Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoyenera Kuchita Mukakhala Pachibwenzi

Zoyenera Kuchita Mukakhala Pachibwenzi

Zimene Baibulo Limanena

Zoyenera Kuchita Mukakhala Pachibwenzi

Lee ndi Julie anali pachibwenzi ndipo ankafunitsitsa kudzisunga mpaka kudzakwatirana. * Koma tsiku lina madzulo ali awiriwiri, anatsala pang’ono kuti agonane. Mwamwayi, anazindikira msanga kuti atsala pang’ono kuchita tchimo lalikulu.

KULAMBIRA koona kumaphatikizapo zambiri osati kumangopita kumisonkhano yachipembedzo mlungu ndi mlungu. Munthu amene akufuna kulambira Mulungu movomerezeka, amafunika kutsatira malamulo a Mulungu komanso ayenera kukhala ndi khalidwe labwino. Yesu Khristu ananena kuti Mulungu amakonda anthu okhawo “amene akuchita chifuniro” chake. (Mateyo 7:21) Kuti tisangalatse Mulungu, timafunika kupewa kuchita zinthu zolakwika pamene tili pachibwenzi, ndipo tikamayamba chibwenzicho, cholinga chathu chiyenera kukhala kudzakwatirana ndi munthuyo.

Masiku ano, kuli zinthu zambiri zimene zimachititsa anthu amene ali pachibwenzi kuchita zinthu zolakwika. Kodi inuyo mungatani kuti chibwenzi chanu chikhale choyera pamaso pa Mulungu? Choyamba, muyenera kudziwa kuti Mulungu anatipatsa malamulo n’cholinga choti zinthu zizitiyendera bwino. Chachiwiri, muyenera kudziwa kuti mtima ndi wonyenga. Chachitatu, muyenera kukambirana mfundo zoti muzitsatira pachibwenzi chanu. Ndipo chachinayi, simuyenera kuiwala Yehova pachibwenzi chanu. Tiyeni tikambirane mfundozi, imodzi ndi imodzi.

Malamulo a Mulungu Ndi Othandiza

Lemba la Yesaya 48:17, 18, limati: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”

Ndithudi, cholinga cha malamulo ndiponso mfundo zimene zili m’Mawu a Mulungu, Baibulo, n’chakuti zitithandize ifeyo. (2 Timoteyo 3:16, 17) Malamulo ndiponso mfundo zimenezi ndi umboni wakuti Mlengi wathu amatiganizira ndipo amafuna kuti tizisangalala ndiponso kuti zinthu zizitiyendera bwino pamoyo wathu. (Salmo 19:7-10) Kodi inuyo mumaona choncho mumtima mwanu? Ngati mumaona choncho, ndiye kuti mukusonyeza nzeru yeniyeni.

Dziwani Kuti Mtima Ndi Wonyenga

Yehova ali ngati mnzathu wapamtima, amene amatiuza zoona zokhazokha ndipo satibisira chilichonse chokhudza ifeyo. Mwachitsanzo, Mawu ake amatichenjeza kuti “mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?” (Yeremiya 17:9) Baibulo limanenanso kuti: “Wokhulupirira mtima wake wake ali wopusa; koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.”—Miyambo 28:26.

Kodi anthu amene ali pachibwenzi angasonyeze bwanji kuti amakhulupirira mtima wawo? Njira imodzi yochitira zimenezi ndi kuchita zinthu zimene zingawachititse kuti agonane, ngati mmene zinalili ndi Lee komanso Julie. Njira inanso ndi kunyalanyaza malangizo anzeru operekedwa ndi makolo oopa Mulungu. Makolo otero amadziwa kuti achinyamata amakhala ndi chilakolako champhamvu chofuna kugonana ndipo amafunika kuthandizidwa kuti asachimwe.

Choncho, achinyamata amene amatsatira nzeru ya Mulungu, sapeputsa malangizo a makolo awo. Iwo amatsatira ndi mtima wonse malangizo a makolo amene amawakonda, ngakhale makolowo awauze zinthu zimene iwo sangasangalale nazo. Munthu yemwe amakukondani kwambiri ndi Atate wanu wakumwamba, Yehova Mulungu, yemwe amakulangizani ‘kuchotsa zopweteka m’mtima mwanu, ndi kulekanitsa zoipa ndi thupi lanu.’ (Mlaliki 11:9, 10) Kodi mungachite motani zimenezi? Musamagonjere zilakolako zolakwika.

Kambiranani Mfundo Zoti Muzitsatira

Baibulo limati: “Anthu amene amakhala pamodzi n’kumakambirana amakhala ndi nzeru.” (Miyambo 13:10, NW) Chibwenzi chikangoyamba kumene, anthu ochenjera amakambirana mfundo za m’Malemba zoti azitsatira pankhani yosonyezana chikondi moyenera. Ndipo amatsimikiza kutsatira mfundo zimenezo. Musayese dala kusonyezana chikondi mosayenera kapena kudzidalira, chifukwa kuchita zimenezi kuli ngati kuyendetsa galimoto mosatsatira malamulo a pamsewu. Si nzeru kuganiza zoyamba kutsatira malamulo a pamsewu mutachita kale ngozi.

Baibulo limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” (Miyambo 22:3) Anthu amene ali pachibwenzi angapewe mavuto ambiri ngati amachezera pagulu kapena amatenga munthu wina wodalirika popita koyenda. Mavuto omwe mungakumane nawo chifukwa chonyalanyaza mfundo imeneyi ndi monga kuwononga chikumbumtima chanu, kudzichotsera ulemu wanu ndiponso ulemu wa mnzanuyo. Mungachititsenso manyazi anthu onse amene adziwa, kuphatikizapo achibale. Choncho, khalani ochenjera. Kambiranani mfundo za m’Malemba ndipo muziyesetsa kuzitsatira.

Muziganizira Yehova Pachibwenzi Chanu

Banja lili ngati chingwe cha nkhosi zitatu, ndipo Mulungu ndiye nkhosi yaikulu ya chingwe chimenechi. Lemba la Mlaliki 4:12 limati: “Chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.” (Mlaliki 4:12) Mfundo imeneyi imakhudzanso anthu amene ali pachibwenzi. Ngati mukufuna kuti Mulungu adalitse chibwenzi chanu, aliyense wa inu ayenera kuyesetsa kukhala paubwenzi ndi Mulungu. Lemba la Salmo 1:1-3 limati: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, . . . Komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. . . Ndipo zonse azichita apindula nazo.”

Ndithudi, kuti zinthu zitiyendere bwino pamoyo wathu, kuphatikizapo pamene tili pachibwenzi ndiponso m’banja, timafunika kuchita zinthu zimene Yehova amasangalala nazo. Ndipotu iye ndi Mlengi wathu ndiponso ndi amene anatipatsa mphatso yoti tizikondana ndi munthu wina komanso ndi amene amapereka mphatso ya ukwati. Choncho, tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti timayamikira mphatso zimenezi.—Yakobe 1:17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Maina ena tawasintha.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amatifunira zabwino?—Yesaya 48:17, 18.

● Kodi tiyenera kudziwa chiyani chokhudza mtima wathu?—Yeremiya 17:9.

● Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti zinthu zikuyendereni bwino pachibwenzi komanso m’banja?—Salmo 1:1-3.

[Chithunzi patsamba 13]

Chibwenzi chikangoyamba kumene, anthu ochenjera amakambirana mfundo za m’Malemba zoti azitsatira pankhani yosonyezana chikondi moyenera, ndipo amatsimikiza kutsatira mfundo zimenezo