Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi n’kulakwa kuchita zinthu zina pandekha?

Kodi n’kulakwa kuchita zinthu zina pandekha?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi n’kulakwa kuchita zinthu zina pandekha?

Pa zitsanzo zili m’munsizi, chongani m’kabokosimo zimene mungachite.

1. Muli kuchipinda chanu ndipo mwatseka chitseko. Kenako mng’ono wanu akulowa popanda kugogoda.

‘Palibe vuto . . . Nthawi zina inenso ndimachita zomwezo.’

‘Ndingaone kuti ndi mwano, chifukwa akhoza kundipeza ndikuvala.

2. Mukulankhula ndi mnzanu pa foni ndipo mayi anu ali pafupi kwambiri moti akumva zonse zimene mukukambirana.

‘Palibe vuto . . . Palibe chilichonse choti ndiziwabisira.’

‘Ndingakhumudwe kwambiri ndipo ndingaone kuti akundilondalonda.’

3. Mwangofika kumene panyumba ndipo mwangofikira kufunsidwa mafunso ambirimbiri ndi makolo. “Unali kuti? Unapita kukatani? Unapita ndi ndani?”

‘Palibe vuto . . . Ndimawauza chilichonse.’

‘Ndingakhumudwe kwambiri chifukwa ndingaone kuti makolo anga sandikhulupirira.’

MULI mwana, mwina simunkafuna kukhala panokha nthawi zina. Ndipo ngati mng’ono wanu walowa m’chipinda chanu popanda kugogoda, simunkakhumudwa. Nthawi imeneyo anthu ankadziwa chilichonse chimene mukuchita. Koma panopa mumafuna kuti anthu asamadziwe chilichonse chimene mukuchita. Mnyamata wina wazaka 14, dzina lake Corey, anati: “Nthawi zina ndimafuna kuti anthu ena asadziwe zinthu zina zomwe ndikuchita.” *

Kodi mukudziwa chifukwa chake panopa mumafuna kuchita zinthu zinazake panokha? N’chifukwa chakuti mukukula. Mwachitsanzo, thupi lanu likusintha ndipo zimenezi zimachititsa kuti muzida nkhawa kwambiri ndi mmene mukuonekera, ngakhale pamene muli ndi anthu am’banja lanu. Chifukwa chinanso n’chakuti pamene munthu akukula, amakhala ndi nkhani zachinsinsi zimene amafuna kuti aziganizire payekha. Umenewu ndi umboni wakuti mwayamba “kulingalira” mwakuya, lomwe ndi khalidwe limene Baibulo limalimbikitsa. (Miyambo 1:1, 4; Deuteronomo 32:29) Ngakhale Yesu anapita “payekha” kuti akasinkhesinkhe.—Mateyo 14:13.

Komabe, muyenera kukumbukira kuti mudakali mwana wapakhomo, ndipo makolo anu ali ndi ufulu wodziwa zimene zikukuchitikirani pamoyo wanu. (Aefeso 6:1) Koma mwina inu simungasangalale ndi zimene iwo amafuna atadziwazo chifukwa inuyo mumaona kuti mwakula. Ndiyeno kodi mungatani kuti musamalimbane ndi makolo anu pankhani imeneyi? Tiyeni tione zinthu ziwiri zimene zingayambitse mavuto.

Mukamakhala Panokha

Nthawi zina pangakhale zifukwa zomveka zofunira kukhala panokha. Mwachitsanzo, mwina mungafune kuti “mupumule pang’ono.” (Maliko 6:31) Kapenanso mungafune kuti mupemphere, mogwirizana ndi malangizo amene Yesu anapatsa ophunzira ake, akuti “popemphera, lowa m’chipinda chako pawekha ndi kutseka chitseko, ndipo pemphera kwa Atate wako.” (Mateyo 6:6; Maliko 1:35) Koma vuto ndi lakuti, ngati mutadzitsekera kuchipinda kwanu, (ngati muli ndi chipinda chanuchanu), makolo anu sangadziwe kuti mwatseka n’cholinga chakuti mupemphere. Ndipo ang’ono anu sangadziwe chifukwa chake mukufuna kukhala panokha.

Zimene mungachite. M’malo mokangana ndi anthu ena chifukwa chofuna kukhala panokha, chitani zotsatirazi.

● Mungauze ang’ono anu malamulo angapo oti azitsatira, n’cholinga chakuti muzikhala ndi mpata wochita zinthu zina panokha. Makolo anu akhoza kukuthandizani kuchita zimenezi.

● Muziyesetsa kuwamvetsa makolo anu. Mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Rebekah, anati: “Nthawi zina makolo anga amabwera kuchipinda kwanga kuti aone zimene ndikuchita. Koma kunena zoona, inenso ndingachite zomwezi nditakhala kholo, makamaka chifukwa chakuti masiku ano achinyamata akukumana ndi mavuto ambiri.” Mofanana ndi Rebekah, mungachite bwino kuyesetsa kudziwa zomwe zikuchititsa makolo anu kuti akhudzidwe kwambiri.—Miyambo 19:11.

