Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndizitani Kuti Ndizigwiritsa Ntchito Ndalama Mwanzeru?

Kodi Ndizitani Kuti Ndizigwiritsa Ntchito Ndalama Mwanzeru?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Ndizitani Kuti Ndizigwiritsa Ntchito Ndalama Mwanzeru?

“Ndimapeza ndalama zochepa koma zinthu zofuna ndalamazo ndi zambirimbiri. Nthawi zambiri tulo sitibwera ndikaganizira za udindo wanga wosamalira banja.”—Anatero James.

“Ndikaganizira mmene ndingathetsere mavuto anga, nthawi zambiri ndimasowa pogwira.”—Anatero Sheri.

PANTHAWI ya mavuto a zachuma, anthu ambiri amakonda kunena mawu amenewa. Pofotokoza za mavuto a zachumawa, mkulu wa bungwe loona za anthu apantchito padziko lonse, dzina lake Juan Somavia, anati: “Vuto limeneli likukhudza aliyense padzikoli.”

Kuchotsedwa ntchito mwadzidzidzi kapena kusowa ndalama zogulira zinthu zofunika pabanja panu kungachititse kuti muzida nkhawa kwambiri kapena muziona kuti ndinu wopanda pake. Baibulo limanena kuti panthawi ina Davide ankaona chimodzimodzi. Iye anapemphera kuti: “Masautso a mtima wanga akula: Munditulutse m’zondipsinja.” (Salmo 25:17) Kodi Baibulo limanenapo chilichonse chokhudza nthawi yomwe tikukhalayi? Ndipo kodi mawu anzeru a m’Baibulo angatithandize bwanji kuti tipewe kuda nkhawa kwambiri?

Mfundo Zothandiza Panthawi Yovuta

Baibulo linalosera kuti “m’masiku otsiriza” a dongosolo lino kudzakhala “masautso” ndiponso “idzafika nthawi yovuta.” (2 Timoteyo 3:1; Mateyo 24:8) Mawu amenewa akukwaniritsidwa masiku ano. Komabe, sikuti palibe chiyembekezo, chifukwa Mulungu kudzera m’Baibulo watipatsa mfundo zimene zingatithandize kuti tipirire mavuto a zachuma.

Mwachitsanzo, Baibulo limatithandiza kuti tiziona ndalama moyenera. Lemba la Mlaliki 7:12 limati: “Nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.” Inde, ndalama zikhoza kutithandiza, koma nzeru zochokera kwa Mulungu, zomwe zimapezeka m’Baibulo, n’zimene zingatithandize nthawi zonse. Taganizirani mfundo zina zothandiza zimene zimapezeka m’Baibulo.

Mfundo Zimene Zingatithandize

Muzigwira ntchito molimbika. Baibulo limati: ‘Moyo wa waulesi ukhumba osalandira kanthu; koma moyo wa akhama udzalemera.’ (Miyambo 13:4) Kodi tikuphunzira chiyani palembali? Tiyenera kuyesetsa kukhala oona mtima komanso akhama pa ntchito. Antchito okhulupirika amakondedwa kwambiri ndi mabwana awo ndipo anthu otere savutika kupeza ntchito komanso sachotsedwa ntchito chisawawa.—Aefeso 4:28.

Muziganiza kaye musanagule chilichonse. Yesu anati: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononga, kuti aone ngati alinazo zokwanira kumalizira nsanjayo?” (Luka 14:28) Ngakhale kuti Yesu palembali ankanena za zimene zimafunika kuti munthu akhale wotsatira wake, mfundoyi ndi yothandizanso pogula zinthu. Choncho muyenera kulemba zinthu zimene mukufuna kugula ndiponso mtengo wake.

Musamawonongere ndalama zinthu zolakwika. Kuchita juga, kusuta fodya, kumwa mowa mwauchidakwa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo zimawonongetsa ndalama komanso n’zoipa kwa Mulungu.—Miyambo 23:20, 21; Yesaya 65:11; 2 Akorinto 7:1.

