Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinasiya Ntchito ya Ndalama Zambiri

Ndinasiya Ntchito ya Ndalama Zambiri

Ndinasiya Ntchito ya Ndalama Zambiri

Yosimbidwa ndi Martha Teresa Márquez

NDINKAKONDA kwambiri kuimba kuyambira ndili wamng’ono ndipo nthawi zina ndinkaimba pa wailesi. Sukulu sindinapite nayo patali. Ndinangophunzira sukulu ya mkaka yokha basi. Kenako mtsogoleri wa gulu linalake la akatswiri oimba la m’dziko lathu anayamba kundiphunzitsa kuimba mumzinda wa Mexico City.

Mu 1969, ndili ndi zaka 24, mnzanga wina yemwe anali katswiri wovina anandiuza kuti ndikaimbe nawo pa mpikisano wa oimba kumalo achisangalalo otchuka kwambiri otchedwa La Rampa Azul. Ndinaimba nyimbo yotchuka yakuti Cucurrucucú Paloma, yolembedwa ndi katswiri wina wa ku Mexico, dzina lake Tomás Méndez, ndipo anthu anaikonda kwambiri. Ichi chinali chiyambi cha ntchito yanga yoimba. Nthawi zambiri nyimbo zanga ndinkaimba ndekha ndipo ndinkadziwika ndi dzina lakuti Romelia Romel.

Ndinkagwira ntchito limodzi ndi Tomás Méndez komanso ndi akatswiri ena a ku Mexico olemba nyimbo ndiponso oimba monga Cuco Sánchez ndi Juan Gabriel. Ndinkasangalala kwambiri kuona dzina langa litalembedwa m’manyuzi, m’magazini ndi pa zikwangwani zamagetsi. Ndinkaimba m’malo omwera mowa, pa wailesi, ndi m’madera osiyanasiyana a ku Mexico ndi ku Belize. Ndinagwiranso ntchito limodzi ndi katswiri wotchuka wanthabwala wa ku Mexico, dzina lake Leonorilda Ochoa, pa nthawi imene anangoyamba kumene kuchita pulogalamu yake pa TV.

Patapita nthawi ndinatchuka ndipo ndinkapeza ndalama zambiri moti ndinkatha kugula zinthu zodzikongoletsera zamtengo wapatali monga ndolo, mphete, ndi zina zotero. Ndinalinso ndi makhoti odula aubweya komanso ndinkakhala m’nyumba yapamwamba kwambiri. Ndinali ndi chilichonse chimene ndinkafuna pamoyo wanga koma sindinkasangalala. Ndinkaona kuti chinachake chikusoweka. Ngakhale kuti ndinakulira m’chipembedzo cha Katolika, ndinkachita manyazi kupita kutchalitchi. Ndinkadziona kuti ndinali wodetsedwa chifukwa ndinali munthu wachiwerewere.

Mmene Ndinayambira Kukonda Yehova

Nthawi ina ndikukonzekera kutulutsa chimbale choyamba cha nyimbo zanga, ndinauza mnzanga wina zinthu zimene ndimalakalaka nditachita pa moyo wanga. Mnzangayu anali woimba wa nyimbo za chamba cha ranchera ndipo dzina lake linali Lorena Wong. Ndinamuuza kuti ndimafuna nditakhala sisitere kuti ndizithandiza anthu osauka. Koma iye anati, “Umafuna utakhala sisitere? Koma mutu wako ukuyenda?”

Kenako anandifunsa kuti: “Kodi umadziwa dzina la Mulungu?”

Ndipo ine ndinamuyankha kuti: “Ambuye Yesu Khristu.”

Koma iye anati: “Ayi, dzina lake ndi Yehova. Yesu ndi Mwana wake.”

Modabwa ndinamufunsa kuti: “Yehova?” Ndinali ndisanamvepo za dzinali. Lorena anandipatsa Baibulo ndipo anandiuza kuti auza mphunzitsi wake yemwe anali wa Mboni za Yehova kuti adzacheze nane. *

Ndinali ndi njala yaikulu yauzimu ndipo nthawi iliyonse ndikakumana ndi Lorena, ndinkamufunsa kuti: “Kodi uwauza liti aphunzitsi ako aja kuti abwere?”

