Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Wotsimikiza

Khalani Wotsimikiza

Khalani Wotsimikiza

“Anthu amene amatsimikiza mumtima mwawo kuti sadzasutanso fodya ndi amene amasiyadi kusuta.”—Linatero buku lakuti “Stop Smoking Now!”

NGATI mukufuna kusiya kusuta, choyamba muyenera kutsimikiza kuti mukufuna kusiyadi kusuta fodya. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuchita zimenezi? Muyenera kuganizira za phindu limene mungapeze ngati mutasiya kusuta.

Simumawononga ndalama. Kusuta ngakhale paketi imodzi patsiku, kungakuwonongereni ndalama zambiri pachaka. Gyanu, yemwe amakhala ku Nepal, anati: “Ndinadabwa kwambiri nditawerengetsa ndalama zimene ndimawononga pogula fodya.”

Mumakhala ndi moyo wosangalala. Regina yemwe amakhala ku South Africa, anati: “Nditasiya kusuta fodya, ndinayamba kukhala ndi moyo wosangalala tsiku lililonse.” Munthu amene ankasuta fodya akasiya, amayamba kumva kukoma kwa chakudya, amakhala ndi mphamvu zambiri, ndiponso amayamba kuoneka bwino.

Mumakhala ndi thanzi labwino. “Munthu amene poyamba ankasuta fodya akangosiya kusuta, amayamba kukhala ndi thanzi labwino kwambiri. Zimenezi zimachitikira anthu amisinkhu yonse komanso aamuna kapena aakazi.”—Linatero bungwe la U.S. Centers for Disease Control and Prevention.

Mumachita zinthu modzidalira. “Ndinasiya kusuta chifukwa chakuti sindinkafuna kuti ndikhale kapolo wa fodya. Sindinkafuna ngakhale pang’ono kukhala kapolo wa chinthu chilichonse.”—Anatero Henning, wa ku Denmark.

Anzanu ndi achibale anu amatetezeka ku matenda. “Utsi umene anthu osuta fodya amatulutsa umayambitsa matenda osiyanasiyana kwa anthu omwe sasuta. . . . Kafukufuku akusonyeza kuti utsi wa fodya umayambitsa matenda a khansa ya m’mapapo komanso matenda a mtima, omwe amapha anthu masauzande ambiri chaka chilichonse.”—Linatero bungwe la American Cancer Society.

Mumasangalatsa Mlengi. Baibulo limati: “Okondedwanu, tiyeni tidziyeretse kuchotsa chilichonse choipitsa cha thupi.” (2 Akorinto 7:1) Limanenanso kuti: “Mupereke matupi anu nsembe . . . yoyera, yovomerezeka kwa Mulungu.”—Aroma 12:1.

“Ndinasiya kusuta fodya nditangodziwa kuti Mulungu sasangalala ndi zinthu zimene zimawononga thupi.”—Anatero Sylvia, wa ku Spain.

Komabe, nthawi zina kungokhala wotsimikiza sikokwanira. Mufunikiranso kuthandizidwa ndi anthu ena, kuphatikizapo achibale ndiponso anzanu. Koma kodi iwo angatani kuti akuthandizeni?