Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Mu January 2009, mayiko 8 okha anali ndi zida zanyukiliya zopitirira 23 300.”—STOCKHOLM INTERNATIONAL PEACE RESEARCH INSTITUTE, SWEDEN.

Mu Africa, mijigo ndi zitsime masauzande ambiri zasiya kugwira ntchito. Zambiri zinakumbidwa posachedwapa ndi chithandizo chochokera ku mayiko ena. Zitsimezi zasiya kugwira ntchito “makamaka chifukwa chakuti sizikukonzedwa. Limeneli ndi vuto laling’ono loti likanatha kupewedwa.”—INTERNATIONAL INSTITUTE FOR ENVIRONMENT AND DEVELOPMENT, BRITAIN.

Asayansi Ajambula M’mimba mwa Nyama Yakale Kwambiri

Asayansi enaake ku Russia ajambula m’mimba mwa nyama inayake yakale yooneka ngati njovu. Zithunzi zimene anajambulazo zimasonyeza mbali zosiyanasiyana za m’mimba mwa nyamayi. Nyama imene anajambulayi inafa itangokhala ndi moyo mwina miyezi itatu kapena inayi. Nyamayi inapezeka itakwiririka ndi madzi oundana m’dera lozizira kwambiri la Yamalo-Nenets, kum’mwera chakumadzulo kwa dziko la Russia. Alexei Tikhonov, yemwe ndi wachiwiri kwa mkulu wa dipatimenti yoona za nyama, anati: “Nyamayi ithandiza kwambiri pophunzira za nyama zamtunduwu zomwe zinali zazikulu kwambiri kuposa njovu komanso pophunzira za nyama zina zakale zimene panopa sizipezekanso.” Ataiunika nyamayi ndi zipangizo zofanana ndi zimene masiku ano amaunikira m’thupi mwa munthu kuchipatala, anapeza kuti sinavulale pena paliponse. Anapezanso kuti m’njira imene mumadutsa mpweya komanso m’njira yodutsa chakudya munali mchenga. Zimenezi zinachititsa asayansiwo kuganiza kuti nyamayo inafa “itamira m’madzi.”

Kusudzulana Kwaphweka

Nyuzipepala ya El Universal inanena kuti panopa mumzinda wa Mexico City, kusudzulana sikukuvutanso. Mu 2008, zifukwa 21 zololeza munthu kuthetsa banja zomwe zinalembedwa m’mabuku a malamulo zinachotsedwamo. Zina mwa zifukwazi zinali kusakhulupirika ndi nkhanza. Panopa chimene munthu angachite kuti athetse banja lake ndi kungotumiza ndalama zokwana madola 400 ku akaunti yakubanki ya maloya komanso kutumiza pepala losainidwa bwino lopempha kuthetsa banja, lomwe munthu angalipeze pa Intaneti. Ndipo ayenera kunena papepalalo kuti wasiya kukonda mkazi kapena mwamuna wakeyo. Anthu sakufunikiranso kukaonekera pamaso pa woweruza. Njira imeneyi ikutenga miyezi iwiri kapena inayi kuti banja lithe pamene poyamba zinkatenga zaka. Nkhani yokhudza kasamalidwe ka ana, kulipira munthu wosudzulidwayo ndalama, kugawana katundu ndi nkhani zina zimadzaonedwa pambuyo pake.

Mbalame ya Sodo “Imathamanga Kuposa Ndege Zankhondo”

Munthu wina wochita kafukufuku pa yunivesite ya California ku Berkeley m’dziko la America, anati: “Tikayerekezera kukula kwa mbalameyi ndi kukula kwa ndege, tingati sodo amathamanga kwambiri kuposa ndege zankhondo.” Christopher Clark, anajambula asodo akusonyezana chikondi ndipo anayeza liwiro limene mbalame yaimuna imathamanga pofuna kukopa zazikazi. Iye anapeza kuti pa sekondi iliyonse, mbalamezi zinkathamanga kwambiri mpaka kufika maulendo 400 kuposa kutalika kwa thupi lake.” Clark ananena kuti tikatengera kukula kwa mbalameyi ndi ndege, mbalameyi “imathamanga kwambiri kuposa ndege yankhondo” yomwe yafika pamapeto pa liwiro lake. Mbalameyi ikamatera imakhala ikuthamanga kwambiri moti ndege itakhala kuti ikuthamanga choncho munthu woyendetsa ndegeyo akhoza kukomoka.