Podikirira aphunzitsiwo, ndinayamba kuwerenga ndekha Baibulo ndipo ndinadabwa kwambiri nditaonadi kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. (Salmo 83:18) Nditawerenga malamulo khumi, ndinadabwanso kupeza lamulo lakuti “Usachite chigololo.” (Eksodo 20:14) Pa nthawiyi n’kuti ndikukhala ndi mwamuna winawake wapabanja. Iye anandiberekera mwana wamwamuna, yemwe pa nthawiyi anali ndi miyezi 8. Ameneyu anali mwana wanga wachiwiri. Ndinali kale ndi mwana wina wamwamuna wa bambo wina, amenenso sindinakwatirane naye.

Tsiku lina ndikukonzekera nyimbo yoti ndikaimbe kwinakwake, ndinamva kugogoda pakhomo pa nyumba yanga. Nditatsegula chitseko, ndinapeza kuti anali Mauricio Linares, mphunzitsi wa Lorena uja. Iye anali limodzi ndi mkazi wake. Iwo anandiuza cholinga cha Mulungu kwa anthu ndipo anandisiyira buku lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. * Ndinalimaliza usiku umodzi wokha ngakhale kuti ndinkavutika kuwerenga mawu ena. Apa m’pamene ndinayambira kukonda Yehova.

Ndinayamba Kusintha Moyo Wanga

Pa nthawi imene Mboni za Yehova zinali kundithandiza kuphunzira Baibulo komanso kundithandiza kuti ndiziwerenga bwino, ndinazindikira kuti ndikufunikira kusintha moyo wanga kuti ndisangalatse Yehova. Ndinayamba kutaya mafano, mamendulo, ndi zithumwa zomwe ndinkakhulupirira kuti zinkandibweretsera mwayi, ngakhale kuti zinali zopangidwa ndi golide.

Ndinavutika kwambiri kuti ndisiye kusuta fodya ndi kumwa mowa mopitirira muyezo. Ndikamadutsa pasitolo yogulitsa mowa, kukhosi kwanga kunkangoti dyokodyoko. Choncho, ndinasiya kucheza ndi anzanga onse chifukwa ankandipatsa mowa komanso ankandiuza kuti ndipite nawo kukadya ndi kumwa ku malesitilanti odula. Sindinkafuna kupita kumalo amenewa chifukwa ndinkadziwa kuti ndikapitako, ndikamwa mowa mopitirira muyezo.

Zinali zovuta kwambiri kuti ndisiye kupita kumaphwando a anthu olemera ndiponso otchuka. Nditaitanidwa kuphwando la tsiku la kubadwa la katswiri wina wotchuka wa nkhonya wa ku Cuba, ndinapemphera kuti: “Yehova, phwando limeneli likhala lomaliza. Sindidzapitanso kuphwando ngati limeneli kapena kuchita chilichonse chimene inuyo simusangalala nacho.” Ndipo ndinasungadi lonjezo langa.

Ndinathetsa chibwenzi ndi mwamuna amene anandiberekera mwana wanga wachiwiri uja ngakhale kuti anali ndi chuma komanso anandilonjeza kuti andipatsa ndalama zambiri ndikapanda kumusiya. Komabe zinali zovuta kwambiri kwa ine kuthetsa chibwenzicho chifukwa ndinkamukonda kwambiri ndiponso iye ankadziwa zimenezi. Chifukwa chopsa mtima iye anandiuza kuti: “Ineyo ndiye Mulungu ndi Khristu wako.”

Koma ine ndinamuyankha kuti: “N’kutheka kuti zinalidi choncho poyamba, koma panopa Mulungu wanga ndi Yehova.” Choncho, anandiopseza kuti andilanda mwana amene anandiberekera komanso kuti andimenya.

Pa nthawiyi anthu ena anandiuza kuti kuimba kuli ngati ntchito ina iliyonse, moti ndikhoza kukhala wa Mboni n’kumaimbabe. Koma ena anandichenjeza kuti: “Zidzakhala zovuta kuti upewe kusuta fodya, kuledzera komanso anthu okonda nyimbo zako amene angafune kuchita nawe zachiwerewere.” Ndinazindikira kuti anthu amenewa akundiuza zoona.

