Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“M’chaka cha 2008, ndalama zimene asilikali anagwiritsa ntchito padziko lonse zinakwana pafupifupi madola 1464 biliyoni. Zimenezi zikutanthauza kuti ndalama zimene zinagwiritsidwa ntchito pazinthu zokhudzana ndi nkhondo zinawonjezeka ndi 45 peresenti kuchokera m’chaka cha 1999.”—STOCKHOLM INTERNATIONAL PEACE RESEARCH INSTITUTE, SWEDEN.

“Malinga ndi lipoti limene kampani ya Google inatulutsa, anthu akukhazikitsa malo a pa Intaneti mabiliyoni ambiri tsiku lililonse.—NEW SCIENTIST, BRITAIN.

“Chiwerengero cha anthu amene [ankayembekezereka] kugona ndi njala tsiku lililonse padziko lonse m’chaka cha 2009 [chinali] chachikulu kwambiri kuposa zaka zina, mwina chimakwana 1 020 miliyoni patsiku.—FOOD AND AGRICULTURE ORGANIZATION OF THE UNITED NATIONS, ITALY.

Ngamila Yoyamba Kupangidwa ndi Asayansi

M’chaka cha 1996, akatswiri ochita kafukufuku anapanga nkhosa pogwiritsa ntchito njira zasayansi. Kuchokera m’chaka chimenechi, akatswiriwa akwanitsa kupanga nyama zosiyanasiyana monga ng’ombe, mbuzi ndi hatchi. Koma posachedwapa, akatswiri a nyama ku Dubai akwanitsa kupanga ngamila pogwiritsa ntchito njira zasayansi. Ngamilayi inali yaikazi ndipo anaipatsa dzina la Chiarabu lakuti Injazi, lomwe limatanthauza “Chipambano.” Nyuzipepala ya ku Abu Dhabi ya The National inati: “Takhala tikupanga nyama pogwiritsa ntchito njira zasayansi pofuna kuyeserera chabe. Koma tsopano tiyamba kupanga ngamila zothamanga kwambiri ndiponso zopereka mkaka wambiri.”

Kuwombana kwa masetilaiti

Magazini ya Science News inati: “Kwa zaka zambiri, m’njira zimene masetilaiti amadutsa m’mlengalenga mwakhala mukuchuluka zinthu zoyendamo, koma vutoli linakula kwambiri pamene masetilaiti awiri anawombana mu February [2009].” Ngoziyi inachitikira m’mlengalenga, pafupifupi makilomita 800 kuchoka pansi, m’dziko la Siberia. Panthawiyi setilaiti ya ku America inawombana ndi setilaiti ya dziko la Russia, yomwe poyamba ankaigwiritsira ntchito pa nkhondo. Ngoziyi inachititsa kuti zidutswa zikuluzikulu zokwana pafupifupi 700 ziziyendayenda m’mlengalenga. Zidutswa zikachuluka m’njira imene masetilaiti amadutsa, n’zosavuta kuti ngozi zizichitika pafupipafupi. Panopa, kwakhazikitsidwa malo amene akuonera mmene tizidutswa tokwana 18,000, tomwe n’tatikulu masentimita 10, tikuyendera m’mlengalenga. Koma vuto ndi lakuti ngati masetilaitiwa atawombana ndi kachidutswa kalikonse kakang’ono koma kothamanga kwambiri, kungachitikebe ngozi yoopsa.

Kuzimitsira Galimoto Angongole

Nyuzipepala ya The Wall Street Journal inati: “Anthu ambiri sanyalanyaza kulipira mabilo a foni zawo chifukwa amadziwa kuti akapanda kulipira awadulira.” Panopa ogulitsa magalimoto akuchitanso zimenezi. Nyuzipepalayi inanena kuti: “Anthu ogulitsa magalimoto ayamba kuika tizipangizo tinatake m’galimoto timene tikuchititsa kuti galimotoyo izilephera kunyamuka ngati wogulayo wachedwetsa kupereka ngongole.” Tizipangizoti, tomwe timaikidwa m’injini, timachotsedwa munthuyo akamaliza kupereka ngongoleyo. Nyuzipepalayi inanenanso kuti, nthawi zambiri anthuwa sazimitsa galimotoyo, koma amangoichititsa kuti iziwala magetsi komanso izichita phokoso “lomukumbutsa munthu wogulayo kuti amalize kupereka ngongole yake.”