Anthu Akhala Akulambira Njoka kwa Zaka Zambiri
Anthu Akhala Akulambira Njoka kwa Zaka Zambiri
ANTHU anayamba kale kwambiri kulambira njoka. Anthu akale a ku Iguputo komanso anthu ena amene ankakhala ku Kerete ankalambira njoka. Aisiraeli ena ankapereka nsembe kwa njoka ya mkuwa. Aisiraeli enanso ankapereka nsembe kwa mafano a “zokwawa.”—Ezekieli 8:10-12; 2 Mafumu 18:4.
Kale anthu ambiri ku Mexico ankalambira milungu yooneka ngati njoka. Nthawi zina, anthu a mtundu wa Maya ankagwiritsa ntchito njoka ngati mulungu wawo wamkulu, yemwe ankadziwika ndi dzina lakuti Itzamná. Mulungu wa maphunziro, chikhalidwe, komanso nzeru wa anthu a mtundu wa Toltec, yemwe ankadziwika ndi dzina lakuti Quetzalcoatl, ankaoneka ngati njoka ndipo anali ndi nthenga. Ponena za mulungu ameneyu, magazini ina ya ku Mexico inati: “Mulungu ameneyu anali ndi maudindo ambiri kuposa milungu ina yonse imene anthuwa anali nayo.”
Kwa zaka zambiri, anthu a ku Mexico ankalambira mulungu wooneka ngati njoka ameneyu. Ngakhale masiku ano anthu a mtundu wa Cora komanso Huichol, omwe amakhala ku Mexico, amalambirabe mulunguyu. Panthawi ya chikondwerero anthuwa amavala nthenga n’kumayenda ndi mimba ngati njoka. Anthu a mtundu wa Quiche, omwe amakhala kumadzulo kwa dziko la Guatemala, amavina ndi njoka akamachita miyambo ina. Anthu a mtundu wa Chorti, omwe amakhala ku Guatemala, amalambira mafano a njoka zokhala ndi nthenga omwe amawaona kuti amaimira abambo kapena amayi oyera a tchalitchi cha Katolika.
Koma funso ndi lakuti: Kodi Mulungu amene analenga anthu komanso nyama, amawaona bwanji anthu amene amalambira njoka?
Kodi Mulungu Amaiona Bwanji Nkhani Yolambira Njoka?
Yehova Mulungu analamula Aisiraeli kuti: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo.”—Eksodo 20:4, 5.
Yehova analetsa anthu ake kuti asamalambire nyama kapena njoka. Choncho kodi si zoonekeratu kuti anthu amene akufuna kukondweretsa Mulungu sayenera kulambira njoka? N’chifukwa chiyani Mulungu amadana ndi mafano, kuphatikizapo kulambira njoka? Funso limeneli ndi losavuta kuyankha: Yehova ndi amene analenga anthu, njoka ndi zamoyo zonse. Zonsezi ndi ntchito ya manja ake. Choncho, tiyenera kulambira iyeyo osati zinthu zimene analenga.
Mwachitsanzo, taganizirani kuti munthu wamanga nyumba ndipo wauza anthu ena kuti azikhalamo. Kodi zingakhale bwino kuti anthuwo azithokoza ndi kutamanda nyumbayo m’malo mwa munthu amene anamanga nyumbayo? Ngati anthuwo atachita zimenezi, tingati ndi opanda nzeru ndipo munthu amene anamanga nyumbayo sangasangalale. Mulungu sasangalalanso anthu akamalambira zinthu zimene analenga m’malo molambira iyeyo.
Choncho, n’zoonekeratu kuti anthu amene amafuna kukondweretsa Mulungu, ayenera kumvera chenjezo limene mtumwi Yohane ananena, lakuti: “Ana apamtima inu, pewani mafano.”—1 Yohane 5:21.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 23]
KODI MWAMBO WOGWIRA NJOKA POLAMBIRA NDI WOGWIRIZANA NDI BAIBULO?
● Matchalitchi ena ku United States amauza anthu awo kuti akamapemphera kwa Mulungu azinyamula njoka. Ena amaika njoka paphewa ndipo ena amanyamula njoka zambirimbiri nthawi imodzi. Nthawi zina njokazi zikawopsezedwa zimawaluma. Ndipo anthu ena akhala akumwalira chifukwa cholumidwa ndi njoka zimene ananyamula.
Anthu amene amanyamula njoka polambira amati akutsatira zimene lemba la Maliko 16:17, 18 limanena. Mawu ena a m’lembali amati: “Adzanyamula njoka ndi manja awo.” Baibulo la King James Version ndiponso Mabaibulo ena akale amasonyeza ngati kuti mavesiwa analimo m’mipukutu yoyambirira. Koma Mabaibulo a New Revised Standard Version, New American Standard Bible, ndi The New King James Version amasonyeza kuti mavesiwa sapezeka m’mipukutu yoyambirira ya Uthenga Wabwino wa Maliko.
Zimene Baibulo limaphunzitsa sizigwirizana ndi maganizo akuti kunyamula njoka polambira n’koyenera. Baibulo limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Inunso mukhoza kuvomereza kuti Mulungu sangalole kuti olambira ake azimulambira atanyamula njoka, zomwe ndi zoopsa. Mwana wake, Yesu, anapempha anthu kuti: “Bwerani kwa ine, nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani.” (Mateyo 11:28, 29) Yehova komanso Yesu sangafune kuti anthu amene Palibe munthu amene angatsitsimutsidwe ngati akumva ululu, akudwala kapena kufa kumene chifukwa cholumidwa ndi njoka. Ndipo Yehova ndi Yesu sangafune zimenezi.
[Mawu a Chithunzi]
REUTERS/Tami Chappell
[Chithunzi patsamba 22]
Anthu a ku Mexico ankagwiritsa ntchito fano lokhala ndi nthenga looneka ngati njoka
[Chithunzi patsamba 22]
Quezalcoatl, anali mulungu wosemedwa wa a Toltec. Mulunguyu anali ndi nthenga ndipo ankaoneka ngati njoka
[Mawu a Chithunzi patsamba 22]
Top: REUTERS/Tami Chappell; bottom: © Leonardo Díaz Romero/age fotostock