Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ziwanda N’zotani?

Kodi Ziwanda N’zotani?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Ziwanda N’zotani?

MIZUKWA, ziwanda, ndondocha, azimu. Amenewa ndi ena mwa mayina amene anthu a zipembedzo zosiyanasiyana amagwiritsa ntchito pofotokoza mizimu imene amakhulupirira kuti imabweretsa mwayi, tsoka kapena zonsezi. Enanso amanena kuti nkhani yakuti kuli mizimu yangokhala chikhulupiriro chabe, koma si yoona. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi?

Baibulo limanena kuti Mlengi wathu ndi Mzimu ndiponso zolengedwa zimene anayambirira kulenga ndi mizimu. (Yohane 4:24; Aheberi 1:13, 14) Limanenanso kuti kuli mizimu yoipa ndipo m’mavesi ena mizimu imeneyi imatchulidwa kuti ziwanda. (1 Akorinto 10:20, 21; Yakobe 2:19) Koma Baibulo siliphunzitsa kuti Mulungu analenga ziwanda. Ndiye kodi ziwandazo zinachokera kuti?

“Angelo Amene Anachimwa”

Mulungu atalenga angelo, anawapatsa ufulu wosankha kuchita zabwino kapena zoipa. Koma n’zomvetsa chisoni kuti Mulungu atalenga anthu, angelo ena amene Baibulo silitchula chiwerengero chawo, anasankha kuchita zoipa. Iwo anapandukira Mulungu.

Mngelo woyamba komanso wodziwika kwambiri amene anachita zimenezi ndi Satana. Yesu Khristu anafotokoza kuti Satana kuyambira kale “sanakhazikike m’choonadi.” (Yohane 8:44) Kodi n’chiyani chinam’chititsa Satana kuti apandukire Mulungu? Iye ankafuna kuti anthu asiye kulambira Mulungu, yemwe ndi woyenera kulambiridwa chifukwa anatilenga, n’kuyamba kulambira iyeyo. Chifukwa cha mtima umenewu, iye anadzipanga yekha kukhala “Satana,” kutanthauza “wotsutsa.” Patapita zaka zambiri chichitikireni zimenezi, koma Chigumula cha Nowa chisanachitike, angelo ena anapandukiranso Mulungu. Iwo anachoka kumwamba n’kubwera padziko lapansi n’kudzakhala ngati anthu. (Genesis 6:1-4; Yakobe 1:13-15) Zikuoneka kuti pa nthawi imene Chigumula chinkachitika, “angelo amene anachimwa aja” anapita kumalo a mizimu, koma sanathe kubwerera kumwamba. (2 Petulo 2:4; Genesis 7:17-24) Kenako anayamba kudziwika ndi dzina lakuti ziwanda.—Deuteronomo 32:17; Maliko 1:34.

Angelowo anaponyedwa kumalo ena osiyana kwambiri ndi amene ankakhala asanapanduke. Lemba la Yuda 6 limati: “Angelo amene sanasunge malo awo oyambirira koma anasiya malo awo okhala, Mulungu anawasunga m’maunyolo kosatha mu mdima wandiweyani kuti akaweruzidwe tsiku lalikulu.” N’zoonekeratu kuti Mulungu sanafune kuti ziwandazi zipitirize ntchito yawo kumwamba. M’malomwake, iye anaziika “m’maenje a mdima wandiweyani,” kuti zisaonenso kuunika kwauzimu.