● Dzifunseni moona mtima kuti: ‘Kodi nthawi zina ndimachita zinthu zinazake zimene zimachititsa kuti makolo anga azindikaikira ndikadzitsekera? Kodi ndimabisa umunthu wanga moti n’chifukwa chake makolo anga amandibisalira kuti adziwe zambiri zokhudza ineyo?’ Dziwani kuti ngati simubisira makolo anu chilichonse, iwo sangamakukaikireni. *

Zoti muchite. Lembani m’munsimu zinthu zimene munganene kuti muyambe kukambirana ndi makolo anu nkhaniyi.

․․․․․

Mukayamba Kucheza ndi Anzanu

Monga wachinyamata, sikulakwa kucheza ndi anthu ena omwe si a m’banja lanu. Ndipo palibenso vuto ngati makolo anu atafuna kudziwa kuti mukucheza ndi anthu otani ndiponso zimene mumachita nawo limodzi. Makolo anu angaone kuti kuchita zimenezi ndi udindo wawo. Koma inuyo mungaganize kuti makolo anuwo akukukaikirani mopitirira malire. Mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Amy, anati: “Sindisangalala kuti makolo anga azibwera mphindi 10 zilizonse kudzaona kuti ndikuchita chiyani pa foni kapena pa Intaneti. Ndimafuna kuti asamandisokoneze ndikamalankhula kapena kulemberana uthenga ndi anzanga.”

Zimene mungachite. Musalole kuti zimene mumachita ndi anzanu zikudanitseni ndi makolo anu. Muziyesetsa kutsatira mfundo zotsatirazi.

● Onetsetsani kuti mwauza makolo anu za anthu amene mumacheza nawo ndipo konzani zoti adziwane nawo. Ngati makolo anu sakuwadziwa bwino anthu amene mumacheza nawo, kodi mungawaimbe mlandu ngati iwo amafufuza okha kuti adziwe anthu amene mumacheza nawowo? Makolo anu amadziwa kuti anthu amene mumacheza nawo angakuchititseni kuti mukhale munthu wabwino kapena woipa. (1 Akorinto 15:33) Ngati makolo anu atawadziwa bwino anthu amene mumacheza nawo, iwo sangade nanu nkhawa.

● Lankhulani ndi makolo anu mwaulemu zokhudza anzanu. Musawadzudzule kuti akulowerera kwambiri m’nkhani zanu. M’malomwake, auzeni kuti, “Ndikuona kuti chilichonse chimene ndikukambirana ndi anzanga mumachifufuza n’kumandiimba nacho mlandu. Choncho, ineyo ndikumalephera kucheza ndi anzanga momasuka.” Mwina zimenezi zingathandize kuti makolo anu azikupatsani mpata wocheza ndi anzanu popanda kufufuza kuti mukukambirana zinthu zotani.—Miyambo 16:23.

● Ganizirani mofatsa: Kodi nkhani imene mukuwabisirayo ndi yachinsinsidi kapena mukungoopa kuti atulukira zinthu zina zoipa zimene mukuchita? Mtsikana wina wazaka 22, dzina lake Brittany, anati: “Ngati mukukhala ndi makolo anu ndipo iwo akukuderani nkhawa, muyenera kudzifunsa kuti, ‘Ngati sindikuchita zoipa, kodi pali chifukwa chilichonse chobisira zimene ndikuchita?’ Koma ngati mukuwabisira zimene mukuchita ndi anzanu, ndiye kuti pali zinazake zokaikitsa zimene mukuchita.”

Zoti muchite. Lembani m’munsimu zinthu zimene munganene kuti muyambe kukambirana ndi makolo anu za nkhaniyi.

․․․․․

Kodi mukufunikiradi kukhala nokha?

Tsopano ganizirani mfundo zimene mungatsatire kuti muzichita zinthu zina panokha.

Mfundo yoyamba: Ganizirani zinthu zimene mumafuna kuti pochita wina asakusokonezeni.

Kodi mukuona kuti makolo anu ayenera kukusiyani nokha pa zinthu ziti?

․․․․․

Mfundo yachiwiri: Ganizirani mmene makolo anu akuonera nkhaniyi.

Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chimawadetsa nkhawa?

․․․․․

Mfundo yachitatu: Ganizirani mmene mungathetsere vutolo.

(a) Ganizirani chimene chikuchititsa vutolo ndipo lembani m’munsimu.

․․․․․

(b) Kodi mungachite chiyani kuti muthetse vutolo?

․․․․․

(c) Kodi mukufuna kuti makolo anu achite chiyani kuti akuthandizeni pa nkhaniyi?

