Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumadziwa Zotani Zokhudza Mboni za Yehova?

Kodi Mumadziwa Zotani Zokhudza Mboni za Yehova?

Kodi Mumadziwa Zotani Zokhudza Mboni za Yehova?

Munthu wina wophunzira za utolankhani ku Denmark anati: “Ndinawerenga zinthu zambiri pa Intaneti zokhudza Mboni za Yehova komanso ndinamva zinthu zambiri zabodza ndiponso zonyoza anthu amenewa. Chifukwa cha zimenezi, ndinayamba kudana kwambiri ndi Mboni za Yehova.”

KENAKO mtolankhaniyu anacheza ndi banja lina la Mboni za Yehova ndipo anapeza zinthu zosiyana ndi zimene ankaganiza. Iye analemba kuti: “Nditangofika kunyumba kwawo, maganizo anga okhudza anthu amenewa anasinthiratu. Ndinazindikira kuti anthu amanena zambiri chifukwa chakuti sawadziwa bwino komanso amangothamangira kuwanyoza. Inenso ndinali mmodzi wa anthu amenewa koma kenako ndinaona kuti zimene ndinkadziwa zokhudza Mboni za Yehova sizinali zoona.”—Cecilie Feyling, mtolankhani wa nyuzipepala ya Jydske Vestkysten.

Bwana wina woyang’anira masitolo enaake akuluakulu ku Ulaya, amene anagwirapo ntchito ndi Mboni za Yehova, anati: “Anthuwa sachita zachinyengo, ndi odalirika ndiponso olimbikira ntchito.” Choncho, iye ankakonda kulemba ntchito anthu a Mboni za Yehova.

Komabe, a Mboni za Yehova amadziwika ndi ntchito yawo yolalikira. Akamagwira ntchito imeneyi, anthu ena amakana kukambirana nawo nkhani za m’Baibulo, pamene ena amasangalala kukambirana nawo. Panopa, anthu oposa 7 miliyoni pafupifupi m’mayiko onse a padziko lapansi, akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ena mwa anthu amenewa pakapita nthawi amakhalanso aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Bungwe lina la zipembedzo ku United States linatulutsa lipoti losonyeza kuti pa zipembedzo zikuluzikulu 25 m’dzikolo, zipembedzo zinayi zokha n’zimene zikukula, ndipo Mboni za Yehova zili m’gulu la zipembedzo zinayi zimenezi.

Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambirimbiri akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova? Kodi Mboni za Yehova zimaphunzitsa bwanji Baibulo? Ndipo kodi anthu amene akuphunzitsidwawo amafunika kulowa chipembedzo cha Mboni za Yehova? Ngakhale kuti mwina simukufuna kukhala wa Mboni, muyenera kudziwa mayankho a mafunso amenewa. Choncho, m’malo mongomva nkhani za m’maluwa zimene anthu odana ndi Mboni amanena, fufuzani kuti mudziwe zoona zake. Lemba la Miyambo 14:15 limati: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”

Tikukhulupirira kuti magazini ino ikuthandizani kudziwa zoona zenizeni zokhudza Mboni za Yehova. Ndipotu popeza mukuwerenga magaziniyi, umenewu ndi umboni wakuti mukufuna kudziwa zambiri. Pamene mukuwerenga nkhani zitatu zotsatirazi, mungachite bwino kuwerenga mavesi amene ali m’nkhanizo pogwiritsa ntchito Baibulo lanu. * Anthu amene amachita zimenezi ndi anzeru ndiponso ali ndi “maganizo apamwamba,” mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena.—Machitidwe 17:11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Ngati mulibe Baibulo koma mumagwiritsa ntchito Intaneti, mukhoza kuwerenga Baibulo pa adiresi iyi: www.pr418.com. Pa adiresi imeneyi mukapezapo bokosi la mutu wakuti, “Werengani Baibulo pa Intaneti.” Palinso mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa 380.