Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kusamalira Thanzi Langa?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kusamalira Thanzi Langa?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kusamalira Thanzi Langa?

Chongani cholinga chilichonse chimene mukufuna kukwaniritsa.

Kutsitsa sikelo

Kukhala ndi khungu losangalala

Kukhala wamphamvu

Kukhala wochangamuka

Kuchepetsa nkhawa

Kusapsa mtima msanga

Kusadzikayikira

PALI zinthu zina pa moyo zimene simungachite kusankha, monga makolo anu, achibale anu, kumene mumakhala ndi zina zotero. Koma mukhoza kusankha kuti mukhale ndi thanzi labwino kapena ayi. Kuti mukhale ndi thanzi labwino, zimadalira chibadwa chanu komanso zimene mumachita pa moyo wanu. *

Mwina munganene kuti, ‘Sindingayambe kudandaula za thanzi langa panopa chifukwa ndidakali mwana.’ Koma kodi zimenezi ndi zoona? Taonani zolinga zimene zili pamwambapa. Kodi mwachonga zingati? Dziwani kuti kukhala ndi thanzi labwino n’kofunika kwambiri kuti mukwaniritse zolinga zimenezo.

N’kutheka kuti mumamva ngati Amber, * mtsikana wazaka 17, amene ananena kuti: “Sindingakhalire kudya zakudya zopangidwa ndi tirigu wosakonola, zopanda mafuta ndiponso zopanda shuga nthawi zonse.” Ngati mumamva choncho, musadandaule. Simuyenera kudera nkhawa za thanzi lanu mopitirira muyezo, mpaka kusiya kudya maswiti kapena kuyamba kumathamanga mtunda wautali kwambiri mlungu uliwonse. Mungafunike kungosintha pang’ono zochita zanu kuti muyambe kuoneka bwino, kumva bwino ndiponso kuti thupi lanu lizigwira ntchito bwino. Tiyeni tione mmene anzanu ena achitira zimenezi.

Mukamadya Zakudya Zoyenera, Mumaoneka Bwino

Baibulo limatilimbikitsa kuti tisamachite zinthu monyanyira. Lemba la Miyambo 23:20 limati: “Usakhale . . . ndi ankhuli osusuka.” Nthawi zina kutsatira malangizo amenewa n’kovuta.

“Mofanana ndi achinyamata ambiri, nthawi zonse ndimamva njala. Makolo anga amati ndikamadya ndimangokhala ngati chakudyacho ndikuponyera m’dzenje.”—Anatero Andrew, wazaka 15.

“Chifukwa chakuti panopa sindinayambe kupeza mavuto alionse ndi zakudya zina, ndimangoona kuti n’zabwinobwino.”—Anatero Danielle, wazaka 19.

Kodi mukufuna kuti muzidya modziletsa? Onani zimene anzanu ena ananena kuti zimawathandiza.

Muzidziwa kuti mwakhuta. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Julia, anati: “Poyamba ndinkawerengetsera kuchuluka kwa chakudya chomwe ndadya, koma panopa ndimangosiya kudya ndikaona kuti ndakhuta.”

Muzipewa zakudya zosalongosoka. Mnyamata wina wazaka 21, dzina lake Peter, anati: “Nditasiya zakumwa zoziziritsa kukhosi, zinandithandiza kutsitsa sikelo yanga ndi makilogalamu asanu m’mwezi umodzi wokha.”

Siyani zizolowezi zoipa za kadyedwe. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Erin, anati: “Ndimayesetsa kuti ndikatenga chakudya kamodzi, ndisatengenso china.”

Chinsinsi Chake: Nthawi ya kudya ikakwana, muzidya. Mukapanda kudya, pambuyo pake mumamva njala kwambiri ndipo mumadya mopitirira muyezo.

Mukamachita Masewera Olimbitsa Thupi Nthawi Zonse, Mumamva Bwino

Baibulo limati: “Chizolowezi chochita masewero olimbitsa thupi chipindulitsa.” (1 Timoteyo 4:8) Koma achinyamata ambiri sakonda kuchita masewera olimbitsa thupi.

