tipeze zinthu zokhalitsa. Iye anati: “Musagwirire ntchito chakudya chimene chimawonongeka, koma chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha.” (Yohane 6:27) Nthawi inanso m’mbuyomo, Yesu ananena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Kunena zoona, moyo wosatha ndi mphoto yapamwamba kwambiri.

Mmene Mungathetsere Nkhawa

Yesu ankadziwa kuti anthufe timakonda kuda nkhawa ndi zinthu zakuthupi. Choncho, iye analangiza ophunzira ake kuti: “Lekani kufunitsitsa chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa, ndipo siyani kuda nkhawa; pakuti zonsezi ndi zinthu zimene amitundu a dzikoli amazifunafuna mwakhama, koma Atate wanu amadziwa kuti zinthu zonsezi inu mumazisowa. Koma inu, funitsitsani kosaleka ufumu wake, ndipo zinthu zimenezi zidzawonjezedwa kwa inu.”—Luka 12:29-31.

Mawu amenewa athandiza Akhristu ambiri kuti akhale ndi moyo wosafuna zambiri. Mwachitsanzo, Juliet, yemwe amakhala ku Malaysia, anati: “Ntchito yomwe ndinkagwira inkanditopetsa kwambiri. Choncho, ine ndi mwamuna wanga tinapemphera kuti Yehova atithandize kukhala ndi moyo wosafuna zambiri. Iye sanachedwe kuyankha pemphero lathu. Pasanathe mwezi, ndinapeza ntchito yophunzitsa ana olumala.” Munthu winanso wa ku Australia, dzina lake Steve, yemwe ali ndi kampani yofolera nyumba, anasintha kagwiridwe ka ntchito kuti azikhala ndi nthawi yambiri yochita zinthu zauzimu ndi banja lake. Mkazi wake Maureen ananena kuti: “Mwamuna wanga amasangalala kuposa kale, ndipo ine ndi ana timasangalalanso. Ndipo ndaona kuti pabanja mukamapanda kufuna zambiri, aliyense amasangalala.”

Koma ngati ntchito yakutherani ndipo mwina mufunika kutuluka m’nyumba yomwe mukukhala, pangafunike chikhulupiriro cholimba kuti mutsatire malangizo a Yesu akuti musadere nkhawa. Komabe, ngati mutaika zinthu zauzimu patsogolo ndiponso kudalira Mulungu, mungathe kukhala ndi moyo wosafuna zambiri. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kudzapeza ‘moyo weniweni,’ womwe ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. M’dziko limeneli mudzakhala chilungamo ndipo ntchito iliyonse imene anthu azidzagwira idzakhala yosangalatsa ndiponso yopindulitsa.—1 Timoteyo 6:17-19; Yesaya 65:21-23.

Kodi mungakonde kuphunzira zambiri zokhudza ‘moyo weniweni’ umene Baibulo limalonjeza? Ngati mungakonde, onanani ndi munthu wa Mboni za Yehova m’dera lanu, kapena lembani kalata ku adiresi yoyenera patsamba 5 la magazini ino.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

M’dziko latsopano la Mulungu, ntchito iliyonse idzakhala yosangalatsa ndiponso yopindulitsa

[Bokosi patsamba 8]

NTCHITO ZIMENE MUNGAGWIRE KWINA

M’munsimu muli ntchito zimene anthu m’mayiko ena angagwire ngati ntchito zina zikusowa.

● Kulondera pakhomo (ngati eni nyumba apita kukagwira ntchito kwina kapena ali kutchuthi)

● Kuyeretsa: m’masitolo; m’maofesi; m’nyumba zongomangidwa kumene, zomwe zapsa kapena zomwe anthu asamukamo, komanso kugwira ntchito zina zapakhomo (m’nyumba za ena); mungayeretsenso mawindo (m’maofesi kapena pakhomo)

● Kukonza zinthu: njinga, zipangizo zosiyanasiyana (m’malaibulale mumakhala mabuku ambiri ofotokoza mmene mungakonzere zinthu zosiyanasiyana)

● Ntchito zamanja: kukonza makabati, zitseko, makonde, kupenta, kumanga mpanda, kukhoma denga

● Ntchito zaulimi: kubzala mbewu, kuthyola zipatso, kukolola

● Kubzala ndi kusamalira maluwa: m’maofesi, m’mabanki, m’masitolo ndi m’malo ena

● Kuyang’anira malo

● Kuika ndiponso kutsuka kapeti

● Kugulitsa nyuzipepala

● Kusamutsa katundu, kusunga katundu

● Kudulira mitengo, kutchetcha, kudula mitengo

● Kuyendetsa basi yonyamula ana a sukulu

● Kujambula zithunzi (pakakhala mwambo winawake)

● Kugulitsa nyambo kwa asodzi

● Kusinthana ntchito: kukonza galimoto kuti inuyo akukonzereni magetsi, kusoka kuti inuyo akukonzereni mpopi wa madzi

Mukafuna kudziwa zambiri onani Galamukani! ya March 8, 1996, masamba 3-11.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

NTCHITO ZIMENE MUNGAGWIRE PANYUMBA PANU

Ganizirani bwinobwino zinthu zimene anthu a m’dera lanu amafuna. Funsani anthu a kwanuko. Ndipo yesetsani kuchita khama.

● Kulera ana a anthu ena

● Kugulitsa masamba kapena maluwa; kugulitsa zakumwa

● Kusoka zovala

● Kukonza zinthu zokagulitsa kumafakitale

● Kuphika zakudya

● Kuluka zinthu zosiyanasiyana

● Kusoka nsalu za m’mipando

● Kutayipa zinthu zosiyanasiyana ndiponso kulemba zinthu za anthu pakompyuta

● Kutsegula malo oyimbira foni

● Kukonza tsitsi

● Kuchititsa lendi nyumba

● Kutumiza makalata a anthu otsatsa malonda

● Kutsuka magalimoto

● Kusamalira ziweto za anthu ena

● Kukonza makiyi ndi maloko

Dziwani izi: Zambiri mwa ntchito zimenezi mungazilengezetse pamtengo wotsika m’manyuzipepala kapena mungakhome mapepala m’mitengo kapena m’malo ena.