Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zipangizo Zolozera Malo

Zipangizo Zolozera Malo

Zipangizo Zolozera Malo

MUYENERA kuti mukudziwa mmene zimavutira kuyenda m’dera lachilendo chifukwa mukhoza kusochera. Nanga kodi anthu amene amayenda panyanja amatani kuti asasochere? Kungokhala ndi kampasi yokha si kokwanira kuti munthu amene akuyenda panyanja akafike kumene akupita. Iye ayenera kudziwa malo omwe ali ndiponso kumene akulowera. M’zaka za m’ma 1730, kusanabwere zipangizo zolozera malo zamakono, zinali zovuta kuti anthu oyenda panyanja adziwe bwinobwino malo omwe ali ndiponso mmene angayendere kuti akafike kumene akupita. Iwo ankagwiritsa ntchito mapu ndipo zinkawatengera maola ambiri akuwerengera mmene ayendere.

Masiku ano anthu apaulendo amagwiritsa ntchito kachipangizo kolozera malo komwe si kokwera mtengo kwenikweni, kotchedwa GPS (Global Positioning System). Kuti mugwiritse ntchito kachipangizo kameneka, mumangolemba dzina la malo amene mukupitawo. Ndipo kachipangizoka kamasonyeza malo omwe muli ndiponso kumene mukupita. Kodi kachipangizo kameneka kamadalira chiyani kuti kagwire bwino ntchito?

Kachipangizoka kamadalira masetilaiti omwe amakhalapo pafupifupi 30. Setilaiti iliyonse imatumiza uthenga wosonyeza kumene ili ndiponso mmene nthawi ilili kumeneko. Kachipangizo kanuko kakangolumikizana ndi masetilaiti angapo, kamakulozerani malo amene mukufuna kupita. Koma pamagona masamu kuti kachite zimenezi. M’masekondi ochepa chabe, kamawerengetsa mtunda umene ulipo kukafika ku masetilaiti atatu, omwe amakhala kutali kwambiri komanso motalikirana.

Pulofesa Bradford Parkinson ndi Pulofesa Ivan Getting anali anthu oyamba kupanga GPS chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1960. Ngakhale kuti poyamba kachipangizoka kanapangidwa kuti kazithandiza asilikali, kanayamba kugwiritsidwanso ntchito ndi anthu wamba mu 1996. Kachipangizo kolozera malo kameneka kakusonyeza kuti luso la zopangapanga lapita patsogolo kwambiri. Koma kodi ndi kachipangizo koyambadi kolozera malo?

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

Globe: Based on NASA photo