“Ndili kusekondale, ana a sukulu ambirimbiri ankalephera phunziro la masewera olimbitsa thupi. Koma phunziro limeneli ndiye linali lophweka kwambiri, ngati kudya chakudya.”—Anatero Richard, wazaka 21.

“Ena amaganiza kuti, ‘Ndivutikirenji kumathamanga panja kuli chidzuwa n’kumatuluka thukuta, pamene ndikhoza kungochita masewera enaake pa kompyuta n’kumayerekezera kuti ndikuthamanga.’”—Anatero Ruth, wazaka 22.

Mukangoganizira zochita masewera olimbitsa thupi, kodi mumagwa ulesi nthawi yomweyo? Ngati mumatero, dziwani kuti kuchita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse, n’kofunika kwambiri. Mungapindule m’njira zitatu izi:

Phindu loyamba. Simudwaladwala. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Rachel, anati: “Nthawi zonse bambo anga ankandiuza kuti, ‘Ngati ulibe nthawi yochita masewera olimbitsa thupi, ndiye ukonzekere kupeza nthawi yodwala.’”

Phindu lachiwiri. Maganizo anu amakhazikika. Mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Emily, anati: “Kuthamanga kumandithandiza ndikakhala ndi zambiri zoganiza. Thupi langa limakhalanso ndi mphamvu ndipo maganizo anga amakhazikika moti sindikhalanso ndi nkhawa.”

Phindu lachitatu. Mumasangalala. Mtsikana wina wazaka 22, dzina lake Ruth, anati: “Ndimakonda kukhala panja, ndipo ndimakonda masewera monga kukwera mapiri, kusambira, kutsetsereka ndi thabwa pachipale chofewa ndiponso kupalasa njinga.”

Chinsinsi Chake: Mlungu uliwonse, muzichita masewera olimbitsa thupi amene inuyo mumakonda. Muzichita masewerawa kwa mphindi zosachepera 20, maulendo atatu pa mlungu kapena kuposa pamenepa.

Mukamagona Mokwanira, Mumagwira Bwino Ntchito

Baibulo limati: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” (Mlaliki 4:6, NW.) Ngati simugona mokwanira, thupi lanu limalephera kugwira bwino ntchito.

“Ndikapanda kugona mokwanira, sizimandiyendera. Ndimavutika kwambiri kuika maganizo anga pa chinthu chilichonse.”—Anatero Rachel, wazaka 19.

“Nthawi ikamakwana 2 koloko masana, ndimakhala nditatoperatu moti ndikhoza kugona ndili mkati mocheza.”—Anatero Kristine, wazaka 19.

Kodi mumaona kuti simugona mokwanira? Taonani zimene anzanu ena achita kuti azigona mokwanira.

Musamagone mochedwa. Mtsikana wina wazaka 18, dzina lake Catherine, anati: “Ndayamba kuyesetsa kuti ndizigona nthawi yabwino.”

Musamacheze mpaka usiku kwambiri. Mnyamata wina wazaka 21, dzina lake Richard, anati: “Nthawi zina anzanga amandiimbira foni kapena kunditumizira uthenga pa foni usiku kwambiri. Koma masiku ano, ndimasiya kuchezako n’kukagona.”

Musamasinthesinthe. Mtsikana wina wa zaka 20, dzina lake Jennifer, anati: “Masiku ano, ndikuyesetsa kuti nthawi yanga yogona ndi yodzuka izikhala yomweyo tsiku lililonse.”

Chinsinsi Chake: Muziyesetsa kuti muzigona maola 8 kapena 10 tsiku lililonse.

Pa zinthu zitatu zimene takambirana mu nkhani ino, kodi ndi chinthu chiti chimene mukufunikira kusintha pa moyo wanu?

zakudya masewera olimbitsa thupi kugona

Lembani m’munsimu zinthu zimene mukufunika kuchita kuti muthe kusintha.

