Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Ena Amanena

Zimene Ena Amanena

Zimene Ena Amanena

France “Mboni za Yehova zimamvera malamulo a dziko. . . . Iwo sasokoneza chitetezo cha dziko. Amagwira ntchito mwakhama, amalipira misonkho mokhulupirika, amagwira ntchito zachitukuko modzipereka komanso amathandiza anthu ovutika. Zimasangalatsa kwambiri kuona Mboni za Yehova zochokera m’mitundu yosiyanasiyana zikukhala pamodzi mwamtendere pamisonkhano yawo. . . . Anthu onse akanakhala a Mboni za Yehova, bwenzi apolisife tikusowa ntchito.”—Anatero mneneri wa bungwe linalake la apolisi ku France.

Ukraine “Mboni za Yehova zimayesetsa kwambiri kuphunzitsa ana awo makhalidwe abwino. Amaphunzitsa ana awo kuti azipewa makhalidwe oipa amene angaike moyo wawo kapena wa anthu ena pangozi. Iwo amayesetsa kuchita zimenezi ngakhale kuti anthu ambiri masiku ano amaona kuti makhalidwe amenewo ndi abwinobwino. Iwo amachenjeza ana awo za kuipa kogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kusuta fodya kapena kuledzera. Amayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo komanso kugwira ntchito mwakhama. . . . Mboni za Yehova zimaphunzitsa ana awo kuti azilemekeza anthu audindo komanso anthu ena. Amawaphunzitsanso kuti asamabe kapena kuwononga katundu wa anthu ena komanso kuti azimvera malamulo a boma.”—Anatero Pulofesa Petro Yarotsky m’buku lakuti The History of Religion in Ukraine.

Italy “Anthu okwana 30,000 anali phee! m’bwalo la masewera la Olympic . . . Panalibe kutaya zinyalala mwachisawawa, kuchita phokoso kapena kukalipirana. Ndi mmene zinthu zinalili dzulo m’bwalo la masewera la Olympic . . . Panalibe munthu ngakhale mmodzi amene amanyoza anzake, kusuta fodya kapena kumwa mowa. Anthu ake amangowerenga Baibulo ndiponso kulemba mfundo za msonkhanowo. Ngakhale ana awo samavuta.”—Inatero nyuzipepala ya L’Unità, m’lipoti lake lofotokoza za msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova ku Rome.

Britain “Dikoni wamkulu m’tawuni ya Cheltenham, ananena kuti [Tchalitchi cha ku England] chikufunika kukhala ndi anthu odzipereka, amene angamayende m’madera osiyanasiyana n’kumalalikira ngati Mboni za Yehova.”—Inatero magazini ya The Gazette, ya dayosisi ya ku Gloucester.

Netherlands Anthu amene amakhala pafupi ndi Nyumba ya Ufumu mumzinda wa Leeuwarden analembera kalata Mboni za Yehova za kumeneko. M’kalatayo, iwo anati: “Tikufuna kukuthokozani chifukwa chothandiza kwambiri kuti msewu wa Noorder uzioneka wokongola. Anthu anu amavala bwino nthawi zonse ndipo ndi anthu amakhalidwe abwino. Ana anu ndi oleredwa bwino. Anthu anu saimika magalimoto pamalo oletsedwa, sataya zinyalala mumsewu ndiponso msewu wapafupi ndi Nyumba ya Ufumu umakhala wooneka bwino nthawi zonse. Tikufuna kuti mupitirizebe kukhala pafupi nafe mpaka kalekale chifukwa timasangalala kukhala nanu limodzi.”

Mexico Pulofesa Elio Masferrer wa pasukulu ina yophunzitsa za chikhalidwe ndi mbiri yakale, ananena kuti Mboni za Yehova zathandiza kwambiri anthu amene “akumana ndi mavuto aakulu m’banja mwawo monga kuwagwiririra, kuwamenya, uchidakwa ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.” Iye ananena kuti zimene Mboni za Yehova zimaphunzitsa “zimathandiza anthu amene amadziona kuti ndi achabechabe, ndipo anthuwa amayamba kudziona kuti ndi ofunika” ndiponso zimawathandiza “kupewa mavuto aakulu chifukwa amasintha n’kuyamba kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu.”—Inatero nyuzipepala ya Excélsior.

Brazil Nyuzipepala ina inanena kuti: “Gulu la Mboni za Yehova ndi logometsa. Malo amene amachitira misonkhano yawo amakhala aukhondo nthawi zonse. Chilichonse chimakhala m’malo mwake . . . Msonkhano wawo ukatha, malowo amawasiya akuoneka bwino kwambiri kuposa mmene anawapezera. Wokamba nkhani akamalankhula, aliyense amakhala phee! kumvetsera. Sipakhala zokankhanakankhana. Aliyense amayesetsa kusonyeza khalidwe labwino. . . . Kunena zoona anthu ake amachita zinthu mwadongosolo. Iwo amadziwadi kulambira Mulungu.”—Inatero nyuzipepala ya Comércio da Franca.

Mboni za Yehova zimakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mlengi ndi amene amadziwa bwino mfundo zimene anthu ayenera kutsatira pa moyo wawo kuposa munthu wina aliyense. (Yesaya 48:17, 18) Choncho munthu aliyense akawayamikira chifukwa cha khalidwe lawo labwino, Mboni za Yehova zimatamanda Mlengi wawo. Yesu anati: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wa kumwamba.”—Mateyo 5:16.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

“Mboni za Yehova zimaphunzitsa ana awo makhalidwe abwino . . . komanso kuti azimvera malamulo a boma”

[Mawu Otsindika patsamba 5]

‘. . . Anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana atakhala pamodzi mwamtendere pamsonkhano . . . ’