Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Chiyani?

Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Chiyani?

Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Chiyani?

Mboni za Yehova sizibisa zimene zimakhulupirira, moti mabuku awo amapezeka m’zilankhulo zambirimbiri. M’munsimu muli zinthu zina zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira.

1. Baibulo Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Jason David BeDuhn, yemwe ndi pulofesa wa maphunziro a zachipembedzo, analemba kuti: “[Mboni za Yehova zimatenga] ziphunzitso zawo m’Baibulo. Iwo asanayambe kukhulupirira ndiponso kuphunzitsa anthu mfundo inayake, amayamba afufuza kaye m’Baibulo.” A Mboni za Yehova amaonetsetsa kuti zimene amakhulupirira zikugwirizana ndi Baibulo, osati kuzisintha kuti zigwirizane ndi maganizo awo. Komabe iwo amadziwa kuti zinthu zina m’Baibulo n’zophiphiritsa. Mwachitsanzo, masiku 7 amene Baibulo limanena kuti zinthu zinalengedwa, ndi ophiphiritsa ndipo amaimira zaka zambiri.—Genesis 1:31; 2:4.

2. Mlengi Podzisiyanitsa ndi milungu yonyenga, Mulungu woona anadzipatsa dzina lakuti Yehova. (Akatswiri ena amakonda dzina lakuti Yahweh, limenenso linagwiritsidwa ntchito m’Baibulo lachikatolika la Jerusalem Bible.) * (Salmo 83:18) Zilembo zachiheberi zoimira dzina la Mulungu zimapezeka nthawi pafupifupi 7,000 m’zinenero zoyambirira zimene Baibulo linalembedwa. Pogogomezera kufunika kwa dzinali, Yesu m’pemphero lachitsanzo anati: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyo 6:9) Mulungu amafuna kuti anthu azipembedza iye yekha basi, ndipo m’pake kuti amafuna zimenezi. Choncho, Mboni za Yehova sizigwiritsa ntchito mafano polambira.—1 Yohane 5:21.

3. Yesu Khristu Iye ndi Mpulumutsi, “Mwana wa Mulungu,” ndiponso “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” (Yohane 1:34; Akolose 1:15; Machitidwe 5:31) Iye si Mulungu chifukwa anachita kulengedwa. Yesu mwiniwakeyo anati: “Atate ndi wamkulu kuposa ine.” (Yohane 14:28) Yesu ankakhala kumwamba asanabwere padziko lapansi, ndipo atapereka moyo wake nsembe ndi kuutsidwa, anabwerera kumwambako. Ndipo Yesu anati: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”—Yohane 14:6.

4. Ufumu wa Mulungu Ufumu umenewu ndi boma lenileni lakumwamba limene mfumu yake ndi Yesu Khristu. Iye adzalamulira ndi anthu enanso okwana 144,000, amene “anagulidwa pa dziko lapansi.” (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3, 4; Danieli 2:44; 7:13, 14) Iwo adzalamulira dziko lapansi ndipo pa nthawiyo zinthu zonse zoipa zidzachotsedwa. Dziko lonse lapansi lidzadzaza ndi anthu oopa Mulungu.—Miyambo 2:21, 22.

5. Dziko lapansi Lemba la Mlaliki 1:4 limati: “Dziko lingokhalabe masiku onse.” Anthu oipa akadzawonongedwa, dziko lapansi lidzakhala paradaiso ndipo anthu olungama adzakhalamo kosatha. (Salmo 37:10, 11, 29) Mawu amene Yesu ananena m’pemphero lake akuti “chifuniro chanu chichitike . . . pansi pano,” adzakwaniritsidwa.—Mateyo 6:10.

6. Ulosi wa m’Baibulo Baibulo limati: “Mulungu . . . sanganame.” (Tito 1:2) Choncho, chilichonse chimene Mulungu wanena chimachitika. Ndipo n’zosakayikitsa kuti ulosi wa m’Baibulo wonena za kutha kwa dziko loipali udzakwaniritsidwa. (Yesaya 55:11; Mateyo 24:3-14) Kodi ndi anthu otani amene adzapulumuke pa chiwonongeko chikubwerachi? Lemba la 1 Yohane 2:17 limati: “Wochita chifuniro cha Mulungu akhalabe kosatha.”

7. Akuluakulu a boma Yesu anati: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.” (Maliko 12:17) Mogwirizana ndi mawu amenewa, a Mboni za Yehova amamvera malamulo a dziko limene akukhala, ngati malamulowo sakutsutsana ndi malamulo a Mulungu.—Machitidwe 5:29; Aroma 13:1-3.

8. Kulalikira Yesu analosera kuti mapeto asanafike ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ udzalalikidwa padziko lonse lapansi. (Mateyo 24:14) Mboni za Yehova zimaona kuti ndi mwayi waukulu kugwira nawo ntchito yopulumutsa anthu imeneyi. Komabe, anthuwo ali ndi ufulu wosankha kumvera uthengawo kapena ayi. Baibulo limati: “Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.”—Chivumbulutso 22:17.

9. Ubatizo Mboni za Yehova zimabatiza anthu okhawo amene aphunzira Baibulo mokwanira ndipo akufuna kutumikira Mulungu monga Mboni zake. (Aheberi 12:1) Anthu amenewa amabatizidwa m’madzi posonyeza kuti adzipereka kwa Mulungu.—Mateyo 3:13, 16; 28:19.

10. Kusiyana kwa abusa ndi anthu wamba Yesu anauza otsatira ake kuti: “Nonsenu ndinu abale.” (Mateyo 23:8) Akhristu oyambirira, kuphatikizapo amene analemba nawo Baibulo, sankaona kuti anthu ena mumpingo ndi apamwamba ndipo ena ndi apansi. Mboni za Yehova zimatsatiranso zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mboni za Yehova sizinangopeka dzina lakuti “Yehova” limeneli. Kuyambira kale kwambiri, dzina la Mulungu lakuti “Yehova” lakhala likulembedwa m’zinenero zina zimene sizinagwiritsidwe ntchito polemba Baibulo koyambirira, monga Chingelezi ndi Chijeremani. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ena omasulira Baibulo masiku ano achotsa dzina la Mulungu m’Mabaibulo awo ndipo m’malomwake aikamo mawu monga “Mulungu” kapena “Ambuye.” Zimenezi zikusonyeza kuti anthu amenewa salemekeza Mlembi Wamkulu wa Baibulo.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

“Atate ndi wamkulu kuposa ine.”—Yohane 14:28

[Mawu Otsindika patsamba 9]

“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.”—Mateyo 24:14