Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupanikizika Kumayambitsa Mavuto Aakulu

Kupanikizika Kumayambitsa Mavuto Aakulu

Kupanikizika Kumayambitsa Mavuto Aakulu

Kodi chimachitika n’chiyani mukamathamangira basi kapena sitima? Magazi anu amayamba kuthamanga ndiponso mtima wanu umagunda mofulumira. Komabe pakapita nthawi, mtima wanu umabwerera m’malo mwake ngakhale basi kapena sitimayo itakuthawani.

KOMA ngati chinthu chimene chikuchititsa kuti mupanikizikecho chikutenga nthawi yaitali chisanathe, zimene zimachitika zimasiyana kwambiri ndi zimene tafotokoza pamwambazi. Pangapite nthawi yaitali kuti nkhawa, kuphwanya kwa thupi, kuthamanga magazi ndiponso kusokonezeka kwa ntchito yogaya chakudya m’thupi zithe. Anthu ambiri amaona kuti amakhala opanikizika nthawi zonse. Mwachitsanzo, ambiri sasangalala ndi ntchito imene amagwira. Kodi kupanikizika kungakhudze bwanji thanzi lanu?

Mmene Kupanikizika Kungakukhudzireni

Dr. Arien van der Merwe, katswiri wa mavuto amene amabwera chifukwa chopanikizika, anafotokoza mmene kupanikizika kumakhudzira munthu. Iye ananena kuti munthu akapanikizika, “ubongo wake umachititsa kuti thupi litulutse timadzi tinatake, tomwe timakonzekeretsa chiwalo chilichonse kuthana ndi vuto lililonse.”

Pa nthawiyi mumatha kuchita zinthu mosiyana ndi mmene mumachitira nthawi zonse. Mukaona, kumva kapena kugwira chinthu choopsa, thupi limatumiza uthenga ku ubongo. Ndipo nthawi yomweyo ubongowo umatumiza uthenga ku mtima, mapapo ndi ziwalo zina kuti ziyambe kugwira ntchito mofulumira.

Choncho pakachitika zinthu zamwadzidzidzi, thupi lanu limatha kuchita zinthu mwachangu. Mwachitsanzo, ngati galimoto ikufuna kukugundani mumathawa nthawi yomweyo. Kupanikiza kumeneku ndi kwabwino chifukwa kumatha kukupulumutsani. Koma kukhala wopanikizika nthawi yaitali kumayambitsa mavuto.

Kupanikizika Kumayambitsa Matenda Ambiri

Mukapanikizika, minofu ya m’thupi mwanu imakungika, magazi amathamanga kwambiri ndiponso mtima umagunda mofulumira. M’magazi mumadzaza shuga, mafuta ndi zinthu zina. Zimenezi zimafunika kuti zizichitika kwa nthawi yochepa kuti thupi lithe kuchita zinthu mwamphamvu ndiponso mwachangu. Koma zikachitika kwa nthawi yaitali, ziwalo zina zofunika kwambiri m’thupi zimawonongeka. Ndiyeno kodi zotsatira zake zimakhala zotani?

Msana ndi mutu zimayamba kupweteka ndiponso minofu ya m’khosi ndi minofu ina ya m’thupi imakungika. Madokotala ambiri amati munthu akayamba kusonyeza zizindikiro zimenezi, pamatenga nthawi yaitali kuti vuto lakelo lithe. Kukhala wopanikizika kwa nthawi yaitali kumachititsa kuti munthu asamaganize mwachangu, asamagwire bwino ntchito, zinthu zisamamusangalatse komanso kuti asamagwirizane ndi anzake. Kungayambitsenso kuti munthu azitsegula ndiponso kumva kupweteka m’mimba ndi khosi. Nthawi zina ngati munthu wapanikizika kwa nthawi yaitali angadwale matenda enanso oopsa kwambiri. Angathe kufa ziwalo, akhoza kudwala matenda a mtima komanso matenda a shuga. Ngati munthuyo anali kale ndi matenda amenewa, matendawo akhoza kukula.

