Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Loya Amene Anafufuza Zimene Mboni za Yehova Zimaphunzitsa

Loya Amene Anafufuza Zimene Mboni za Yehova Zimaphunzitsa

Loya Amene Anafufuza Zimene Mboni za Yehova Zimaphunzitsa

“POYAMBA ndinkadziwa zinthu zochepa kwambiri zokhudza Mboni za Yehova,” anatero Les Civin, yemwe ndi loya komanso mkulu wa kampani ina ya maloya ku South Africa. Kenako anaganiza zofufuza ziphunzitso za Mboni za Yehova. Kodi anapeza zotani? Tamvani zimene iye anauza atolankhani a magazini ya Galamukani!

Kodi poyamba munali m’chipembedzo chiti?

Ndinabadwira m’banja la chipembedzo chachiyuda koma chakumayambiriro kwa m’ma 1970, ndinakwatira Carol, yemwe anali wa Anglican. Pa nthawiyi iye sankakonda zopemphera ndipo m’banja mwathu zachipembedzo sizinkatikhudza kwenikweni. Mwana wathu wamwamuna, dzina lake Andrew, atakwanitsa zaka 8, Carol anaganiza zoyamba kupemphera n’cholinga choti Andrew akulire m’banja lopemphera. Rabi wina anandiuza kuti ngati Carol atayamba Chiyuda, Andrew angakhalenso wachiyuda ndipo akanatha kuchitiridwa mwambo wachiyuda umene amachitira mnyamata akakwanitsa zaka 13, posonyeza kuti tsopano wakula. Choncho tinayamba maphunziro amene amachitika mlungu uliwonse kusunagoge.

Munayamba bwanji kucheza ndi Mboni za Yehova?

A Mboni za Yehova akabwera kunyumba kwathu, nthawi zambiri ndinkakana kukambirana nawo. Ndinkawauza kuti: “Ndine Myuda ndipo sindikhulupirira Chipangano Chatsopano.” Kenako Carol anandiuza kuti mnzake wina ndi wa Mboni za Yehova ndipo amadziwa kwambiri Baibulo. Carol anandipempha kuti tiphunzireko pang’ono Baibulo, ndipo monyinyirika ndinavomera zophunzira ndi Mboni za Yehova.

Mutayamba kuphunzira Baibulo, munkamva bwanji?

Ndinkawaderera kwambiri amene ankandiphunzitsawo. Maphunziro amene ndinalandira kusunagoge anandichititsa kuti ndizikonda kwambiri ziphunzitso zachiyuda komanso ndinkadziona kuti ndinabadwira mu mtundu wosankhika. Ndiye ndinkaganiza kuti, ‘Anthu awa angandiphunzitse chiyani?’ Nthawi yoyamba kukambirana ndi Mboni za Yehova, ndinauza wa Mboni amene anabwera kunyumba kwathu kuti: “Ndinabadwira m’Chiyuda ndipo ndidzafera m’Chiyuda. Chimenechi ndiye chipembedzo changa. Palibe chimene munganene chomwe chingachititse kuti ndisinthe chipembedzo changa.” Iye sanalimbane nane. Choncho, Lolemba ndi Lachisanu lililonse madzulo, tinkapita kumapemphero achiyuda ndipo Lamlungu m’mawa (ndikapanda kupeza chifukwa chokanira) tinkaphunzira ndi Mboni za Yehova. Iwo ankatiphunzitsa ulere pamene kusunagoge kuja tinkalipira.

Pokambirana, ndinkagwiritsa ntchito Baibulo langa lachiyuda chifukwa ndinkaganiza kuti a Mboni za Yehova ankagwiritsa ntchito Baibulo limene analisintha n’cholinga choti ligwirizane ndi zikhulupiriro zawo. Koma ndinadabwa kuona kuti Baibulo langa linkagwirizana kwambiri ndi Baibulo lawo. Zimenezi zinandichititsa kufuna kwambiri kuwasonyeza a Mboniwo kuti sakudziwa zimene akunena.

Carol atapita kangapo kusunagoge, anandiuza kuti akuona kuti Rabi amene ankatiphunzitsa sakudziwa zambiri zokhudza Baibulo. Iye anandiuza kuti asiya kupita kusunagoge ndipo apitirizabe kukhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu. Zimenezi zinandikhumudwitsa kwambiri ndipo ndinkaganiza zongothetsa banja lathu. Kenako mtima wanga utakhala m’malo, ndinaganiza njira ina. Popeza ndine loya, ndinaganiza zofufuza bwinobwino chipembedzo cha Mboni za Yehova kuti ndimuuze Carol kuti kagulu kampatuko kopanda maziko kameneka kamaphunzitsa zabodza.

