Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamadziderere?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamadziderere?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamadziderere?

INDE AYI

Kodi mukadziyang’ana pa galasi, ◯ ◯

mumasangalala ndi mmene

mukuonekera?

Kodi mumaona kuti muli ndi ◯ ◯

luso linalake lofunika kwambiri?

Kodi mumatha kukana anzanu ◯ ◯

akakuuzani kuti muchite zinthu

zimene mukuona kuti n’zolakwika?

Kodi anthu akakudzudzulani ◯ ◯

pazifukwa zomveka mumayesetsa

kuti musakhumudwe?

Kodi anthu ena akamakunyozani ◯ ◯

mumatha kupirira?

Kodi mumaona kuti anthu ◯ ◯

amakukondani?

Kodi mumasamalira thanzi lanu?

Kodi mumasangalala anthu ena ◯ ◯

akachita bwino zinthu zinazake?

Kodi mumaona kuti zinthu ◯ ◯

zimakuyenderani pa moyo wanu?

Ngati mwachonga bokosi lakuti ‘Ayi,’ pa ambiri mwa mafunso omwe ali pamwambawa, ndiye kuti mumadziderera ndipo maganizo amenewa angakulepheretseni kuona zinthu zimene mumachita bwino. Nkhaniyi ikuthandizani kuganizira zinthu zimene mumachita bwino.

ACHINYAMATA ambiri amakhala ndi maganizo akuti saoneka bwino, ndi olephera ndiponso anzawo amawaposa pa zinthu zambiri. Kodi inunso mumaganiza choncho? Tamvani zimene achinyamata ena ananena.

“Nthawi zambiri ndikalakwitsa ndimakhumudwa kwambiri ndipo ndimadziona kuti ndine wolephera.”—Anatero Leticia. *

“Ngakhale utakhala wooneka bwino bwanji, umakumanabe ndi anthu ena ooneka bwino kuposa iweyo.”—Anatero Haley.

“Ndimachita manyazi kwambiri ndikakhala pagulu. Ndimaganiza kuti aliyense akuona kuti ndine wachabechabe.”—Anatero Rachel.

Ngati inunso muli ndi maganizo amenewa, musadandaule. Pali zimene mungachite kuti vuto lanulo lithe. Zinthu zitatu zotsatirazi zingakuthandizeni.

1. Muzicheza ndi Anthu Odalirika

Lemba lofunika. “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo m’bale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.”—Miyambo 17:17.

Tanthauzo lake. Mnzanu wodalirika angakuthandizeni kwambiri panthawi yamavuto. (1 Samueli 18:1; 19:2) Ngakhale kungodziwa kuti pali winawake amene amakuderani nkhawa kumalimbikitsa. (1 Akorinto 16:17, 18) Choncho, muzicheza ndi anthu amene angakuthandizeni kuti musamadziderere.

“Anzanu enieni sangakuchititseni kuti muzidziona kuti ndinu wosafunika.”—Anatero Donnell.

“Nthawi zina kungodziwa kuti pali winawake amene amakukonda n’kofunika kwambiri. Zimakuchititsa kudziona kuti ndiwe wofunika.”—Anatero Heather.

Chenjezo: Musamalole kuchita zinthu n’cholinga chongosangalatsa anzanu. (Miyambo 13:20; 18:24; 1 Akorinto 15:33) Kuchita zinthu zolakwika n’cholinga chongosangalatsa anzanu kungapangitse kuti anzanuwo azikudyerani masuku pamutu komanso kuti muzidziona kuti ndinu wachabechabe.—Aroma 6:21.

Zoti muchite. Lembani m’munsimu dzina la mnzanu amene angakuthandizeni kudziona kuti ndinu wofunika.

․․․․․

Mungachite bwino kupeza nthawi yocheza ndi munthu amene mwamutchulayo. Dziwani izi: Munthuyo akhoza kukhala wamkulu kapena wamng’ono kwa inuyo.

2. Muzithandiza Ena

Lemba lofunika. “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.

Tanthauzo lake. Mukamathandiza ena mumakhalanso mukudzithandiza nokha. Baibulo limanena kuti: “Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.” (Miyambo 11:25) Imeneyi ndi mfundo yosatsutsika. Mukamathandiza ena mumakhala wosangalala kwambiri. *

“Ndimaganizira zinthu zabwino zimene ndingachitire ena ndipo ngati munthu wina mumpingo wakumana ndi vuto ndimayesetsa kumuthandiza. Kukonda anthu ndiponso kuwathandiza kumandichititsa kuti ndizikhala wosangalala.”—Anatero Breanna.

“Ntchito yolalikira ndi yabwino kwambiri chifukwa imathandiza kuti munthu uziganizira kwambiri ena m’malo momangoganizira za iweyo.”—Anatero Javon.

