Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mboni za Yehova Zimaphunzitsa Bwanji Baibulo?

Kodi Mboni za Yehova Zimaphunzitsa Bwanji Baibulo?

Kodi Mboni za Yehova Zimaphunzitsa Bwanji Baibulo?

Zimakambirana ndi anthu nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo ndipo nthawi zambiri zimagwiritsa ntchito buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? M’bukuli muli mitu 19 ndipo ina mwa mituyi ndi yakuti:

“Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?”

“Kodi Yesu Kristu Ndani?”

“Kodi Akufa Ali Kuti?”

“Kodi Tili ‘M’masiku Otsiriza’?”

“N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?”

“Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Likhale ndi Moyo Wosangalala”

Ophunzira amaloledwa kufunsa mafunso ndipo amaona okha mayankho ake kuchokera m’Baibulo. Kenako mogwirizana ndi zimene aphunzira m’Baibulo, amasankha okha chipembedzo chimene akufuna.

Mukhoza kupempha kuti munthu aziphunzira nanu Baibulo. Mukhozanso kuitanitsa bukuli polemba adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.