“Akusocheretsa Dziko Lonse Lapansi”

Ngakhale kuti ziwanda zinalandidwa mphamvu yoti zizisintha n’kukhalanso anthu, zimathabe kulimbikitsa anthu kuti azichita zinthu zoipa. Ndipo Satana, pamodzi ndi ziwanda zake, akukwanitsadi ‘kusocheretsa dziko lonse lapansi.’ (Chivumbulutso 12:9; 16:14) Kodi akukwanitsa bwanji? Akugwiritsa ntchito kwambiri “ziphunzitso za ziwanda.” (1 Timoteyo 4:1) Ziphunzitso zonyenga zimenezi, ngakhale kuti zina zimaoneka ngati zachipembedzo, zikuchititsa khungu anthu mamiliyoni ambiri kuti asadziwe choonadi chonena za Mulungu. (2 Akorinto 4:4) Zina mwa zinthu zimene ziwanda zimalimbikitsa ndi zotsatirazi:

Chiphunzitso chakuti munthu akafa amakakhala ndi moyo kwina. Ziwanda zimachititsa anthu kukhulupirira kuti anthu amoyo akhoza kulankhula ndi akufa. Zimatha kuchititsa anthu kukhulupirira kuti aona m’bale wawo amene anafa, amva mawu ake, kapena kuwachititsa kukhulupirira zinthu zinanso zosocheretsa. Zimenezi zimachititsa anthu kukhulupirira bodza lakuti munthu akafa amakakhala ndi moyo kwinakwake. Koma Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Akufa sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5, 6) Popeza kuti iwo ‘amatsikira kuli chete,’ sangalemekeze Mulungu.—Salmo 115:17. *

Makhalidwe otayirira. Lemba la 1 Yohane 5:19 limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” Satana ndi ziwanda zake alidi ndi mphamvu chifukwa, pogwiritsa ntchito mapulogalamu a pa TV, mawailesi, mabuku osiyanasiyana ndi zinthu zina zotero, akulimbikitsa anthu kuchita zinthu zotayirira. (Aefeso 2:1-3) N’chifukwa chake anthu ambiri masiku ano amachita zoipa za mtundu uliwonse kuphatikizapo chiwerewere. Ambiri amaona kuti makhalidwe amenewa ndi abwinobwino, ndipo amaona kuti anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo ndi achikale komanso amaganiza moperewera.

Kukhulupirira mizimu Mtumwi Paulo anakumana ndi mtsikana wina wantchito wogwidwa ndi “chiwanda cholosera za m’tsogolo” chimene chinkamuchititsa kuti azitha “kupezera ambuye ake phindu lochuluka mwa kumachita zoloserazo.” (Machitidwe 16:16) Paulo ankadziwa kuti ziwanda n’zimene zinkamuthandiza mtsikanayo kuchita zimenezi, choncho iye sanamvetsere zimene ankanena. Iye anachita zimenezi chifukwa sanafune kulakwira Mulungu, amene amadana ndi anthu ochita zamizimu.—Deuteronomo 18:10-12.

Dzitetezeni ku Ziwanda

Kodi mungadziteteze bwanji ku ziwanda? Baibulo limati: “Gonjerani Mulungu; koma tsutsani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani.” (Yakobe 4:7) Timasonyeza kuti tikugonjera Mulungu tikamamvera zimene Baibulo limaphunzitsa. Baibulo ndi buku lopatulika limene limavumbula “machenjera” a Satana ndi ziwanda zake. (Aefeso 6:11, 2 Akorinto 2:11) Baibulo limatiuzanso kuti mizimu yoipa, pamodzi ndi onse amene amatsutsana ndi Mulungu, sadzakhalapo mpaka kalekale. (Aroma 16:20) Koma lemba la Miyambo 2:21 limati: “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Ngati mukufuna kumva zambiri zokhudza zimene zimachitika munthu akafa komanso lonjezo la m’Baibulo lakuti akufa adzauka, onani mutu 6 ndi 7 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Mulungu analenga ziwanda?—2 Petulo 2:4.

● Kodi n’zotheka kulankhulana ndi munthu amene anafa?—Mlaliki 9:5, 6.

● Kodi mungadziteteze bwanji ku ziwanda?—Yakobe 4:7.

[Chithunzi patsamba 21]

Ziwanda zimasocheretsa anthu m’njira zambiri