Ndiye zinatha bwanji?

Rabi wina anandipatsa buku lotsutsa zoti maulosi okhudza Mesiya anakwaniritsidwa pa Yesu. Kwa miyezi 18, ine ndi Carol tinkaphunzira buku limeneli. Pa nthawiyi, tinapitirizabe kuphunzira ndi Mboni za Yehova mlungu uliwonse. Koma titafufuza ulosi uliwonse wa m’buku limene anatipatsa Rabi lija, ndinayamba kukayikira zimene bukulo linkanena. Mosiyana ndi zimene bukuli linkanena, ndinapeza kuti maulosi osiyanasiyana okhudza Mesiya amene ali m’Baibulo anakwaniritsidwa pa Yesu Khristu. Nkhaniyi inafika pachimake titaphunzira ulosi wopezeka pa Danieli 9:24-27, umene unasonyeza kuti Mesiya adzaonekera m’chaka cha 29 C.E. * Munthu wa Mboni amene ndinkakambirana naye anatulutsa Baibulo lokhala ndi mawu achiheberi ndi mawu achingelezi m’munsi mwake otanthauzira mawu achiheberiwo. Ndinafufuza tanthauzo la mawuwo n’kuwerengetsera zaka, ndipo kenako ndinati: “Ulosiwu ukusonyezadi kuti Mesiya anayenera kuonekera m’chaka cha 29 C.E. Koma kodi zimenezi zikukhudza bwanji Yesu?”

Munthu wa Mboni uja anati: “Chimenechi ndi chaka chimene Yesu anabatizidwa.”

Ndinachita chidwi kwambiri. Komanso ndinagoma kuona kuti maulosi a m’Baibulo ndi olondola komanso ogwirizana kwambiri.

Kodi anzanu anatani ataona kuti mwayamba kukhulupirira zinthu zosiyana ndi zimene munkakhulupirira poyamba?

Ena anatimvera chisoni kwambiri ndipo anatiuza kuti atiperekeza kwa anthu amene angatithandize kudziwa kuti tikungokhulupirira zinthu m’chimbulimbuli. Koma zoona zake n’zakuti tinafufuza kaye mozama tisanayambe kukhulupira zimene tinkakhulupirirazo.

Kodi n’chiyani chinakuchititsani kuti mukhale wa Mboni za Yehova?

Poyambirira penipeni, ndinkapita kumisonkhano ina ndi ina ku Nyumba ya Ufumu ndi mkazi wanga. Pa nthawiyi n’kuti mkazi wangayo atakhala kale wa Mboni. * Ndinachita chidwi kwambiri kuona kuti anthu a Mboni za Yehova ankakondana kwambiri popanda kuganizira za mtundu wawo ndiponso ifeyo ankationa kuti ndife anzawo. Ku chipembedzo changa chakale zimenezi sizinkachitika. Choncho patapita zaka pafupifupi zitatu ndikuphunzira ndi Mboni za Yehova, ndinabatizidwa.

Kodi mumadandaula kuti munasankha kukhala wa Mboni za Yehova?

Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala wa Mboni za Yehova. Koma ndimati ndikakumbukira mmene ndinkatsutsira choonadi, ndimaona kuti sindikuyenerera madalitso amene Yehova wandipatsa. Choncho sindinong’oneza bondo ngakhale pang’ono chifukwa cha zimene ndimakhulupirira.

Kodi mwadalitsidwa bwanji chifukwa chokhala wa Mboni za Yehova?

Ndadalitsidwa m’njira zambiri. Mwachitsanzo, ndine mkulu, kapena kuti m’busa wauzimu amene amasamalira ndi kuphunzitsa nkhosa, mumpingo wakwathu. Komanso ndimathandiza mu Dipatimenti Yoona za Malamulo pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku South Africa. Koma madalitso aakulu amene ndapeza ndi akuti ndamudziwa bwino Yehova ndi Mwana wake. Ndadziwanso bwino nthawi yomwe tikukhalayi ndiponso tanthauzo la zinthu zimene zikuchitika padzikoli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 C.E. ndi mawu achidule achingelezi oimira “Common Era” omwe amatanthauza “M’nyengo Yathu Ino.” Ngati mukufuna kudziwa zambiri za ulosi wa Danieli wokhudza Mesiya, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? patsamba 198.

^ ndime 18 Carol anamwalira mu 1994, ndipo Les Civin anakwatiranso.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Ndinagoma kuona kuti maulosi a m’Baibulo ndi olondola komanso ogwirizana kwambiri