Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
Kalata ina imene Papa Benedict XVI analembera mabishopu a Katolika inati: “Panopa n’zofunika kwambiri kuti . . . bungwe la United Nations komanso mabungwe azachuma padziko lonse asinthidwe mwina ndi mwina n’cholinga chakuti akhale ndi mphamvu zambiri.”—L’OSSERVATORE ROMANO.
“Pa anthu atatu alionse ku Ukraine, mmodzi amatha kusuta paketi imodzi ya fodya tsiku lililonse.”—EXPRESS, UKRAINE.
Ku United States, anyamata 44 pa 100 alionse osakwanitsa za 20 omwe anafunsidwa, ananena kuti “aonapo kamodzi kapena kangapo pa Intaneti, chithunzi cha mtsikana wa m’kalasi mwawo atajambulitsa wosavala.”—TIME, U.S.A.
“Chiwerengero cha Anthu Anjala Chafika Poipa”
Nyuzipepala ya Associated Press yanena kuti nkhondo, chilala, mavuto azandale, kukwera mitengo kwa zakudya ndiponso umphawi zachititsa kuti zinthu zifike poipa kwambiri. Chiwerengero cha anthu ogona ndi njala chapitirira 1 biliyoni. Josette Sheeran yemwe amagwira ntchito ku bungwe la WFP, lomwe ndi nthambi ya United Nations yoona za chakudya padziko lonse, anati: “Vuto la njala ndi loopsa kwambiri. . . . Pali zinthu zitatu zimene zimachitika anthu akakhala ndi njala: Amatha kuukira boma, kusamukira kumayiko ena kapena kufa kumene. Zinthu zonsezi n’zosayenera.” Panopa chiwerengero cha anthu anjala chikuwonjezereka mofulumira kwambiri kuposa kuwonjezereka kwa anthu padziko lonse. Ngakhale m’mayiko olemera, chiwerengero cha anthu amene sapeza chakudya chokwanira chawonjezereka ndi anthu oposa 15 pa anthu 100 alionse.
Kuwerenga Musanagone N’kothandiza
Makolo akamawerengera ana awo mabuku anawo asanakagone, zimawathandiza kuti tulo libwere. Koma kuwonjezera pamenepo akatswiri akuti zimenezi zimathandiza kuti ana aziphunzira kulankhula msanga, azitha kutsegula okha mabuku komanso azitha kukumbukira zinthu. Nyuzipepala ya Guardian inanena kuti: “Kuwerenga mokweza kumathandiza anawo kugwirizana ndi makolo awo ndiponso kuchitira limodzi zinthu. Komanso kumachititsa kuti anawo azikonda kuwerenga.” Pulofesa Barry Zuckerman, yemwe anatsogolera kafukufukuyu, anati: “Mapeto ake, anawo amakonda mabuku chifukwa chakuti amawerenga ndi munthu amene iwo amamukonda.”
Ng’ombe Zosangalala Zimatulutsa Mkaka Wambiri
Asayansi pa yunivesite ya Newcastle ku England anati: “Ng’ombe zimene zimapatsidwa mayina zimatulutsa mkaka wambiri kuposa zopanda mayina.” Ndipo ng’ombe zimene zimakondedwa iliyonse payokha zimawonjezera mkaka umene zimatulutsa ndi malita pafupifupi 280 pachaka. N’chifukwa chiyani zili choncho? Dr Catherine Douglas wa pa yunivesite ina ya zaulimi anati: “Anthu akamakondedwa paokhapaokha amasangalala. N’chimodzimodzinso ndi ng’ombe, zimasangalala kwambiri komanso zimamasuka ngati zikukondedwa iliyonse payokha.” Dr Douglas ananenanso kuti: “Zimene kafukufukuyu wasonyeza n’zimene alimi osamalira bwino ziweto akhala akuchita kwa zaka zambiri. Kusonyeza chidwi pa ng’ombe iliyonse payokha, monga kuitchula dzina, komanso kusewera nayo kuyambira ili yaying’ono, kumathandiza kuti ng’ombe izikhala yosangalala, izolowerane ndi anthu komanso izipereka mkaka wambiri.”