․․․․․

Mfundo yachinayi: Kambiranani.

Panthawi yoyenera kambiranani ndi makolo anu zimene mwalemba pamwambazi.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Mayina ena mu nkhaniyi asinthidwa.

^ ndime 21 Koma ngati makolo anu sakukukhulupiriranibe, auzeni modekha ndiponso mwaulemu mmene mukumvera. Mvetserani madandaulo awo, ndipo onetsetsani kuti palibe chilichonse chimene mukuchita chomwe chingachititse kuti azikukaikirani.—Yakobe 1:19.

ZOTI MUGANIZIRE

● N’chifukwa chiyani makolo anu ali ndi ufulu wodziwa zimene mukuchita?

● Kodi kuyesetsa kuti muzilankhulana bwino ndi makolo anu kungakuthandizeni bwanji kuti muzidzatha kulankhulana bwino ndi anthu ena m’tsogolo?

[Bokosi/Zithunzi patsamba 19]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

“Ngati achinyamata sabisira makolo awo zimene akuchita, makolowo salimbana n’kuona mauthenga amene ali mu foni kapena m’kompyuta yawo.”

“Sindingakhumudwe ngati makolo atawerenga uthenga wanga. Ngati mabwana amawerenga uthenga umene antchito awo alandira pakompyuta, kuli bwanji makolo anga?”

“Makolo safuna kuti mwana wawo akumane ndi mavuto, ndipo chifukwa cha zimenezi nthawi zina angachite zinthu zomwe mungaone ngati akupitirira malire awo. Zimenezi zingaoneke ngati si zabwino, koma kunena zoona, ndimaona kuti inenso nditakhala kholo, ndingamachite zomwezo.”

[Zithunzi]

Eden

Kevin

Alana

[Bokosi patsamba 21]

MAWU KWA MAKOLO

● Ngati mwana wanu wamwamuna ali m’chipinda chake, kodi mungangofikira kulowa osagogoda?

● Ngati mwana wanu wamkazi waiwala foni yake pothamangira kusukulu, kodi mungaitenge n’kuyamba kuona mauthenga amene ali mufonimo?

Mafunso amenewa ndi ovuta kuyankha. N’zoona kuti muli ndi ufulu wodziwa zimene mwana wanu akuchita komanso udindo womuteteza. Koma kodi ndi bwino kuti muzifufuza chilichonse chimene iye akuchita? Ndiye kodi mungatani kuti muzichita zinthu moyenerera?

Choyamba, dziwani kuti ngati mwana wanu akubisa zinthu zina kapena ngati akumafuna kukhala yekha, nthawi zina sizitanthauza kuti iye walowerera. Nthawi zambiri n’zimene zimachitika ana akamakula. Kusiya mwana wanu kuti azichita zinthu zina payekha kungamuthandize kuti azisankha anthu ocheza nawo mwanzeru ndiponso azitha kuthana ndi mavuto payekha pogwiritsa ntchito “luntha la kulingalira.” (Aroma 12:1, 2) Zingamuthandizenso kuti azitha kuganiza bwino, ndipo zimenezi zingadzamuthandize kwambiri atakula. (1 Akorinto 13:11) Komanso zingamuthandize kuti aziganiza mozama ngati atafunsidwa mafunso ovuta kwambiri.—Miyambo 15:28.

Chachiwiri, dziwani kuti ngati mumafuna kuti muzingolamulira mwana wanu pa chilichonse, iye angadane anu ndipo angasiye kumvera malamulo anu. (Aefeso 6:4; Akolose 3:21) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kungomusiyiratu mwana wanu kuti azichita zonse payekha? Ayi, chifukwa inuyo ndi kholo lake basi. Komabe, cholinga chosiyira mwana wanu kuti azichita zina ndi zina payekha ndi chakuti azitha kusiyanitsa chabwino ndi choipa. (Deuteronomo 6:6, 7; Miyambo 22:6) Koma kulangiza mwana wanu n’kofunika kwambiri kuposa kum’londalonda.

Chachitatu, kambiranani nkhaniyo ndi mwana wanu. Mvetserani pamene akukufotokozerani mavuto ake. Mungachite bwino kukhala munthu wololera nthawi zina. (Afilipi 4:5) Mwana wanu ayenera kudziwa kuti ali ndi ufulu wochita zinthu zina payekha, malinga ngati akusonyeza kuti ndi wodalirika. Muyenera kumuuza chilango chimene mungamupatse ngati atachita zinthu zimene simugwirizana nazo, ndipo mudziperekadi chilangocho. Dziwani kuti n’zotheka kumulola mwana wanu kuchita zinthu zina payekha, popanda kunyalanyaza udindo wanu monga kholo.

[Chithunzi patsamba 20]

Mufunika kuyesetsa kuti makolo anu azikudalirani chifukwa munthu salandira malipiro asanagwire ntchito