Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Matenda Ofooketsa Mafupa Amayamba Mosaonekera

Matenda Ofooketsa Mafupa Amayamba Mosaonekera

Matenda Ofooketsa Mafupa Amayamba Mosaonekera

Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Anna, ankadwala matenda enaake ovutika kudya. Koma atayamba kuchira, tsiku linalake anagwa mwadzidzidzi. Iye ananena kuti ankamva ululu woopsa mumsana. Mafupa ake awiri a mumsana anali atathyoka ndipo zimenezi zinachititsa kuti afupike ndi masentimita asanu. Zonsezi zinachitika chifukwa chakuti Anna ankadwala matenda ofooketsa mafupa.

MATENDA ofooketsa mafupa amayamba mosaonekera ndipo munthu sasonyeza zizindikiro zilizonse zoti ali ndi matendawa mpaka mafupawo amabowokabowoka mkati. Kenako munthuyo akachita zinazake mwamphamvu, akagunda chinachake, kapena akagwa, amathyoka fupa. Nthawi zambiri mafupa amene amathyoka ndi a m’chiuno, m’nthiti, mumsana kapena padzanja. Anthu ambiri amaganiza kuti matendawa amangogwira amayi okalamba amene alinso ofooka. Koma ngakhale achinyamata angadwale matendawa, ngati mmene anadwalira Anna.

Matendawa Ndi Oopsa Kwambiri

Bungwe lina loona za matenda ofooketsa mafupa padziko lonse linati “m’mayiko a ku Ulaya, pa masekondi 30 alionse, munthu mmodzi amathyoka fupa chifukwa cha matenda ofooketsa mafupa.” Ku United States, anthu 10 miliyoni amadwala matendawa, ndipo anthu ena 34 miliyoni akhoza kudzadwala matendawa chifukwa chakuti mafupa awo ndi osalimba kwambiri. Bungwe lina loona za umoyo ku America linati: “Mkazi mmodzi pa akazi awiri alionse, ndi mwamuna mmodzi pa amuna anayi alionse, a zaka 50 kapena kuposa, adzathyoka fupa pa nthawi inayake pa moyo wawo chifukwa cha matendawa.” Ndipotu palibe chiyembekezo choti zimenezi zisintha.

Magazini yofalitsidwa ndi Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse inati anthu amene amathyoka mafupa chifukwa cha matenda ofooketsa mafupa adzawonjezeka kuwirikiza kawiri pa zaka 50 zikubwerazi padziko lonse lapansi. Mwina bungweli linanena zimenezi chifukwa chiwerengero cha anthu okalamba chikuyembekezeka kukula. Komabe mfundo yaikulu ndi yakuti matenda amenewa amabweretsa mavuto aakulu. Anthu ambiri odwala matendawa amalumala kapena kufa kumene. Pafupifupi anthu 25 pa anthu 100 alionse a zaka 50 kapena kuposa amene amathyoka fupa la m’chiuno, amafa chaka chisanathe. Zimenezi zimachitika chifukwa cha matenda ena amene amayamba chifukwa cha kuvulalako.

Kodi Ndani Angadwale Matendawa?

Posachedwapa ofufuza apeza kuti anthu ambiri amadwala matendawa chifukwa chotengera kwa makolo awo. Makolo akakhala kuti anadwalapo matendawa ndipo anathyokapo fupa la m’chiuno, kawirikawiri ana awonso amadzadwala matendawa n’kudzathyokanso fupa. Nthawi zinanso ngati mayi wapakati sakudya zakudya zokwanira, mwana wake amabadwa ndi mafupa osalimba ndipo zimenezi zingamuchititsenso kuti adzadwale matenda ofooketsa mafupa. Komanso, munthu akamakalamba mafupa ake amakhala osalimba, ndipo akhoza kudwala matenda amenewa. Palinso matenda ena amene angachititse munthu kudwala matenda ofooketsa mafupa, monga matenda a shuga ndi matenda a chithokomiro.

Akazi akasiya kusamba, thupi lawo limasiya kupanga timadzi tinatake timene timachititsa kuti mafupa azikhala olimba. N’chifukwa chake akazi ambiri amadwala matendawa kuposa amuna. Mkazi akachitidwa opaleshoni yomuchotsa mbali zinazake za chiberekero, akhoza kusiya kusamba nthawi yake isanakwane, ndipo zikatero akhoza kudwala matendawa mosavuta.

Koma pali zinthu zina zimene munthu angachite kuti apewe matendawa, monga kudya zakudya zoyenera ndi kuchita masewera olimbitsa thupi. Kudya zakudya zokhala ndi kasiyamu ndi vitamini D wokwanira, kungathandize munthu kupewa matendawa. Kudya mchere wambiri kungachititse kuti munthu adwale matendawa, chifukwa mchere umachititsa kuti thupi lizitaya kasiyamu wambiri. Komanso anthu omwa mowa kwambiri, amene nthawi zambiri sadya zakudya zolongosoka, angadwale mosavuta matenda ofooketsa mafupa.

