Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akazi Ayenera Kukhala Atumiki Mumpingo?

Kodi Akazi Ayenera Kukhala Atumiki Mumpingo?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Akazi Ayenera Kukhala Atumiki Mumpingo?

MAYI wina wachikatolika analembera kalata nyuzipepala ya USA Today kuti: “Zimandidabwitsa komanso zimandipsetsa mtima kuona kuti mpaka pano akazi sakupatsidwabe udindo mumpingo.” Anthu enanso ambiri ali ndi maganizo amenewa. Komabe, m’matchalitchi ena akazi amatha kukhala atumiki mumpingo. Iwo amatha kukhala abusa, ansembe, mabishopu, ndi maudindo ena otero.

Matchalitchi amene salola akazi kukhala atumiki mumpingo amati akutsatira Baibulo. Komanso amene amalola akazi kuima kutsogolo n’kumaphunzitsa m’tchalitchi amati akutsatiranso Baibulo. Koma Baibulo siligwirizana ndi maganizo onsewa. Chifukwa chiyani? Choyamba, tiyeni tione mmene Baibulo limagwiritsira ntchito mawu akuti “mtumiki.”

Atumiki a M’nthawi ya Akhristu Oyambirira

Kodi mawu akuti “mtumiki” amatanthauza chiyani? Ambiri amangoganiza kuti mawu amenewa amanena za atsogoleri achipembedzo omwe amatsogolera mapemphero mumpingo, kaya akhale aamuna kapena aakazi. Koma Baibulo limagwiritsa ntchito mawuwa m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ananena kuti Febe ‘ankatumikira mumpingo wa ku Kenkereya.’—Aroma 16:1.

Kodi mukuganiza kuti Febe ankaima kutsogolo n’kumaphunzitsa mumpingo ku Kenkereya? Kodi ndi utumiki wotani umene Febe ankachita? M’kalata imene Paulo analembera mpingo wa ku Filipi, ananena kuti akazi ena anathandizana naye “pa ntchito [yolalikira] uthenga wabwino.”Afilipi 4:2, 3.

Njira yaikulu imene Akhristu oyambirira ankafalitsira uthenga wabwino inali kulalikira “poyera komanso kunyumba ndi nyumba.” (Machitidwe 20:20) Anthu amene ankagwira ntchitoyi anali atumiki. Ena a iwo anali akazi monga Purisikila. Iye ndi mwamuna wake ‘anafotokoza njira ya Mulungu molondola’ kwa munthu wina woopa Mulungu amene anali asanabatizidwe n’kukhala Mkhristu. (Machitidwe 18:25, 26) Zikuoneka kuti Purisikila anali mtumiki wodziwa bwino ntchito yake monga mmene analilinso Febe ndi akazi ena ambiri.

Ntchito Yofunika Kwambiri

Kodi ntchito yolalikira inali yotsika komanso yosafunika kwenikweni imene ankasiyira akazi, kuti amuna azigwira ntchito yofunika yoyendetsa mpingo? Ayi sizinali choncho. Tikutero pa zifukwa ziwiri. Choyamba, Baibulo limasonyeza bwino kuti Akhristu onse, kuphatikizapo amuna amene anali ndi udindo waukulu mumpingo, ankafunika kulalikira. (Luka 9:1, 2) Chachiwiri, kulalikira kunali njira yaikulu imene Akhristu aamuna ndi aakazi omwe ankakwaniritsira lamulo la Yesu lakuti, “Mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, . . . [ndi] kuwaphunzitsa.” Ndipo zimenezi sizinasinthe mpaka pano.—Mateyo 28:19, 20.

Akazi ena alinso ndi ntchito ina yofunika mumpingo. Paulo analemba kuti: “Akazi achikulire akhale . . . aphunzitsi a zinthu zabwino; kuti akumbutse akazi ocheperapo msinkhu kukonda amuna awo, kukonda ana awo.” (Tito 2:3, 4) Choncho, akazi achikulire amene akhala akutsatira mfundo zachikhristu pa moyo wawo kwa nthawi yaitali amakhala ndi mwayi wothandiza akazi achitsikana kuti azichita zinthu mwanzeru. Imeneyinso ndi ntchito yaikulu komanso yofunika.

Kuphunzitsa Mumpingo

Koma Baibulo silimanena paliponse kuti akazi aziima kutsogolo mumpingo n’kumaphunzitsa. M’malomwake, mtumwi Paulo analangiza akazi kuti “akhale chete m’mipingo.” N’chifukwa chiyani anawalangiza choncho? Chifukwa chimodzi chimene Paulo anatchula n’chakuti zinthu “zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.” (1 Akorinto 14:34, 40) Kuti zinthu ziziyenda bwino mumpingo, Mulungu anapereka ntchito yophunzitsa kwa amuna okha basi. Komabe, dziwani kuti munthu sapatsidwa udindo woyang’anira mumpingo chifukwa chakuti ndi mwamuna basi. Kuti munthu apatsidwe udindo umenewu, pali zinthu zimene amafunika kukwaniritsa. *1 Timoteyo 3:1-7; Tito 1:5-9.

Kodi ntchito imene Mulungu wapatsa akazi ndi yotsika? Ayi. Kumbukirani kuti Yehova Mulungu anawapatsa ntchito yofunika kwambiri yolalikira za iyeyo. (Salmo 68:11) Masiku ano, amuna ndi akazi a Mboni za Yehova amene amagwira ntchito yolalikira, athandiza anthu mamiliyoni ambiri kulapa ndi kupeza njira ya ku moyo. (Machitidwe 2:21; 2 Petulo 3:9) Imeneyi si ntchito yamasewera.

Dongosolo limeneli limathandiza kuti akazi ndi amuna azikhala mwamtendere komanso kuti ena asamaoneke ngati otsika. Zimenezi zili ngati ntchito imene maso ndi makutu amagwira. Mukafuna kuwoloka msewu womwe mumadutsa magalimoto ambiri, maso ndi makutu amakuthandizani kuti musachite ngozi, ngakhale kuti amagwira ntchito zosiyana. Mofanana ndi zimenezi, amuna ndi akazi amathandizana kuchita chifuniro cha Mulungu ngakhale kuti udindo wawo si wofanana. Amuna ndi akazi akamachita zinthu mothandizana mumpingo, Mulungu amadalitsa mpingowo ndipo pamakhala mtendere.—1 Akorinto 14:33; Afilipi 4:9. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Komanso, udindo wa mwamuna mumpingo uli ndi malire. Iye ayenera kugonjera Khristu ndiponso kuchita zinthu motsatira mfundo za m’Baibulo. (1 Akorinto 11:3) Anthu amene ali ndi udindo mumpingo ayeneranso ‘kugonjerana wina ndi mnzake,’ ndipo ayenera kukhala odzichepetsa komanso ochita zinthu mogwirizana.—Aefeso 5:21.

^ ndime 15 Akazi akamatsatira dongosolo limene Mulungu anaika loti amuna azitsogolera mumpingo, amathandiza angelo kuti nawonso akhale omvera.—1 Akorinto 11:10.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi m’nthawi ya Akhristu oyambirira, akazi ankaphunzitsa m’njira yotani?—Machitidwe 18:26.

● Kodi anthu amene amapatsidwa udindo woyang’anira mumpingo amayenera kukwaniritsa zinthu zotani?—1 Timoteyo 3:1, 2.

● Kodi Mulungu amawaona bwanji akazi amene amagwira ntchito yolalikira masiku ano?—Salmo 68:11.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

“Ambuye anapatsa mawu: Akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.”—SALMO 68:11.