Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mlomo wa Nankapakapa

Mlomo wa Nankapakapa

Panagona Luso!

Mlomo wa Nankapakapa

● Imodzi mwa sitima zothamanga kwambiri padziko lonse imapezeka ku Japan ndipo imathamanga makilomita 300 pa ola limodzi. Koma popanga sitimayi anabera nzeru zina kuchokera kwa mbalame yaing’ono yotchedwa nankapakapa.

Taganizirani izi: Mbalameyi ikaona nsomba m’madzi imadumphiramo ikuthamanga kwambiri popanda kuvundula madzi. Katswiri wina wopanga sitima, dzina lake Eiji Nakatsu, anachita chidwi kwambiri ndi mbalameyi. Iye anafuna kudziwa chimene chimachititsa kuti mbalameyi izilowa m’madzi mwakachetechete. Atadziwa zimene zimachititsa zimenezi, iye anakwanitsa kupanga sitima yothamanga kwambiri. Nakatsu anati: “Sitima ikamadutsa mumsewu wa pansi pa nthaka ikuthamanga kwambiri, mumsewumo mumayamba kuwomba chimphepo chachikulu. M’kupita kwanthawi chimphepochi chimapanga phokoso.”

Choncho, iwo anaganiza zopanga sitima imene kutsogolo kwake kunali kooneka ngati mlomo wa nankapakapa. Kodi zimenezi zinathandiza? Inde, chifukwa anayamba kupanga sitima yothamanga kwambiri komanso yosadya mafuta kuposa imene ankapanga poyamba. Izi zili chonchi chifukwa sitimayi siwombana ndi mphepo yambiri ikamayenda. Ndipo sitimayi ikamadutsa mumsewu wa pansi pa nthaka, simapanga phokoso.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi mlomo wa nankapakapa unachita kupangidwa ndi Mlengi kapena unakhalapo mwangozi?

[Mawu a Chithunzi patsamba 29]

Kingfisher diving: Woodfall/Photoshot; bullet train: AP Photo/Kyodo