Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Khalanibe pa Ubwenzi ndi Yehova”

“Khalanibe pa Ubwenzi ndi Yehova”

Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa Mutu Wakuti

“Khalanibe pa Ubwenzi ndi Yehova”

● Msonkhano wa masiku atatu umenewu udzachitika m’malo osiyanasiyana padziko lonse lapansi. M’madera ambiri, tsiku lililonse msonkhano uzidzayamba 8:20 m’mawa ndi nyimbo zopanda mawu. Mutu wa tsiku Lachisanu, womwe wachokera pa lemba la Salmo 73:28, ndi wakuti “Kwa Ine Kuyandikira kwa Mulungu Ndi Chinthu Chabwino.” Nkhani ya tcheyamani wa msonkhano ikadzatha, padzabwera nkhani yakuti “Misonkhano Yachigawo Imatithandiza Kukhalabe pa Ubwenzi ndi Yehova” ndiponso yakuti “Mwanayo Akufuna Kuulula za Atate.” Kenako nkhani yosiyirana ya mutu wakuti “Tsanzirani Anthu Amene Anakhalabe pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova” idzafotokoza mmene Abrahamu, Rute, Hezekiya ndi Mariya anachitira zimenezi. Chigawo cha m’mawa chidzatha ndi nkhani yaikulu ya mutu wakuti “Mmene Yehova Amayandikirira kwa Ife.”

Nkhani yoyamba ya chigawo chamasana Lachisanu ndi yakuti “Mayankho a Mafunso Okhudza Yehova.” Nkhani imeneyi ikadzatha, padzabwera nkhani yakuti “Lolani kuti Chilango cha Yehova Chikuumbeni,” ndi yakuti “Musam’kwiyire Yehova.” Kenako padzabwera nkhani yosiyirana yokhala ndi mbali zisanu yakuti “Kulankhulana Bwino Kumathandiza Mabanja Kukhalabe pa Ubwenzi ndi Yehova.” Mbali zisanu zimenezi ndi zakuti: “Yehova Ndi Chitsanzo Chabwino Kwambiri pa Nkhani ya Kulankhulana,” “Amuna, Muzilankhulana Bwino ndi Akazi Anu,” “Akazi, Muzilankhulana Bwino ndi Amuna Anu,” “Makolo, Muzilankhulana Bwino ndi Ana Anu,” ndiponso “Ananu, Muzilankhulana Bwino ndi Makolo Anu.” Chigawo chamasana chidzatha ndi nkhani yakuti, “Chilengedwe Chimatithandiza Kudziwa Bwino ‘Mulungu Wamoyo.’”

Mutu wa Loweruka ndi wakuti, “Yehova Amakonda Anthu Owongoka Mtima,” ndipo wachokera pa Miyambo 3:32. Nkhani yosiyirana yokhala ndi mbali zisanu ya mutu wakuti “Thandizani Anthu kuti ‘Ayanjanenso ndi Mulungu’” ili ndi nkhani zakuti “Otalikirana ndi Mulungu Ndiponso Opanda Chiyembekezo,” “Anawafunsa,” “Kwaniritsani Udindo Wanu Mukamalalikira ndi Munthu Wina,” “Akopeni ndi Khalidwe Lanu Labwino,” ndiponso “Pitirizani Kuchita Khama.” Pambuyo pa nkhani zakuti “Utumiki wa Nthawi Zonse Umalimbitsa Ubwenzi Wanu ndi Yehova,” ndiponso “Okonda Yehova Sakhala ndi Chowakhumudwitsa,” chigawochi chidzatha ndi nkhani ya ubatizo. Kenako anthu oyenerera adzabatizidwa.

Loweruka, chigawo chamasana kudzakhala nkhani yosiyirana ya mbali 8 ya mutu wakuti, “Musalole Chilichonse Kusokoneza Ubwenzi Wanu ndi Yehova.” Mbali zimenezi zidzakhala zakuti, “Zochita za Satana Zovuta Kuzizindikira,” “Kunyada,” “Ndalama,” “Thanzi Lathu,” “Ntchito,” “Zosangalatsa,” “Banja,” ndi “Zipangizo Zamakono.” Kenako padzabwera sewero la mawu okha la mutu wakuti, “Musataye Mtima Yehova Akakudzudzulani.” Tsikuli lidzatha ndi nkhani yakuti “Khalanibe pa Ubwenzi ndi Yehova Ngati Mmene Anachitira Yeremiya.”

Mutu wa tsiku Lamlungu, wochokera pa Yoswa 23:8, ndi wakuti “Muumirireni Yehova.” Pambuyo pa nyimbo ndi pemphero lotsegulira, padzabwera nkhani yosiyirana ya mutu wakuti “Kuzindikira Makhalidwe Abwino a Yehova.” Nkhani yosiyiranayi idzafotokoza makhalidwe 8 a Yehova ndipo idzakhala ndi mbali zakuti, “Wofikirika,” “Wachisoni,” “Woyamikira,” “Woolowa Manja,” “Wosakondera,” “Wokhululuka,” “Wololera,” ndi “Wokhulupirika.” Kenako padzabwera nkhani ya onse ya mutu wakuti “Kodi Mungatani Kuti Muyandikire kwa Mulungu?” Chigawo cha m’mawa chidzatha ndi chidule cha Phunziro la Nsanja ya Olonda, limene limachitika mlungu uliwonse.

Lamlungu masana kudzakhala sewero losonyeza zinthu zimene zinachitika m’nthawi ya Akhristu oyambirira. Seweroli likunena za mmene Akhristu anathawira ku Yerusalemu ndipo ndi lamutu wakuti, “Yendani mwa Chikhulupiriro, Osati mwa Zooneka ndi Maso.” Seweroli likadzatha, padzabwera nkhani yomaliza ya msonkhano wachigawowu ya mutu wakuti “Khalanibe ‘M’malo Otetezeka a Wam’mwambamwamba.’”

Konzekereranitu panopa kuti mudzakhalepo. Kuti mudziwe malo amene kudzachitikire msonkhanowu kufupi ndi kwanu, kafunseni ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kapena lemberani ofalitsa a magazini ano. Nsanja ya Olonda ya March 1, imene imafalitsidwanso ndi ofalitsa a magazini ino, ili ndi m’ndandanda wa malo amene kudzachitikire misonkhanoyi ku Malawi ndi ku Mozambique.