Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

TV Yoyamba

TV Yoyamba

TV Yoyamba

ANTHU atayamba kuulutsa mawu pa wailesi, akatswiri ena anaona kuti n’zothekanso kumaonetsa zithunzi za anthu amene akulankhulawo. Koma kuchita zimenezi kunali kovuta. Tangoganizirani ntchito imene imakhalapo kuti zithunzi zioneke pa TV.

Choyamba, kamera ya TV imaloza ku chinthu chimene mukufuna kujambula. Ndipo chinthucho chimatumizidwa ku kachipangizo kenakake kamene kamatha kuzindikira chinthucho. Posintha chinthucho, kachipangizoka sikaunika chinthu chonsecho nthawi imodzi koma kamaunika timadontho ting’onoting’ono timene timapanga chinthucho. Chinthucho chikafika kumene chikupita, TV ya m’nyumba imachisintha kuti chikhale mmene chinalili poyamba ndipo timatha kuchiona.

Akuti munthu amene anapanga TV yoyamba anali John Logie Baird, wa ku Scotland. Poyamba mkuluyu ankagwira ntchito za magetsi koma kenako anasiya chifukwa cha kudwala. Zitatero, anaganiza zopanga makina otha kusonyeza zithunzi. Maganizo amenewa anali nawo kuyambira ali mnyamata.

Kamera ya TV imene Baird anagwiritsa ntchito inali ndi disiki yokhala ndi mabowo okwana 30 amene anabowoledwa mozungulira kuchokera pakati pa disikiyo. Disikiyo ikamazungulira, mabowowo ankapangitsa kuti chithunzicho chikhale ndi mizeremizere. Ndipo kenako chithunzicho chinkatumizidwa pa sikilini. Chithunzicho chikafika pa sikilini, chinkasintha n’kuyamba kuoneka mmene chinalili poyamba. Koma chomwe chinatsala n’chakuti madisikiwo azizungulira nthawi imodzi. Pamene Baird ankagwira ntchito imeneyi, ankapukuta nsapato za anthu kuti azipeza ndalama.

Pa October 2, 1925, iye anakwanitsa kuonetsa koyamba zithunzi za pa TV kuchokera m’chipinda cha pamwamba pa nyumba yake kupita m’chipinda china. Munthu woyamba kuoneka pa TV imeneyi anali mnyamata wina yemwe ankagwira ntchito mu ofesi pansi pa nyumba ya Baird. Iye anapatsidwa ndalama zokwana mashiling’i awiri ndi theka ngati malipiro ake. Mu 1928, Baird anasonyeza zithunzi za pa TV m’mayiko ena. John Baird atafika ku New York, analandiridwa ndi anthu amene ankaimba zitoliro. Koma popeza kuti iye ankaona kuti sakuyenera ulemu umenewu, anali ndi manyazi kwambiri. Iye anatchuka kwambiri chifukwa chopanga TV. Koma kodi Baird anatenga kuti nzeru zimenezi?