Chenjezo: Musamathandize ena n’cholinga choti mupeze phindu. (Mateyo 6:2-4) Kuthandiza ena n’cholinga cholakwika n’kopanda phindu. Nthawi zambiri ena amadziwa kuti mwachita zimenezo n’cholinga choti mupeze kenakake.—1 Atesalonika 2:5, 6.

Zoti muchite. Ganizirani munthu winawake amene munamuthandizapo m’mbuyomu. Kodi dzina lake ndani, ndipo munamuchitira chiyani?

․․․․․

Mutachita zimenezi, munamva bwanji?

․․․․․

Ganiziraninso munthu wina amene mungamuthandize ndipo lembani mmene mungamuthandizire.

․․․․․

3. Mukalakwitsa Musamadandaule Kwambiri

Lemba lofunika. “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 3:23.

Tanthauzo lake. Simungalephere kulakwitsa zina ndi zina chifukwa ndinu wopanda ungwiro. Nthawi zina mukhoza kunena kapena kuchita zinthu zolakwika. (Aroma 7:21-23; Yakobe 3:2) Choncho mukalakwitsa musamadandaule kwambiri. Baibulo limati: “Wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso.”—Miyambo 24:16.

“Nthawi zina timadziona kuti ndife osafunika chifukwa chodziyerekezera ndi ena.”—Anatero Kevin.

“Aliyense amachita zinthu zina zabwino, zina zoipa. Tiyenera kunyadira zabwino zimene timachita ndi kuyesetsa kusintha makhalidwe athu oipa.”—Anatero Lauren.

Chenjezo: Nthawi zonse mukalakwitsa, musamanamizire kuti mwachita zimenezo chifukwa cha kupanda ungwiro. (Agalatiya 5:13) Kuchita dala zinthu zoipa kungachititse kuti ubwenzi wanu ndi Yehova Mulungu usokonekere.—Aroma 1:24, 28.

Zoti muchite. Lembani m’munsimu khalidwe limene mukuona kuti mufunika kulisiya.

․․․․․

Lembani deti la lero pafupi ndi khalidwe limene mwalembalo. Fufuzani mfundo zimene zingakuthandizeni kuti musiye khalidwelo ndipo pakatha mwezi umodzi, onani ngati mwasintha.

Ndinu Munthu Wofunika

Baibulo limati: “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” (1 Yohane 3:20) Zimenezi zikutanthauza kuti iye angaone kuti ndinu wofunika kwambiri ngakhale kuti inu simungadzione choncho. Ndiyeno kodi mukuganiza kuti zolakwa zanu zimachititsa Mulungu kukuonani kuti ndinu wosafunika? Taganizirani kuti muli ndi ndalama yapepala yokwana madola 100. Ngati ndalamayo itang’ambika pang’ono, kodi mungaitaye? Ayi. Ngakhale kuti ndalamayo yang’ambika, imakhala yofunikabe.

Ndi mmenenso Mulungu amakuonerani. Iye amayamikira mukamayesetsa kumumvera, ngakhale kuti mungaone ngati zimene mumachitazo n’zosafunika kwenikweni. Baibulo limatitsimikizira kuti “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.”—Aheberi 6:10.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Mayina ena m’nkhaniyi tawasintha.

^ ndime 30 Ngati ndinu wa Mboni za Yehova, taganizirani mmene mumasangalalira mukamauza anthu ena uthenga wa Ufumu.—Yesaya 52:7.

ZOTI MUGANIZIRE

Kodi mungatani ngati mwayamba kudziona kuti ndinu wosafunika chifukwa chakuti

● Anzanu amakunyozani?

● Mumaona kuti anzanu amakuposani pa zinthu zambiri?

● Mumangoganizira zolakwa zanu basi?

[Mawu Otsindika patsamba 27]

“Munthu akhoza kukhala wokongola koma n’kumadziona kuti ndi wosakongola, kapenanso akhoza kukhala wosaoneka bwino kwenikweni koma n’kumadziona kuti ndi wokongola kwambiri. Zimangodalira mmene amaonera zinthu.”—Anatero Alyssa

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

“Ngakhale nyumba yolimba kwambiri imafunika kuikonza nthawi ndi nthawi kuti ipitirize kukhala yolimba. Inenso ndimakumbukira kuti mnzanga wina ankandiuza mawu achikondi, ankandimwetulira komanso ankandikumbatira. Zimenezi zinandithandiza kuti ndisamadziderere.”

“M’malo mochita nsanje ndi makhalidwe abwino amene anthu ena ali nawo, tiziyesetsa kutengera makhalidwe awowo ngati mmene iwonso amachitira.”

[Zithunzi]

Aubrey

Lauren

[Chithunzi patsamba 28]

Ndalama imakhala yofunikabe ngakhale itang’ambika. Inunso ndinu wofunika kwa Mulungu ngakhale kuti mumalakwitsa zinthu zina