Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Atsogoleri Achipembedzo Ayenera Kulipidwa Akachititsa Mwambo Winawake?

Kodi Atsogoleri Achipembedzo Ayenera Kulipidwa Akachititsa Mwambo Winawake?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Atsogoleri Achipembedzo Ayenera Kulipidwa Akachititsa Mwambo Winawake?

M’MAYIKO osiyanasiyana, atsogoleri a matchalitchi ambiri amalipiritsa ndalama akachititsa mwambo wa ubatizo, ukwati kapena maliro. Ndalama zimene amawalipira zimakhala zochuluka zedi.

Atsogoleri ena achipembedzo amalipidwa ndi boma akachititsa mwambo winawake wa boma komanso akamatsegula ndi pemphero tsiku lililonse zokambirana za kunyumba ya malamulo. N’zoona kuti anthu ambiri amayamikira ntchito zimene atsogoleri achipembedzo amagwira komanso pamafunika ndalama zoyendetsera matchalitchi awo. Koma kodi Baibulo limavomereza kuti atsogoleriwa azilipiritsa anthu ndalama kapena kuchita zinthu zokopa anthu kuti apereke ndalama?

“Nyumba ya Malonda”?

Pa nthawi imene Yesu Khristu anali padziko lapansi, atsogoleri achipembedzo chachiyuda ndi anthu ena ankaona zochitika zachipembedzo, makamaka mwambo wa Pasika ngati nthawi yopanga ndalama. Kodi Yesu ankasangalala ndi zimenezi? Ayi. Baibulo limatiuza kuti iye “anakhuthula makobili a osintha ndalama ndi kugubuduza matebulo awo.” Ndiyeno anati: “Mulekeretu kusandutsa nyumba ya Atate wanga kukhala nyumba ya malonda!”—Yohane 2:14-16.

Zinthu zofanana ndi zimenezi zinachitikanso m’nthawi ya mneneri Mika, yemwe anakhala ndi moyo zaka za m’ma 700 B.C.E. Baibulo limanena kuti atsogoleri achipembedzo a ku Isiraeli ‘ankaipidwa ndi chiweruzo,’ kapena kuti chilungamo, ndipo ansembe ‘ankaphunzitsa chifukwa cha malipiro.’ Komabe, iwo ankaganiza kuti Mulungu akusangalala nawo, ndipo ankanena kuti, “Kodi Yehova sali pakati pa ife?” (Mika 3:9, 11) Koma Yehova sanali pakati pawo. Iye ankanyansidwa nawo ndipo anauza mneneri wake mobwerezabwereza kuti awadzudzule.

Masiku ano, atsogoleri achipembedzo ambiri amadyeranso anthu masuku pamutu, ndipo amasandutsa malo awo opempherera kukhala ‘nyumba za malonda.’ Matchalitchi ambiri amachita malonda ndipo nthawi zambiri amapeza phindu lochuluka chifukwa chogulitsa mafano ndi zinthu zosiyanasiyana zachipembedzo. *1 Yohane 5:21.

“Munalandira Kwaulere, Patsani Kwaulere”

Potuma atumwi ake kuti akalalikire uthenga wabwino, kuchiritsa odwala ndiponso kuukitsa akufa, Yesu anawauza kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyo 10:7, 8) Otsatira a Yesu sankafunika kulipiritsa anthu akawachitira zinazake. Yesu mwiniwakeyo anapereka chitsanzo chabwino potumikira anthu popanda kuwalipiritsa.

Potsatira chitsanzo cha Yesu, mtumwi Paulo ankachita utumiki wake “kwaulere.” (1 Akorinto 9:18) Akafuna ndalama, ankagwira ntchito yopanga mahema. (Machitidwe 18:1-3) Choncho, ponena za iyeyo ndi amishonale anzake, iye anati: “Sitichita nawo malonda mawu a Mulungu, mmene ambiri akuchitira.” (2 Akorinto 2:17) Koma bwanji za ndalama zogwiritsira ntchito pampingo, mwina zogulira malo olambirira kapena zochitira lendi malo amenewa?

“Mulungu Amakonda Wopereka Mokondwera”

Mboni za Yehova zimapeza ndalama kuchokera kwa anthu amene amapereka mwa kufuna kwawo. Zimatsatira mfundo yakuti: “Aliyense achite mwa kutsimikiza kwa mtima wake, osati monyinyirika kapena mokakamizika ayi, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.” (2 Akorinto 9:7) Potsatira mfundo imeneyi, Mboni za Yehova sizigulitsa mabuku awo ndiponso sizilipiritsa zikachititsa mwambo wa ubatizo, ukwati, kapena maliro. Komanso sizipereka chakhumi kapena kuyendetsa mbale ya zopereka pamisonkhano yawo. Aliyense amene akufuna kupereka ndalama zothandizira ntchito yawo ya padziko lonse yolalikira, amaika ndalamazo m’mabokosi amene amaikidwa kumbuyo pamalo awo olambirira.

Padziko lonse lapansi, ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo n’zimene zimathandiza Mboni za Yehova kumanga Nyumba za Ufumu, Nyumba za Msonkhano, maofesi a nthambi, ndi nyumba zosindikizira mabuku. Amagwiritsanso ntchito ndalamazi pothandiza anthu pakagwa masoka achilengedwe. Mofanana ndi mkazi wamasiye wosauka amene Yesu anamuyamikira, anthu ena amapereka ndalama zochepa kwambiri. (Luka 21:2) Koma ena amapereka zambiri. Mulimonsemo, anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo n’kumapereka mmene angathere, amadalitsidwa kwambiri ndi Mulungu ndipo amakhala ndi chimwemwe chenicheni.—Machitidwe 20:35; 2 Akorinto 8:12.

[Mawu a M’munsi]

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Yesu anawauza chiyani anthu amene ankachita malonda m’kachisi?—Yohane 2:14-16.

● Kodi mtumwi Paulo ankalandira ndalama kwa anthu chifukwa cha ntchito yake yachipembedzo?—2 Akorinto 2:17.

● Kodi Yehova amasangalala ndi munthu wopereka motani?—2 Akorinto 9:7.

[Mawu Otsindika patsamba 23]

“Mulekeretu kusandutsa nyumba ya Atate wanga kukhala nyumba ya malonda!”—Yohane 2:14-16.