Tetezani Banja Lanu ku Matenda a Chimfine
Tetezani Banja Lanu ku Matenda a Chimfine
Yesu analosera kuti m’masiku otsiriza ano, kudzakhala “miliri . . . m’malo osiyanasiyana.” (Luka 21:11) Chimfine ndi mtundu umodzi wa miliri imeneyi.
CHIMFINE * chimayambitsidwa ndi tizilombo ting’onoting’ono tosaoneka ndi maso. Tizilomboti tikalowa m’maselo a m’thupi, timachititsa kuti maselowo apange tizilombo tina tambirimbiri. Tizilombo toyambitsa chimfine timagwira ziwalo zotithandiza kupuma. Timafalitsidwa munthu wodwala chimfineyo akamayetsemula, kutsokomola kapena kulankhula. Chimfine chimakhala mliri chikagwira anthu ambiri m’dera lalikulu.
Tizilombo toyambitsa chimfine timagwira anthu, nyama komanso mbalame. Tizilomboti tili m’magulu akuluakulu atatu: A, B ndi C. Tizilombo ta m’gulu A ndi timene timadwalitsa anthu ambiri chimfine. Tizilombo toyambitsa chimfine amatigawa m’magulu enanso potengera mapulotini awiri opezeka kunja kwa thupi la tizilomboti. Mapulotini ake ndi himagulutinini (H) ndi nyulaminidezi (N).
Chimfine n’choopsa chifukwa tizilombo timene timayambitsa matendawa timachulukana mofulumira kwambiri ndiponso timasinthasintha. Komanso, tizilombo tamitundu yosiyana timatha kuphatikizana n’kupanga mtundu wina watsopano. Mtundu watsopanowu ukakhala kuti sukufanana ngakhale pang’ono ndi mitundu ina, thupi la munthu silitha kudziteteza ku tizilombo ta mtundu umenewu.
Chimfine chimafala kwambiri m’miyezi yozizira. Kafukufuku waposachedwapa wasonyeza kuti kunja kukamazizira, khungu la kachilombo koyambitsa chimfine limauma gwa! Ndipo zimenezi zimachititsa kuti kachilomboka kasafe kakakhala mumpweya. Koma kachilomboka kakalowa m’thupi, khungulo limafewa chifukwa cha kutentha ndipo zikatere kamatha kuyambitsa matenda a chimfine. Mpweya wozizira pawokha suyambitsa chimfine koma umachititsa kuti tizilombo toyambitsa matendawa tifalikire mosavuta.
Mmene Mungadzitetezere
Podziwa kufunika kodziteteza, mayiko ambiri anakhazikitsa kale njira zimene zingathandize
anthu kuti asadwale chimfine. Koma kodi inuyo mungachite chiyani? Tiyeni tione mfundo zitatu zimene zingakuthandizeni kuti mudziteteze ku chimfine:Muzigona mokwanira komanso kudya zakudya zoyenera: Muzionetsetsa kuti anthu a m’banja lanu akugona mokwanira komanso akudya zakudya zimene zimathandiza thupi kulimbana ndi matenda. Muzikonda kudya zipatso ndi ndiwo zamasamba, mgaiwa ndi zakudya zina zosakonola, komanso nyama yopanda mafuta ambiri, imene imawonjezera mphamvu ya thupi yolimbana ndi matenda.
Muzikhala malo aukhondo: Ngati zingatheke, muzipukuta mosamala malo okonzerapo zakudya ndi matebulo tsiku lililonse. Muzitsuka mapoto ndi mbale nthawi zonse mukatha kuzigwiritsira ntchito, ndipo muzichapa zofunda pafupipafupi. Muzipukuta ndi mankhwala opha tizilombo zinthu zimene anthu amazigwira kawirikawiri, monga zitseko, matelefoni, ndi zipangizo zoyatsira wailesi kapena TV. Ngati zingatheke, muzitsegula mawindo kuti m’nyumba muzilowa mpweya wabwino.
Muzidzisamalira: Muzisamba m’manja nthawi zonse ndi sopo kapena ndi mankhwala ena opha tizilombo. (Ngati mungakwanitse, muziyenda ndi kabotolo ka mankhwala opha tizilombo tam’manja.)