․․․․․

Ngati mutayamba kusamalira thanzi lanu pochita zinthu zochepa komanso zosavuta zimene takambiranazi, mungapindule kwambiri. Dziwani kuti kukhala ndi thanzi labwino kungakuthandizeni kuti muzioneka bwino, muzimva bwino, ndiponso kuti muzigwira bwino ntchito. Ndipo mosiyana ndi zinthu zina pa moyo wanu, zili ndi inuyo kukhala ndi thanzi labwino kapena ayi. Erin anati: “Kuti mukhale ndi thanzi labwino kapena ayi, sizidalira munthu wina koma inuyo basi.”

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Tikudziwa kuti anthu ambiri ali ndi matenda kapena zilema zimene palibe chilichonse chimene angachite kuti asakhale nazo. Nkhani ino ingathandize anthu amenewa kuti akhale ndi thanzi labwinoko ngakhale kuti ali ndi mavuto amenewa.

^ ndime 13 Tasintha mayina ena m’nkhani ino.

ZOTI MUGANIZIRE

● Kodi kusamalira thanzi lanu kumakhudza bwanji mmene mumadzionera?

● Kodi mungasonyeze bwanji kuti simuchita zinthu monyanyira pa nkhani yosamalira thanzi lanu?—Afilipi 4:5.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 13]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

“Thupi la munthu lili ngati galimoto. Zonsezi zimafuna kuti mwini wake azizisamalira. N’chifukwa chake ndimakonda kuchita masewera olimbitsa thupi.”

“Ukakhala ndi munthu wochita naye masewera olimbitsa thupi, umalimbikira chifukwa sufuna kumukhumudwitsa.”

“Ndikachita masewera olimbitsa thupi ndimamva bwino kwambiri. Pakapita nthawi, ndimayamba kuoneka bwino ndipo zimenezi zimandithandiza kuti ndisamadzikayikire.”

[Zithunzi]

Ethan

Briana

Emily

[Chithunzi patsamba 14]

“Ndinasintha Moyo Wanga”

“Pamene ndinkafika zaka 6 ndinali wonenepa ndithu. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kukonda kutolatola tizakudya. Kenako nthawi zonse ndinkangokhalira kudya. Ndipo sindinkachita masewera alionse olimbitsa thupi chifukwa sindinkawakonda. Patapita zaka zingapo, ndinapezeka kuti ndanenepa kwambiri. Zimenezi sizinkandisangalatsa ngakhale pang’ono. Nthawi ndi nthawi ndinkayesetsa kusintha zakudya zimene ndimadya n’cholinga choti ndichepe thupi, koma ndinkapezeka kuti ndanenepanso. Ndili ndi zaka 15, ndinaganiza zosintha kwambiri moyo wanga. Ndinkafunitsitsa kuti ndichepe thupi potsatira njira yoyenera, imene ndikanatha kuitsatira moyo wanga wonse. Ndinagula buku lofotokoza kadyedwe koyenera ndi njira yoyenera yochitira masewera olimbitsa thupi. Ndinayamba kutsatira njira zimenezi pa moyo wanga. Ndinatsimikiza kuti ngakhale nditabwerera m’mbuyo kapena kufooka, sindisiya kutsatira malangizowa. Ndipo zinandithandizadi. Pomatha chaka chimodzi ndinali nditatsitsa sikelo yanga ndi makilogalamu 25. Sikelo yanga sinakwerenso kwa zaka ziwiri tsopano. Sindinkaganiza kuti zimenezi zingachitike. Ndikuganiza kuti zimenezi zinatheka chifukwa chakuti sindinangosintha kadyedwe kokha koma ndinasinthanso moyo wanga wonse. Nditazindikira kuti ndikuyenera kusintha chilichonse pa moyo wanga, ndinali wokonzeka ndi wofunitsitsa kuchita zimenezi.”—Anatero Catherine, wa zaka 18.

[Chithunzi patsamba 14]

Thanzi lanu lili ngati galimoto. Limafunika kulisamalira nthawi zonse