Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Ndani Ankagwira Ntchito Imeneyi?

1. Tchulani asodzi awiri amene anali ana a Zebedayo komanso atumwi a Yesu.

Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi.

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mateyo 4:21, 22.

․․․․․

2. Tchulani mayina a atumwi ena awiri omwe analinso asodzi.

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mateyo 4:18.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti ophunzira ake adzakhala “asodzi a anthu”? (Mateyo 4:19) Kodi usodzi wa nsomba ndi wa anthu ukufanana bwanji komanso ukusiyana bwanji?

KODI MUKUDZIWA CHIYANI ZOKHUDZA MTUMWI ANDIREYA?

3. Asanayambe kutsatira Yesu, kodi Andireya anali wophunzira wa ndani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Maliko 1:4; Yohane 1:35-40.

․․․․․

4. Kodi Andireya anauza ndani za Yesu, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Yohane 1:40-42.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi kuuza abale anu zinthu zimene mukudziwa zokhudza Yesu kuli ndi ubwino wotani? Komabe, kodi abale anu ena angachite chiyani mutawauza zimenezi?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mateyo 10:32-37.

ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 3 Kodi munthu wochenjera amasamalira chiyani? Miyambo 14:․․․

TSAMBA 8 Kodi Mulungu anadzipatsa dzina loti chiyani? Salmo 83:․․․

TSAMBA 20 Kodi angelo amene anachimwa chinawachitikira n’chiyani? Yuda:․․․

TSAMBA 26 Kodi n’chiyani chimachitika munthu ‘akamalimbikira mkwiyo’? Miyambo 30:․․․

● Mayankho ali patsamba 11

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Yakobe ndi Yohane.

2. Petulo ndi Andireya.

3. Yohane M’batizi.

4. M’bale wake Petulo, ndipo anadzakhala wophunzira wa Yesu.