Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ngakhale Kuti Ndinalumala, Ndine Wosangalalabe

Ngakhale Kuti Ndinalumala, Ndine Wosangalalabe

Ngakhale Kuti Ndinalumala, Ndine Wosangalalabe

Yosimbidwa ndi José Godofredo Várguez

Ndinabadwa bwinobwino ndipo nditakwanitsa zaka 17 ndinayamba kugwira ntchito yowotcherera zitsulo. Tsiku lina, nditagwira ntchitoyi kwa zaka ziwiri, ndinkawotcherera zitsulo pamwamba pafupi ndi nthambo zamagetsi. Kenako kunayamba kugwa mvula ndipo nthawi yomweyo ndinagwidwa shoko, n’kugwa pansi kuchoka pamtunda wamamita 14. Ndipo ndinakhala chikomokere kwa miyezi itatu. Nditatsitsimuka ndinapezeka kuti miyendo ndi manja anga sizikugwira ntchito. Ndinkaona kuti tsogolo langa lathera pomwepo.

POYAMBA ndinkaimba mlandu Mulungu ndipo sindinkamvetsa kuti n’chifukwa chiyani iye wandisiya ndi moyo. Nthawi zina ndinkaganiza zongodzipha. Ndinalowa zipembedzo zambiri koma palibe chimene chinkanena zolimbikitsa komanso kuyankha mafunso anga okhudza Mulungu. Ndipo zipembedzo zimene ndinalowa sizinkalimbikitsa anthu ake kutsatira mfundo za m’Baibulo. Mayi anga atamwalira mu 1981, ndinayamba kumwa mowa ndi kuyenda juga. Ndinkaganiza kuti popeza kuti ndine wolumala, Mulungu azindimvera chisoni ndiponso kundikhululukira ndikaledzera. Ndinkachitanso zinthu zina zoipa monga kukhala limodzi ndi mkazi amene ndinali ndisanakwatirane naye.

Ndinasintha Kwambiri Maganizo Anga

Nditakwanitsa zaka 37, ndinacheza koyamba ndi Mboni za Yehova. Mayi anga ankakonda kunena kuti a Mboni za Yehova ndi anthu oipa kwambiri, koma iwo ankanena zimenezi chifukwa cha zinthu zabodza zimene anamva zokhudza a Mboniwo. Komabe atabwera kunyumba ine ndinawalandira. Cholinga changa chinali chakuti ndiwasonyeze kuti zimene amakhulupirira sizolondola. Ineyo ndinkadzitenga kuti ndimadziwa kwambiri Baibulo. Koma ndinadabwa kwambiri kuona kuti sindinkadziwa zambiri. Komanso alendowa anandigometsa chifukwa anayankha mafunso anga onse pogwiritsa ntchito Baibulo. Sizinanditengere nthawi yaitali kuti ndikhulupirire kuti ndapeza choonadi.

Koma mkazi amene ndinkakhala naye uja anakana kukhala wa Mboni ndipo tinasiyana. Ndinapitirizabe kusintha moyo wanga kuti ugwirizane ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Mulungu wandithandiza kwambiri kuti ngozi imene inandichitikira isandichititse kutaya mtima kwambiri. Panopa ndine wosangalala ndipo kwa zaka 20 zapitazi ndakhala ndikutumikira monga mlaliki wa nthawi zonse. Popeza kuti ndine wolumala, ambiri amadabwa kuti ndimakwanitsa bwanji kuchita zimenezi. Komabe, sindigwira ntchitoyi ndekha. Ndimakhala ndi mng’ono wanga, dzina lake Ubaldo. Iye ali ndi matenda enaake omwe amamuchititsa kuti nthawi zina azichita zinthu ngati mwana wamng’ono. Ubaldo nayenso anaphunzira choonadi cha m’Baibulo ndipo timatumikira Yehova limodzi.

Ine ndi Ubaldo timathandizana zinthu zambiri. Tikamapita kolalikira Ubaldo amandiyendetsa pa njinga ndiponso amagogoda panyumba za anthu. Ndikamalankhulana ndi mwininyumba iye amandithandiza kutsegula Baibulo komanso kumusonyeza munthuyo mabuku oyenerera. Iye amandithandizanso pa zinthu zina zambiri zomwe sindingathe kuchita ndekha. Ineyo ndimagulitsa mafuta odzola ndipo ndalama zimene ndimapeza zimatithandiza tonse. Komanso anthu a mu mpingo wa Mboni za Yehova wa kwathu, amatithandiza kuphika, kugwira ntchito zapakhomo, komanso kutiperekeza kuchipatala. Ine ndi Ubaldo timathokoza kwambiri zimene anthuwa amatichitira.

Panopa ndine mkulu mumpingo mwathu ndipo abale anga auzimu amandithandiza kwambiri kufufuza nkhani za m’Baibulo. Ndikapeza mfundo yofunika kwambiri, ndimaichonga ndi pensulo pogwiritsa ntchito mlomo wanga.

Anthu akandifunsa kuti adziwe ngati ndine wosangalala, ndimawayankha ndi mtima wonse kuti, Inde. Ndimaona kuti ndili ndi zifukwa zonse zokhalira wosangalala. Ndimadziwa kuti moyo wathu uli ndi cholinga, ndipo ndimayembekezera kuti zinthu zimene Mulungu analonjeza anthu okhulupirika zidzachitikadi. Anthu okhulupirika adzakhala ndi moyo wathanzi m’dziko latsopano la paradaiso limene likubwera.—Yesaya 35:5, 6; Luka 23:43.

[Chithunzi patsamba 24]

José ali ndi zaka 18. Anachita ngozi patatha chaka chimodzi

[Chithunzi patsamba 25]

Ine ndi mng’ono wanga Ubaldo timathandizana kwambiri mu utumiki ku Mexico

[Chithunzi patsamba 25]

Ndikamakamba nkhani ku Nyumba ya Ufumu munthu wina amanditsegulira Baibulo

[Chithunzi patsamba 25]

Anthu ena a mumpingo mwathu amatithandiza kuphika ndiponso ntchito zina zapakhomo