Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pemphani Thandizo

Pemphani Thandizo

Pemphani Thandizo

“Ndipo wina akam’laka mmodziyo, awiri adzachirimika.”—Mlaliki 4:12.

NGATI tili ndi anthu otithandiza pamene tikumenyana ndi mdani, kaya mdaniyo akhale wamphamvu bwanji, nthawi zambiri timapambana. Choncho, ngati mukufuna kugonjetsa chizolowezi chosuta fodya, mungapemphe anthu ena kuti akuthandizeni. Mungapemphe anthu a pabanja panu, anzanu, kapena anthu ena amene mukuona kuti angakuthandizeni.

Anthu amene poyamba ankasuta fodya koma anasiya angakuthandizeni kwambiri chifukwa angamvetse vuto lanu komanso angadziwe mmene angakuthandizireni. Bambo wina wa ku Denmark, dzina lake Torben, anati: “Thandizo limene ena anandipatsa kuti ndisiye kusuta fodya linali lofunika kwambiri.” Abraham, yemwe amakhala ku India, analemba kuti: “Chikondi chimene anthu apabanja panga komanso Akhristu anzanga ankandisonyeza chinandithandiza kwambiri kuti ndisiye kusuta.” Komabe nthawi zina thandizo limene achibale ndi anzanu angapereke silingakhale lokwanira.

Mwachitsanzo, bambo wina dzina lake Bhagwandas anati: “Ndakhala ndikusuta fodya kwa zaka 27 koma nditadziwa zimene Baibulo limanena zokhudza zizolowezi zoipa, m’pamene ndinaganiza zosiya kusuta. Ndinayesetsa kuti ndichepetse kusuta. Ndinapeza anzanga ena ocheza nawo. Ndiponso ndinapita kwa alangizi kuti andithandize. Koma palibe chinathandiza. Tsiku lina usiku ndinapemphera kwa Yehova Mulungu kuti andithandize. Ndipo kenako ndinasiya kusuta.”

Chinthu chinanso chimene chingathandize ndi kukonzekera mavuto amene mungakumane nawo ngati mutasiya kusuta. Kodi mungakumane ndi mavuto otani? Nkhani yotsatira ifotokoza za mavuto amenewa.

[Bokosi patsamba 5]

KODI NDI BWINO KUGWIRITSA NTCHITO MANKHWALA?

Masiku ano kuli makampani ambiri amene akupanga mankhwala othandiza anthu kusiya kusuta fodya ndipo akupanga ndalama zambiri. Koma musanaganize zogwiritsa ntchito mankhwala amenewa, dzifunseni mafunso otsatirawa:

Kodi ubwino wake ndi wotani? Akuti mankhwala ambiri otere amachepetsa chibaba komanso mavuto ena amene amabwera munthu akasiya kusuta fodya. Koma anthu ena amati mankhwalawa amangothandiza munthu kwa nthawi yochepa. Choncho, ngati mukufuna kugwiritsa ntchito mankhwala amenewa muyenera kufufuza kuti mudziwe zenizeni.

Kodi kuopsa kwake n’kotani? Mankhwala ena amachititsa anthu kusanza, kukhumudwa, komanso kukhala ndi maganizo ofuna kudzipha. Dziwani kuti mankhwala ena amakhalanso ndi nikotini amene amayambitsa matenda ena. Choncho, munthu amene amagwiritsa ntchito mankhwala amenewa, chilakolako chake chofuna kusuta fodya sichitheratu.

Kodi njira zina zosiyira fodya ndi zotani? Pakafukufuku wina, pa anthu 100 aliwonse amene anakwanitsa kusiya kusuta fodya, 88 ananena kuti anangosiya popanda kugwiritsa ntchito mankhwala aliwonse.