‘Musamakonde kwambiri ndalama.’ Anthu okonda kwambiri ndalama sasangalala kwenikweni ndipo zimene amafuna sizitheka. Nthawi zambiri ‘amadzibweretsera zopweteka zambiri pa thupi pawo.’ (Aheberi 13:5; 1 Timoteyo 6:9, 10) Ndipo chomvetsa chisoni kwambiri n’chakuti amakhala akapolo a ndalama, chifukwa kaya akhale ndi zochuluka bwanji, sakhutira.—Mlaliki 5:10.

Muzikhutira ndi zimene muli nazo. Baibulo limati: “Sitinabwere ndi kanthu m’dziko, ndiponso sitingatulukemo ndi kanthu. Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi nyumba, tidzakhala okhutira ndi zinthu zimenezi.” (1 Timoteyo 6:7, 8) Anthu amene amakhutira ndi zinthu zochepa zimene ali nazo, sada nkhawa kwambiri ngati chuma chayamba kusayenda bwino. Choncho, ndi bwino kuti muzikhutira ndi ndalama zimene mumapeza.—Onani bokosi lomwe lili kumanjaku.

Tonsefe sitidziwa kuti mawa kugwa chiyani. Lemba la Mlaliki 9:11 limati: “Yense angoona zom’gwera m’nthawi mwake.” Choncho, anthu anzeru ‘sadalira chuma chosadalirika, koma amadalira Mulungu’ amene amatsimikizira atumiki ake okhulupirika kuti: ‘“Mulimonse sindidzakusiyani, ngakhale kukutayani konse.”’—1 Timoteyo 6:17; Aheberi 13:5.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Baibulo limati chiyani za nthawi yomwe tikukhalayi?—2 Timoteyo 3:1-5.

● Kodi masiku ano malangizo odalirika angapezeke kuti?—Salmo 19:7.

● Kodi ndingatani kuti ndithandize banja langa kukhala ndi tsogolo labwino?—Mlaliki 7:12.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 19]

NJIRA ZOTHANDIZA KUTI MUSAMAWONONGE NDALAMA

Kugula zinthu: Lembani zimene mukufuna kugula. Musamagule chinthu chifukwa chakuti mwachiona. Muzifufuza zinthu zotchipirako. Muzigula zinthu zimene azitchipitsa ndiponso panthawi imene anthu ambiri sakuzifuna. Ngati n’kotheka, muziguliratu zinthu zambiri nthawi imodzi.

Kusamala ndalama panyumba: Muzilipira mabilu panthawi yake kuti muzipewa kulipira chindapusa. M’malo mogula chakudya chophikaphika, muziphika nokha ndipo musamadye mowononga. Muzipewa kumwa kwambiri mowa. Muzithimitsa magetsi komanso zipangizo zamagetsi mukamaliza kugwiritsa ntchito. Ngati n’kotheka, muzigwiritsa ntchito zipangizo zosadya magetsi ambiri. Ngati mumakhala m’nyumba yaikulu, mungachite bwino kusamuka n’kumakakhala nyumba yocheperapo.

Mayendedwe: Ngati mukufuna kugula galimoto, muyenera kupeza yodalirika ndiponso yosamwa mafuta ambiri. Mukayenda ulendo, muzikachitiratu ntchito zingapo komwe mwapitako, ndiponso mukhoza kugwirizana ndi anzanu amene ali ndi galimoto kuti mugwiritse ntchito galimoto imodzi. Apo ayi, muzikwera basi, kuyenda pansi kapena kuyenda panjinga. Musamakonde kupita kutchuthi panthawi imene anthu ambiri ali patchuthi chifukwa panthawi imeneyi zinthu zimadula.

Foni ndi TV: Kodi mukufunikiradi kukhala ndi foni yam’nyumba komanso yam’manja? Ngati ana anu ali ndi mafoni am’manja, kodi zingatheke kuwagulitsa kapena kungochepetsa kuimba? Ngati muli ndi TV, kodi zingatheke kukhala ndi matchanelo ochepa kuti musamalipire ndalama zambiri? * Muzibwereka mabuku ndi mafilimu ku malaibulale m’malo mogula nokha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 26 Mukafuna kupeza mfundo zina, onani nkhani yakuti “Muzigwiritsa Ntchito Ndalama Mwanzeru,” mu Galamukani! ya March 2009 ndi nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndingatani Kuti Ndizisamala Ndalama?” mu Galamukani! ya June 2006.