Ndili woimba wotchuka, anthu ankandinyengerera ndi ndalama kuti ndichite nawo zoipa. Koma sindinkafunanso kukumana ndi mayesero ngati amenewa. Choncho mu 1975, ndinakana kupita ku China kukaimba, ndipo patapita miyezi 6 ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

Mavuto Komanso Zinthu Zabwino Zimene Ndakumana Nazo

Nditasiya kuimba, ndinkada nkhawa kuti ndidzisamalira bwanji ndekha komanso ndisamala bwanji ana ndi abale anga. Ndinali munthu wosaphunzira ndipo sindinkadziwa ntchito ina iliyonse kupatulapo kuimba. Mkulu wanga Irma ndi ana ake atatu komanso ana anga awiri ankadalira ineyo kuti ndiziwasamalira. Tinasamuka m’nyumba yapamwamba ija n’kukalowa m’nyumba yaing’ono ya chipinda chimodzi. Zinali zovuta kwambiri kuti tizolowere moyo wovutika chifukwa tinali titazolowera moyo wawofuwofu. Kwa nthawi ndithu, mkulu wanga ndi ana aja ankandinyoza chifukwa chosiya kuimba ndipo ankandiuza kuti ndipitirizebe kuimba. Koma ine ndinali nditatsimikiza kutumikira Yehova ndipo ndinali wokonzeka kuchita chilichonse kuti ndikwanitse zimenezi.

Ndinayamba kugulitsa katundu wanga. Ndinagulitsa zinthu zanga zodzikongoletsera, makhoti anga odula aubweya, ndi galimoto yanga. Ndipo ndalama zake n’zimene tinkagwiritsa ntchito. Koma kenako ndalamazo zinatha. Popeza mwamuna amene anandiberekera mwana wanga wachiwiri uja ankandivutitsa kwambiri, mu 1981 tinasamukira mumzinda wina kutali kwambiri ndi kumene timakhala poyamba kuti asatipezenso.

Mboni za Yehova za kudera limene tinasamukirali zinandiphunzitsa kuphika samusa, mandasi ndi zakudya zina. Kenako ndinapeza ntchito pafakitale inayake ndipo ndinkagwira usiku. Koma ntchitoyi inkandilepheretsa kupezeka nthawi zonse pamisonkhano komanso kutumikira Mulungu m’njira zina. Choncho, ndinasiya ntchitoyo n’kuyamba kuphika samusa kunyumba. Samusayu ndinkakamugulitsa m’mphepete mwa msewu. Zimenezi zandithandiza kuti ndizichita utumiki wa nthawi zonse.

Sindinong’oneza Bondo Ngakhale Pang’ono

Anthu akandifunsa ngati ndimadandaula chifukwa chosiya ntchito yanga yoimba imene inkandibweretsera ndalama zambiri, ndimawauza kuti zinthu zimene ndaphunzira zokhudza Yehova komanso zolinga zake sizingafanane ndi ntchito imeneyi. Ndine wosangalala kuti ana anga anaphunzira Baibulo, anadzipereka kwa Yehova ndiponso anakwatira Mboni zinzawo. Ana anga onse awiri, mothandizidwa ndi akazi awo, akuphunzitsa ana awo kutumikira Mulungu wathu, Yehova.

Kwa zaka pafupifupi 30, ndakhala ndili mpainiya. Limeneli ndi dzina limene Mboni za Yehova zimatchulira munthu amene amagwira ntchito yolalikira nthawi zonse. Mothandizidwa ndi Mulungu, ndathandiza anthu ambiri, kuphatikizapo Irma ndi mwana wake wamkazi, kuphunzira choonadi cha m’Baibulo ndi kudzipereka kwa Mulungu. Ndimasangalala kwambiri ndikakumana ndi anthu amene ndawaphunzitsa Baibulo n’kupeza kuti akuyendabe m’choonadi, chifukwa ndimawaona ngati ana anga. (3 Yohane 4) Ambiri mwa anthuwa akuchitanso upainiya. Panopa ndili ndi zaka 64 ndipo ndimaphunzira Baibulo ndi anthu 18.

Njala yauzimu yomwe ndinali nayo ndili mtsikana woimba, yatha tsopano. Komanso zimene ndinkalakalaka kuchita pa moyo wanga zoti ndizithandiza anthu ena, ndazikwaniritsa pomvera lamulo la Yesu lakuti, “Pitani mukapange ophunzira.” (Mateyo 28:19, 20) Ndimayamikira kwambiri Yehova chifukwa wandisamalira zaka zonsezi ndipo akupitirizabe kundisamalira. ‘Ndalawa ndipo ndaonadi kuti Yehova ndi wabwino.’—Salmo 34:8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Lorena Wong anadzakhala wa Mboni za Yehova.

^ ndime 15 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano analeka kulisindikiza.

[Chithunzi patsamba 25]

Ndili ndi ana anga, akazi awo, ndi mkulu wanga yemwe ndimachita naye limodzi upainiya

[Chithunzi patsamba 26]

Mpaka pano ndimaphikabe samusa n’kumagulitsa m’mphepete mwa msewu kuti ndipeze ndalama zodzisamalirira pochita utumiki wa nthawi zonse