Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikondi cha Mpeni Kumphasa

Chikondi cha Mpeni Kumphasa

Chikondi cha Mpeni Kumphasa

Tiyerekezere kuti muli ndi mnzanu amene munadziwana naye kuyambira muli mwana. Iye ankakuthandizani kuchita zinthu ngati munthu wamkulu komanso kuti muzigwirizana ndi anzanu ena. Mukakhala ndi nkhawa, munkangopita kwa iye kuti akuthandizeni ndipo munafika pomudalira pa zinthu zambiri.

Koma patapita nthawi munazindikira kuti mnzanuyo si wabwino. Iye amakukakamirani kuti muziyenda naye kulikonse, ngakhale kumalo amene simungamasuke kupita naye. Ndipo ngakhale kuti nthawi zina munkaona kuti amakuthandizani kuchita zinthu mochangamuka, iye wakuwonongerani thanzi lanu. Kuwonjezera pamenepo, iye wakhalanso akukuberani ndalama zanu.

M’zaka zaposachedwapa, mwakhala mukuyesetsa kuti musiye kucheza naye koma iye akukukakamiranibe. Inuyo mwafika pokhala kapolo wake ndipo mumadandaula kuti zinalakwika kudziwana naye.

FODYA ali ngati bwenzi lotereli kwa anthu ambiri amene amasuta. Mayi wina dzina lake Earline, yemwe anakhala akusuta fodya kwa zaka 50, ananena kuti: “Ndinkaona kuti kusuta fodya n’kothandiza kwambiri. Fodya anafika pokhala ngati mnzanga wapamtima ndipo nthawi zambiri ndikasowa wocheza naye ndinkangoyamba kusuta.” Koma kenako Earline anazindikira kuti fodya ndi woipa komanso woopsa kwambiri. Akanapanda kusiya, bwenzi mawu oyambirira a nkhaniyi akunena za iyeyo. Iye anasiya atadziwa kuti Mulungu sasangalala ndi anthu amene amasuta fodya, chifukwa fodya amawononga thupi limene Iye anatipatsa.—2 Akorinto 7:1.

Bambo wina dzina lake Frank anasiya kusuta n’cholinga choti asangalatse Mulungu. Koma patangopita tsiku limodzi kuchokera pamene anasiya, anapezeka kuti akukwawa m’nyumba mwake n’kumafufuza tindudu totsalira. Frank anati: “Nditaona kuti ndafika pomakwawa pansi n’kumatoleza tindudu ta fodya, ndinadzimvera chisoni kwambiri ndipo ndinaganiza zosiyiratu kusuta fodya. Kuchokera tsiku limenelo sindinasutenso fodya.”

Kodi n’chifukwa chiyani fodya amavuta kusiya? Akatswiri ofufuza apeza kuti zinthu zotsatirazi n’zimene zimachititsa kuti anthu azivutika kusiya kusuta fodya: (1) Fodya amamulowerera munthu ngati mmene mankhwala osokoneza bongo amachitira. (2) Mu fodya muli mankhwala otchedwa nikotini omwe amafika ku ubongo m’masekondi 7 okha kuchokera pamene munthu wasuta. (3) Munthu ukamasuta fodya thupi limazolowera monga mmene limachitira ndi kudya chakudya, kumwa, kulankhula, ndi zina zotero.

Komabe, monga mmene zinalili ndi Earline ndiponso Frank, n’zotheka kusiya chizolowezi chimenechi. Ngati inuyo mumasuta ndipo mukufuna kusiya, nkhani yotsatirayi ikuthandizani kuti muyambe moyo watsopano.