Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chiyani Chimachititsa Munthu Kukhala Wabwino Kapena Woipa?

Kodi N’chiyani Chimachititsa Munthu Kukhala Wabwino Kapena Woipa?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi N’chiyani Chimachititsa Munthu Kukhala Wabwino Kapena Woipa?

KUYAMBIRA kalekale anthu akhala akudana komanso kuphana. Komabe, ngakhale kuti anthu ena amachita zankhanza, pali anthu enanso omwe ndi achifundo komanso amadzipereka kuti athandize ena. Kodi chimachititsa n’chiyani kuti munthu wina azipha anthu mopanda chisoni pamene wina azichita zinthu zabwino kwambiri zothandiza ena? Kodi n’chiyani chimachititsa kuti anthu nthawi zina azichita zinthu zankhanza ngati zinyama?

Ndi Nkhani ya Kupanda Ungwiro Ndiponso Chikumbumtima

Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Maganizo a anthu amakhala oipa kuyambira pa ubwana wawo.” (Genesis 8:21, NW) Ichi n’chifukwa chake ana amakonda kuchita zopulupudza. (Miyambo 22:15) Ndipotu mtima umenewu timachita kubadwa nawo. (Salmo 51:5) Kuti tichite zabwino, timafunika kuchita khama kwambiri.

Komabe, anthufe tinapatsidwa chikumbumtima chimene chimatithandiza kudziwa zinthu zabwino ndi zoipa moti timatha kuchita zinthu zimene anthu ambiri angaone kuti ndi zabwino. Choncho, ngakhale anthu amene sanaphunzitsidwe makhalidwe abwino, amatha kuchita zinthu zabwino. (Aroma 2:14, 15) Komabe, nthawi zina mtima wathu umagawanika, mbali ina umafuna kuchita zabwino ndipo mbali ina umafuna kuchita zoipa. Koma pali chinthu chinanso chimene chimachititsa kuti tizifuna kuchita zabwino kapena zoipa.

Kutengera Makhalidwe a Ena

Bilimankhwe amasintha mtundu wake kuti agwirizane ndi malo amene wakhala. N’chimodzimodzinso anthu amene amasankha kucheza ndi anthu oipa, nawonso amatengera makhalidwe oipawo. Baibulo limachenjeza kuti: “Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa.” (Eksodo 23:2) Koma kukonda kucheza ndi anthu amene amakonda kunena zoona, achilungamo ndiponso amakhalidwe abwino, kumathandiza munthu kuti azichita zabwino.—Miyambo 13:20.

Komabe, ngakhale munthu amene sacheza ndi anthu olakwika angathe kukhala ndi makhalidwe oipa chifukwa chopanda ungwiro. Kupanda ungwiro kungatichititse kuti tiziganiza zinthu zoipa mumtima mwathu, ngakhalenso kuzichita kumene ngati mpata utapezeka. (Genesis 4:7) Ndiponso tikhoza kuchita zinthu zoipa chifukwa cha zinthu zimene timaonera, kumvetsera kapena kuwerenga. Masewera a pakompyuta ndiponso mafilimu nthawi zambiri amalimbikitsa chiwawa ndiponso mtima wobwezera. Komanso kumva kawirikawiri nkhani zoipa zochitika m’dziko mwathu kapena kumaiko ena kungatichititse kuti tisamamvere chisoni anthu.

N’chiyani chimachititsa mavuto onsewa? Baibulo limanena kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Woipa amene akunenedwa palembali ndi Satana Mdyerekezi, ndipo Malemba amati iye ndi wabodza ndiponso wopha anthu. (Yohane 8:44) Iye amalimbikitsa zinthu zoipa pogwiritsa ntchito zochitika za m’dzikoli.

Anthu ena amaganiza kuti palibe chifukwa chowaimbira mlandu pa zoipa zimene amachita chifukwa chakuti pali zinthu zambiri zimene zimawachititsa kuti azichita zoipazo. Koma kodi zimenezi ndi zoona? Ayi. Zoganiza zathu n’zimene zimatipangitsa kuti tichite zoipa. Zili ngati galimoto, nthawi zambiri galimoto imalowera kumene timaikhotetsera.

Timachita Kusankha Kukhala Abwino Kapena Oipa

Tisanachite chinthu chilichonse chabwino kapena choipa, timayamba taganiza kaye. Tikabzala zinthu zabwino mumtima mwathu, timakololanso zabwino. Koma tikamakonda kufesa zinthu zoipa mumtima mwathu, zotsatira zake zimakhala kuchita zinthu zambiri zoipa. (Luka 6:43-45; Yakobe 1:14, 15) Choncho, tikhoza kunena kuti timachita kusankha kukhala munthu wabwino kapena woipa.

Koma n’zosangalatsa kuti Baibulo limanena kuti tikhoza kuphunzira kuchita zabwino. (Yesaya 1:16, 17) Chikondi n’chimene chingatilimbikitse kuchita zabwino chifukwa “chikondi sichikuchititsa zoipa kwa mnansi wako.” (Aroma 13:10) Tikamakonda anthu anzathu, sitingaganize zowachitira zoipa.

Zimenezi n’zimene Ray, yemwe amakhala ku Pennsylvania, m’dziko la United States, anazindikira. Kuyambira ali mwana, Ray anaphunzitsidwa ndewu moti anthu ankangomutchula kuti Chilombo. Ngakhale kuti nthawi zina zinkamuvata kuugwira mtima, atayamba kuphunzira Baibulo anayamba kusintha pang’ono ndi pang’ono. Komabe nthawi zina zinkamuvuta kuugwira mtima. Paulo ankamvanso chimodzimodzi ndipo analemba kuti: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili nane.” (Aroma 7:21) Panopa, pambuyo poyesetsa zaka zambiri, Ray amatha “kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.”—Aroma 12:21.

Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa ‘kuyenda m’njira ya anthu abwino’? (Miyambo 2:20-22) Chifukwa chakuti anthu oipa adzawonongedwa. Baibulo limati: “Ochita zoipa adzadulidwa . . . Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:9-11) Mulungu adzawononga anthu onse oipa. Choncho tiyeni tiziyesetsa kwambiri kuchita zabwino chifukwa tikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi n’chifukwa chiyani anthu amachita zinthu zoipa?—Yakobe 1:14.

● Kodi n’zotheka kusintha n’kuyamba kuchita zabwino?—Yesaya 1:16, 17.

● Kodi zinthu zoipa zidzatha?—Salmo 37:9, 10; Miyambo 2:20-22.

[Zithunzi patsamba 21]

Munthu amachita kusankha kuchita zabwino kapena zoipa