Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mahatchi Ofatsa Koma Amphamvu

Mahatchi Ofatsa Koma Amphamvu

Mahatchi Ofatsa Koma Amphamvu

● M’mayiko ena, ku zionetsero kumakhala mahatchi enaake ang’onoang’ono otchedwa Shetland. Mahatchiwa ali ndi dzina limeneli chifukwa poyambiririra penipeni ankapezeka pachilumba cha Shetland, kumpoto chakum’mawa kwa dziko la Scotland. Ndipo posachedwapa, akatswiri a zinthu zakale anafukula pachilumbachi mafupa a mahatchi ang’onoang’ono omwe akusonyeza kuti mahatchi ake anafa zaka masauzande ambiri apitawo.

Mahatchiwa ndi osavuta kuwazindikira chifukwa ali ndi miyendo yaifupi, ubweya wam’khosi wautali, mchira wautali ndiponso thupi la ubweya wambiri. Ubweyawu unkawathandiza m’nyengo yozizira ya kumalo kumene anachokera. Mahatchiwa amatalika masentimita kuyambira 70 mpaka 107 ndipo nthawi zambiri amakhala oderako kapena akuda ndithu. Anthu akafuna kuyeza kutalika kwa mahatchiwa, nthawi zambiri amagwiritsa ntchito mainchi osati mikono, monga mmene zimakhalira ndi mahatchi ena. Mahatchi aatali kwambiri a mtunduwu sapitirira masentimita 107, pamene mahatchi ena a ku America a mtundu womwewu amatalika mpaka kufika masentimita 117.

Ngakhale kuti mahatchiwa ndi aang’ono, amakhala amphamvu kwambiri. Ndipo tikatengera kukula kwa thupi lawo, tingati ndi amphamvu kwambiri kuposa mahatchi ena onse. Pa chifukwa chimenechi, kale anthu ankagwiritsa ntchito mahatchiwa ponyamula malasha, kulima, ndiponso kunyamula katundu wosiyanasiyana m’migodi ya malasha, mmene nyama zazikulu sizingadutse chifukwa cha kuchepa kwa njira zake. Mahatchi ena ankakhala moyo wawo wonse m’migodi, choncho sankaona dzuwa ngakhale pang’ono.

Mahatchiwa akaphunzitsidwa bwino, amakhala ofatsa komanso omvera ndipo ana amatha kusewera nawo. Chifukwa cha kufatsaku, madokotala ena amauza anthu olumala kuti azisewera ndi mahatchiwa ndipo zimenezi zimawathandiza kwambiri.

Popeza anthu ambiri amawakonda mahatchiwa, komanso amatha kukhala malo alionse, amatumizidwa kumayiko osiyanasiyana padziko lonse. Amatumizidwanso m’mabungwe a anthu okonda mahatchi ndipo m’mayiko ambiri muli malo amene amalembetserako mahatchiwa m’kaundula. Komabe, ngakhale kuti masiku ano mahatchiwa akupezeka m’mayiko ambiri, dzina lawo limasonyezabe kuti anachokera ku Shetland. Pachilumbachi, mahatchiwa ndi athanzi komanso mtundu wawo sunasakanikirane ndi mitundu ina ya mahatchi.

[Chithunzi patsamba 24]

Tikatengera kukula kwawo, mahatchiwa ndi amphamvu kwambiri pa mahatchi onse

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

© S Sailer/A Sailer/age fotostock