Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Tingachite Kuti Tisamapanikizike Kwambiri

Zimene Tingachite Kuti Tisamapanikizike Kwambiri

Zimene Tingachite Kuti Tisamapanikizike Kwambiri

Baibulo limafotokoza za “nthawi yovuta.” Mwina mungavomereze kuti nthawi imene tikukhalayi ndi yovutadi chifukwa timapanikizika kwambiri.—2 Timoteyo 3:1.

MONGA mukudziwira, n’zosavuta kuzimitsa kamoto kakang’ono kusiyana ndi kuzimitsa chimoto chalawilawi. Mofanana ndi zimenezi, sizivuta kuchepetsa kupanikizika ngati zinthu zimene zatipanikizazo n’zazing’ono, kusiyana ndi kuthetsa kupanikizika pambuyo poti takhala opanikizika kwa nthawi yaitali. Dokotala wina anati: “M’pofunika kwambiri kuti tikhale ndi chizolowezi choti tsiku lililonse tiziyesetsa kuchepetsa kupanikizika pa moyo wathu, ngakhale kuti masiku ano timakhala otanganidwa kwambiri.” *

Kuyesetsa kuti tsiku lililonse tisamapanikizike kwambiri kumatithandiza m’njira ziwiri. Choyamba, kumatithandiza kuti tizichepetsa zinthu zimene zingatichititse kupanikizika. Chachiwiri, kumatithandiza kudziwa zimene tingachite tikapanikizika ndi zinthu zimene sitingazipewe.

Kodi Baibulo lili ndi malangizo amene angatithandize kuchepetsa kupanikizika?

Mfundo za M’Baibulo N’zothandiza Kwambiri

Tikamaphunzira mfundo za m’Baibulo, timadziwa maganizo otsitsimula ndi olimbikitsa a Mlengi wathu. Mawu a Mulungu ali ndi malangizo odalirika kwambiri. Ndipotu, Baibulo ndi mgodi waukulu wa mfundo zimene zingatithandize kuchepetsa kupanikizika. Mfundo zimenezi zingatithandize kuti ‘tisaope, kapena kutenga nkhawa,’ komanso kuti tizipirira zinthu zimene zimatipanikiza tsiku ndi tsiku.—Yoswa 1:7-9.

Baibulo limatithandiza kuchepetsa kupanikizika chifukwa limatitsimikizira kuti Atate wathu wakumwamba, Yehova, “ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” (Yakobe 5:11) Patricia, amene ankagwira ntchito yophunzitsa pa yunivesite inayake ku California, anafotokoza kuti: “Chinthu chimodzi chimene chandithandiza kwambiri ndicho kuganizira za cholinga cha Mulungu ndi zinthu zodabwitsa zimene akuchita.”

Taganizirani mmene mawu a Yesu Khristu ndiponso zochita zake zachikondi zinalimbikitsira komanso kutsitsimula omvera ake amene anali oponderezedwa ndi opanikizika. Iye anawauza kuti: “Bwerani kwa ine, nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani [kutanthauza, kuwatsitsimutsa mwauzimu].”—Mateyo 11:28-30.

Mogwirizana ndi mawu akewa, Yesu sanali wankhanza. M’malo mwake, anasonyeza kuti ankawaganizira ophunzira ake, ndipo pa nthawi ina, iye anakonza zoti iwo ayambe apuma kaye pang’ono pa ntchito yawo yolalikira. (Maliko 6:30-32) Choncho sitiyenera kukayikira ngakhale pang’ono kuti Yesu, amene panopa ndi Mfumu kumwamba, zimamukhudza kwambiri tikamapanikizika, ndipo mwachifundo amatipatsa thandizo “panthawi yake.”—Aheberi 2:17, 18; 4:16.

Kulankhulana Bwino Kumathandiza

Kulankhulana bwino ndi chinthu chimodzi chimene chimathandiza kwambiri kuti tichepetse kupanikizika. Baibulo limaphunzitsa kuti: “Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.” (Miyambo 15:22) Choncho anthu ambiri aona kuti kulankhula ndi mwamuna kapena mkazi wawo, mnzawo, kapena wogwira naye ntchito, kumawathandiza kuchepetsa kupanikizika.

Njira imodzi yofunika kwambiri yolankhulira, kapena kuti yochitira “upo,” ndiyo kupemphera kwa Mulungu. Kupemphera kumathandiza komanso sikovuta. Kupemphera nthawi zonse kungakuthandizeni kuti “musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse.” Anthu ambiri apeza kuti chifukwa chodalira kupemphera, athandizidwa kupeza “mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira.” Mogwirizana ndi zimene Baibulo limalonjeza, ‘mitima ndi maganizo’ a anthu amenewa zimatetezedwa.—Afilipi 4:6, 7; Miyambo 14:30.