Musamabwerekane matawelo opukutira m’manja kapena kumaso ndi munthu aliyense, ngakhale anthu a m’banja lanu.Musamagwire maso, mphuno, kapena pakamwa panu ndi m’manja mosasamba. Ngati n’kotheka, muziphimba ndi kapepala pakamwa ndi pamphuno potsokomola kapena poyetsemula, ndipo muzitaya kapepalako nthawi yomweyo. Musamabwerekane zinthu zimene zingafalitse majelemusi, monga mafoni. Ana anu muyenera kuwaphunzitsa bwino kutsatira malangizo amenewa. Kuchita zinthu zimenezi kumathandiza nthawi zonse, koma makamaka pa nthawi imene anthu ambiri akudwala chimfine.
Muziganizira Ena
Munthu akhoza kuyamba kufalitsa matendawa patatsala tsiku limodzi kuti ayambe kusonyeza zizindikiro zoti akudwala chimfine, mpaka kufika tsiku lachisanu atayamba kudwala. Zizindikiro za matendawa sizisiyana kwenikweni ndi za chimfine wamba, kungoti chimfine chimenechi chimadwalitsa kwambiri. Zizindikiro zake ndi monga: kutentha thupi kwambiri, kupweteka kwa mutu, kutopa kwambiri, kutsokomola, ndi kuphwanya thupi. Akakhala ana, nthawi zambiri amatulukanso mamina, kuchita mseru, kusanza ndi kutsegula m’mimba. Ngati mwayamba kusonyeza zizindikiro za chimfine, ndi bwino kukhala kunyumba kuti musapatsire ena.
Mukamadwala, muzigona kwambiri ndiponso muzimwa madzi ambiri ndi zakumwa zina. Pali mankhwala ena amene angakuthandizeni ngati mutawamwa pamene mwangoyamba kumene kudwala. Ana amene akudwala chimfine simuyenera kuwapatsa Asipulini. Ngati mwayamba kuvutika kupuma, kumva kupweteka m’chifuwa kapena ngati mutu ukukupwetekani kwambiri kwa nthawi yaitali, thamangirani kuchipatala chifukwa zikhoza kutheka kuti mukudwala chibayo.
Kudwala chimfine n’kochititsa mantha. Koma ngati mutakonzekera, simungavutike kwambiri. Komanso dziwani kuti Baibulo limanena kuti m’dziko latsopano, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Pali mitundu yosiyanasiyana ya chimfine. Chimfine chomwe tikufotokoza m’nkhani ino n’choopsa kwambiri kuposa chimfine wamba.
[Bokosi patsamba 27]
CHIMFINE CHOOPSA KWAMBIRI
M’chaka cha 2009 ku Mexico kunapezeka chimfine cha mtundu wa H1N1. Mtundu umenewu ndi wofanana ndi wa chimfine chimene chinapha anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse mu 1918. Koma tizilombo toyambitsa chimfine chimene chinapezedwa ku Mexico timafananako pang’ono ndi tizilombo ta chimfine chimene chimagwira nkhumba ndi mbalame.
[Bokosi/Zithunzi pamasamba 28, 29]
NJIRA 6 ZODZITETEZERA KOMANSO ZOTETEZERA ENA
1. Muziphimba pakamwa mukamatsokomola
2. Muzisamba m’manja
3. Muzitsegula mawindo
4. Muzipukuta zinthu zogwiritsidwa ntchito kawirikawiri
5. Mukamadwala, muzikhala panyumba
6. Mukamadwala, musamapatse anthu moni wam’manja
[Bokosi/Chithunzi patsamba 29]
ZIMENE MUNGACHITE PAKAGWA MLIRI
Choyamba, muyenera kutsatira malangizo amene anthu ogwira ntchito zaumoyo angapereke. Si bwino kuchita mantha kapena kuchita zinthu mopupuluma. Tsatirani malangizo amene tafotokoza m’nkhaniyi. Ngati zingatheke, pewani kukhala pagulu la anthu ambiri. Ngati mwapezeka ndi matendawa, n’zothandiza kuvala chophimba pakamwa ndi pamphuno. Muzisamba m’manja pafupipafupi. Mungachite bwino kuguliratu zakudya zomwe sizingawole msanga, komanso mankhwala, sopo ndi zinthu zina zoti mungagwiritse ntchito kwa milungu iwiri kuchitira kuti mwina simungakwanitse kupita kumsika kapena kusitolo.
Mukakhala kuntchito, kumalo olambirira kapena kwina kulikonse komwe kuli anthu ambiri, muzitsatira malangizo amene aperekedwa kumalowo. Yesetsani kutsegula mawindo kuti kamphepo kabwino kazilowa.
[Chithunzi patsamba 27]
Kachilombo koyambitsa chimfine ka H1N1 (akakulitsa)
[Mawu a Chithunzi]
CDC/Cynthia Goldsmith