Monga tafotokozera kumayambiriro kwa nkhaniyi, matenda ovutika kudya ndi amene anachititsa kuti Anna adwale matenda ofooketsa mafupa. Matendawa anamuchititsa kuti akhale ndi vuto la kuperewera kwa zakudya, akhale woonda kwambiri, ndiponso kuti asiye kusamba. Zimenezi zinachititsa kuti akhale ndi mafupa osalimba.

Chinanso chimene chimachititsa munthu kuti adwale matendawa ndicho kusachita mokwanira masewera olimbitsa thupi. Kusuta fodya kukhozanso kuyambitsa matendawa. Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linati pa anthu 8 alionse amene amathyoka fupa la m’chiuno, munthu mmodzi amakhala wosuta fodya. Koma ofufuza apeza kuti munthu akasiya kusuta, mafupa ake amayambanso kulimba ndipo sangathyoke chisawawa.

Tingapewe Bwanji Matendawa?

Munthu ayenera kuyamba kudziteteza ku matenda amenewa kuyambira ali mwana chifukwa imeneyi ndi nthawi imene mafupa amakula komanso amayamba kulemera kwambiri. Kasiyamu wambiri amasungidwa m’mafupa ndipo ndi amene amachititsa kuti mafupa akhale olimba. Zakudya zimene zimakhala ndi kasiyamu wambiri ndi monga mkaka ndi zakudya zopangidwa kuchokera ku mkaka ngati yogati ndi tchizi. Kasiyamu amapezekanso m’minga za nsomba ndi m’ndiwo za masamba obiriwira.

Kuti thupi lithe kugwiritsa ntchito kasiyamu, limafunika kukhala ndi vitamini D wokwanira. Munthu amapeza vitamini ameneyu akakhala padzuwa. Dokotala wina, dzina lake Manuel Mirassou Ortega, amenenso ali m’bungwe loona za matenda a mafupa ku Mexico, anati: “Kukhala padzuwa kwa mphindi 10 tsiku lililonse kumathandiza kupewa matenda ofooketsa mafupa, chifukwa munthu amapeza vitamini D wokwanira.” Vitamini D amapezekanso m’zakudya monga mazira, nsomba za m’nyanja yamchere ndi chiwindi.

Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kofunikanso kwambiri kuti munthu asadwale matenda ofooketsa mafupa. Munthu akakhala wamng’ono, kuchita masewera olimbitsa thupi kumalimbitsa mafupa ake ndipo akakhala wokalamba, kumamuthandiza kuti mafupa ake asayambe kufooka. Kuchita zinthu zolimbitsa thupi monga kuyenda, kukwera masitepe, kunyamula zinthu zolemera, ngakhale kuvina kumathandiza kwambiri. *

Pali zinthu zambiri zimene munthu angachite kuti apewe matendawa. Monga taonera, munthu angafunike kuyamba kudya zakudya zoyenera ndiponso kuchita masewera olimbitsa thupi n’cholinga choti akhale ndi mafupa olimba. N’zovuta kuti munthu amene wazolowera kungokhala asinthe n’kuyamba kuchita masewera olimbitsa thupi. Komabe anthu amene amayesetsa kusintha amapewa matenda ambiri kuphatikizapo matenda ofooketsa mafupa, amene amagwira anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Kuchita masewera olimbitsa thupi mopitiriza muyezo, mpaka kufika posiya kusamba ngati munthu ali wamkazi, kungachititse kuti mafupa akhale osalimba. Akuti ndi bwino kuti akazi a zaka zoposa 65 azikayezetsa mafupa awo kuchipatala kuti adziwe ngati mafupawo ayamba kufooka. Ngati mafupawo ayamba kufooka, akhoza kuwapatsa mankhwala kuti apewe kapena achiritse matendawa. Koma musanayambe kulandira chithandizo chilichonse, muyenera kuganizira kaye ubwino ndi kuipa kwake.

[Mawu Otsindika patsamba 21]

Kuti munthu apewe matendawa, amafunika kudya zakudya zoyenera komanso kuchita masewera olimbitsa thupi, zimene zimathandiza kuti mafupa akhale olimba

[Bokosi/Zithunzi patsamba 19]

Matenda ofooketsa mafupa amachititsa kuti munthu akhale ndi mafupa osalimba, oti akhoza kuthyoka mosavuta. Kuti adziwe ngati munthu ali ndi matendawa, amajambula mafupa kuchipatala.

[Zithunzi]

Fupa labwinobwino

Fupa lamatenda

[Mawu a Chithunzi]

© BSIP/Photo Researchers, Inc.

[Chithunzi patsamba 20]

Masewera olimbitsa thupi amathandiza kuti tikhale ndi mafupa olimba

[Chithunzi patsamba 20]

Mtedza wa almond ndi mkaka zimakhala ndi kasiyamu wambiri