Buku lina lofotokoza za kupanikizika linati: “Anthu amene ali ndi anzawo ambiri omwenso amawalimbikitsa, savutika kwambiri ndi kupanikizika ndipo amakhala ndi maganizo abwino kusiyana ndi amene amafuna kuchita zonse paokha.” Palibe anthu amene amakhala ndi anzawo ambiri owalimbikitsa kuposa anthu amene amalambira Mulungu woona, Yehova. Potsatira malangizo a m’Baibulo, anthu amenewa amasonkhana nthawi zonse ndipo amalimbikitsana. (Aheberi 10:24, 25) Munthu wina amene amapezeka pa misonkhano imeneyi anati: “Ndimagwira ntchito maola ambiri, ndipo ndimapanikizika kwambiri. Koma ndikapita kumisonkhano, ndimaona kuti pofika nthawi imene pemphero lomaliza likuperekedwa, kupanikizika kuja kumakhala kutatha, ndipo ndimakhala nditatsitsimulidwa.”

Komanso, kukhala munthu wa nthabwala kumathandiza kwambiri kuchepetsa kupanikizika. Lemba la Mlaliki 3:4 limati pali “mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka.” Kuseka kumatsitsimula ndiponso kumatithandiza kuti tikhale ndi thanzi labwino. Dokotala wina anafotokoza kuti, “tikamaseka, thupi limatulutsa timadzi tinatake tabwino ndipo limaleka kutulutsa mankhwala enaake oipa.” Mayi wina wokwatiwa anati: “Ndikapanikizika kwambiri, mwamuna wanga amanena kapena kuchita zinthu zinazake zoseketsa, ndipo zimenezi zimandithandiza kwambiri.”

Makhalidwe Amene Amachepetsa Kupanikizika

Baibulo limatilimbikitsa kuti tikhale ndi makhalidwe amene amachepetsa kupanikizika. Makhalidwe amenewa ndi monga “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa, [ndi] kudziletsa,” ndipo amatchedwa “zipatso za mzimu” wa Mulungu. Komanso, Baibulo limatilimbikitsa kuti tipewe “kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe.” M’malo mwake limatilimbikitsa kuti tikhale “okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.”—Agalatiya 5:22, 23; Aefeso 4:31, 32.

Dokotala wina anafotokoza phindu lotsatira mfundo za m’Baibulo zimenezi, makamaka m’dziko lovuta limene tikukhala masiku anoli. Iye anati: “Kulemekeza anthu ena kumachepetsa kwambiri kupanikizika.” Baibulo limatilimbikitsanso kukhala ofatsa kapena kuti odzichepetsa, kutanthauza kuti tizidziwa zinthu zimene sitingakwanitse.—Mika 6:8.

Mulungu amafuna kuti tizivomereza modzichepetsa kuti pali zinthu zina zimene sitingazikwanitse ndi mphamvu kapena nzeru zathu zokha, ndiponso kuti sitingathe kuchita zonse zimene tingafune kuchita. Nthawi zina tingafunike kukana anthu akatipempha kuchita zinthu zimene sitingakwanitse, ndipo tiyenera kudziwa mmene tingakanire, ngakhale kuti zingakhale zovuta kutero.

Komabe, ngakhale mutatsatira malangizo onse a m’Baibulo amene afotokozedwa munkhani ino, sizikutanthauza kuti simuzipanikizika ngakhale pang’ono. Izi zili choncho chifukwa Satana Mdyerekezi akulimbana kwambiri ndi anthu amene akulambira Mulungu. Cholinga chake n’choti asonyeze kuti iwo sangapitirize kulambira Mulungu ngati atapanikizika kwambiri. (Chivumbulutso 12:17) Koma monga mmene taonera, Mulungu amatithandiza pa nthawi yake ndiponso m’njira zosiyanasiyana kuti tichepetse kupanikizika. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Ngati munthu wapanikizika kwambiri kapena kwa nthawi yaitali moti wayamba kudwala, angachite bwino kukaonana ndi dokotala.

^ ndime 20 Kuti mumve zambiri, onani Galamukani! ya February 8, 2005, ya mutu wakuti, “Zimene Mungachite Kuti Moyo Wanu Usakhale Wopanikizika,” ndi Galamukani! ya February 8, 2001 kuyambira ndi nkhani yakuti “Kutangwanitsa kwa Dzikoli.”

[Bokosi patsamba 9]

NJIRA ZINA ZOCHEPETSERA KUPANIKIZIKA

● Musamayembekezere kuti inuyo kapena anthu ena azichita zinthu zonse mosalakwitsa.—Mlaliki 7:16.

● Muzithera nthawi yanu yambiri pa zinthu zofunika.—Afilipi 1:10, 11.

● Muzichita masewera olimbitsa thupi.—1 Timoteyo 4:8.

● Muzisangalala ndi zinthu zimene Yehova analenga.—Salmo 92:4, 5.

● Muzipeza nthawi yokhala nokha.—Mateyo 14:23.

● Muzipuma ndi kugona mokwanira.—Mlaliki 4:6.

[Chithunzi patsamba 7]

Kupeza nthawi yolankhula ndi anthu ena kumathandiza kuti tisapanikizike kwambiri

[Chithunzi patsamba 7]

Kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu amalimbikitsa kumathandiza kuchepetsa kupanikizika