Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
“Padziko lonse, anthu 60 pa 100 alionse ali ndi foni zam’manja . . . Zimenezi zikusonyeza kuti zinthu zasintha kwambiri, chifukwa zaka 6 zapitazo anthu amene anali ndi foni zam’manja anali 15 pa 100 alionse.”—MACLEAN’S, CANADA.
M’zaka 10 zapitazo, chiwerengero cha mitundu yatsopano ya zinthu zamoyo zimene zapezedwa m’madera a pafupi ndi mtsinje wa Mekong, womwe uli kumwera chakum’mawa kwa Asia, chakwana 1,068.—WORLD WILDLIFE FUND, UNITED STATES.
“Pa akaidi amene ali m’ndende za padziko lonse, 25 pa 100 alionse ali m’ndende za ku America. Izi n’zodabwitsa kwambiri chifukwa pa anthu 100 alionse padzikoli, 5 ndi a ku America. Pa anthu 100,000 alionse a ku America, 756 anatsekeredwa m’ndende.—THE ECONOMIST, BRITAIN.
“Zipangizo Zamakono Zikusokoneza Anthu Ambiri”
Zipangizo zina zamakono zikusokoneza anthu pogwira ntchito. Akatswiri oona za mmene zipangizo zosiyanasiyana zimakhudzira anthu, ananena kuti, “zipangizo zamakono zikusokoneza anthu ambiri ndipo zikuchititsa kuti anthu asamaike maganizo awo onse pa zimene akuchita.” Akuti zinthu zina zimene zikusokoneza anthu ndi kutumizirana uthenga pafoni kapena pakompyuta, kalendala yotikumbutsa zimene tikufunika kuchita, phokoso lokudziwitsani kuti mwalandira uthenga pakompyuta kapena pafoni ndi zinthu zina zotero. Chifukwa chakuti zinthu zimenezi zimawasokoneza kawirikawiri, “zikuchititsa kuti anthu asamaike maganizo awo onse pantchito imene akugwira komanso kuti asamamalize ntchitoyo,” inatero nyuzipepala ya Newsweek. Ndipo mavuto ena obwera chifukwa cha kusokonezedwa kumeneku ndi “kuiwalaiwala” ndiponso kulakwitsa zinthu kawirikawiri.
Pakufunika Anthu Ambiri Omasulira Nkhani
Anthu omasulira nkhani akufunika kwambiri m’makhoti, kupolisi, m’zipatala ndi m’malo ena m’dziko la United States. Nkhani ina mu nyuzipepala ya Reuters inanena kuti zimenezi zili choncho chifukwa chakuti “anthu ambiri akulankhula zinenero zosiyanasiyana.” Mwachitsanzo, kampani inayake ku California imalemba ntchito anthu omasulira nkhani okwana 5,200 omwe amalankhula zinenero 176. Zina mwa zinenerozi ndi zikuluzikulu, monga Chitchaina, Chirasha, Chisipanishi komanso zing’onozing’ono za ku Africa ndi Mexico. Munthu akawaimbira foni, makampaniwa “amatha kudziwa chilankhulo chimene munthu akulankhula” pasanathe ndi mphindi imodzi yomwe, ndipo nthawi yomweyo amalumikiza foniyo kwa womasulira kuti athandize “kulankhulana ndi munthuyo.”
Golide Akupezeka Kumalo Osayembekezereka
Nkhani ina imene mtolankhani wa nyuzipepala ya Reuters ku Japan analemba, inanena kuti kutawuni ya Nagano, kumpoto chakumadzulo kwa mzinda wa Tokyo, “atulukira kuti kumalo otayira nyansi za m’chimbudzi kumapezeka miyala ya mtengo wapatali.” Akatswiri atulukira kuti ngati nyansi zosungidwa kumalo otchedwa Suwa zitawotchedwa, muphulusa lake mutha kupezeka golide wambiri kuposa golide amene amakumbidwa m’migodi yaikulu kwambiri ya m’dziko la Japan. M’chaka chimodzi chokha, golideyu akhoza kubweretsa ndalama zopitirira madola 167,000. Nyuzipepalayi inanenanso kuti anthu akuganiza kuti malowa akupezeka ndi golide wambiri chifukwa chakuti ali pafupi ndi “mafakitale omwe amagwiritsa ntchito miyala yachikasuyi.”