Mayi Van der Merwe anafotokoza kuti: “Mankhwala enaake amene thupi limatulutsa munthu akapanikizika kwa nthawi yaitali, amachititsa kuti mafuta aunjikane pamimba ndi pamsana.” Kupanikizika kumayambitsanso matenda ena a pakhungu kapenanso kuwonjezera matendawa. Enanso akuganiza kuti kupanikizika kwambiri kumayambitsa matenda ovutika maganizo, kumachititsa kuti munthu asamachedwe kupsa mtima ndiponso kuti atope kwambiri n’kufika poti sangathenso kugwira ntchito. Komanso, kukhala wopanikizika nthawi zonse kumachititsa kuti munthu azilephera kukumbukira zinthu komanso kuika maganizo ake onse pa zimene akuchita. Kumachepetsanso mphamvu yoteteza thupi ku matenda. Zikatero munthu akhoza kudwala matenda osiyanasiyana monga chimfine, khansa ndi matenda ena amene amayamba chifukwa chakuti thupi ladziukira lokha.

N’chifukwa chiyani ndi bwino kudziwa mmene tingachepetsere kupanikizika? Chifukwa chakuti kumakhudza mbali zonse za moyo wathu. Kumakhudza maganizo athu, thupi lathu, komanso moyo wathu wauzimu. Komabe, kungokhaliratu osapanikizika si bwinonso. Chifukwa chiyani?

Kupanikizika tingakuyerekezere ndi kukwera njinga. Kukwera njinga kungachititse kuti munthu azimva kukoma. Koma ngati njingayo itayamba kuthamanga kwambiri mpaka munthuyo kulephera kuiwongolera, akhoza kuvulala kapena kufa kumene. N’chimodzimodzinso ndi kupanikizika. Kupanikizika pang’ono kungachititse kuti munthu azimva kukoma ndi moyo chifukwa amaganiza mwachangu, amagwira ntchito mwakhama, amasangalala akamachita zinthu ndiponso amakhala ndi thanzi labwino.

Koma kodi tingatani kuti tisamapanikizike kwambiri? Nkhani yotsatira ifotokoza njira zimene zingatithandize kuti tisamapanikizike kwambiri pa moyo wathu.

[Bokosi patsamba 5]

‘TINAPANGIDWA MODABWITSA’ NDI MLENGI WANZERU KOMANSO WACHIKONDI

Anthu ena amanena kuti zimene anthufe timachita tikapanikizika tinatengera zimene anthu akale kwambiri ankachita akamathawa zinyama zinazake zakale zofanana ndi njovu komanso akambuku a mano akuthwa ngati mpeni. Koma zimenezi si zoona. Zinthu zodabwitsa zimene thupi lathu limachita tikapanikizika ndi umboni wakuti tinalengedwa ndi Mlengi waluso kwambiri. Mwachitsanzo, tikadzicheka magazi amatha kusiya okha kutuluka, ndiponso m’magazi muli mphamvu yotha kulimbana ndi matenda komanso kupoletsa zilonda. Zonsezi ndi umboni wakuti Mlengi wathu ndi wanzeru komanso wachikondi.

Zimene thupi lathu limachitazi zimasonyeza kuti ‘chipangidwe chathu n’choopsa ndi chodabwitsa.’ (Salmo 139:13-16) Mulungu mwachikondi chake amatipatsa zinthu zabwino kuti zitithandize pa moyo wathu ndiponso kuti zitithandize mwauzimu. Komanso analenga anthu m’njira yochititsa chidwi kwambiri kuti azitha kusangalala ndi moyo. Zonsezi zimatitsimikizira kuti dziko lapansi likadzakhala Paradaiso, sipadzakhala zopweteka, kulira, kapena imfa.—Chivumbulutso 21:3-5.

[Chithunzi patsamba 5]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

ZIMENE ZIMACHITIKA MUNTHU AKAMANGOKHALA WOPANIKIZIKA NTHAWI ZONSE

Kupweteka kwa mutu

Kukukuta mano

Kupweteka kwa khosi

Matenda a mtima

Zilonda za m’mimba

Kupweteka kwa msana

Kukungana kwa minofu