Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ambiri Amasungulumwa Ngakhale Kuti Pali Njira Zambiri Zolankhulirana

Anthu Ambiri Amasungulumwa Ngakhale Kuti Pali Njira Zambiri Zolankhulirana

Anthu Ambiri Amasungulumwa Ngakhale Kuti Pali Njira Zambiri Zolankhulirana

MASIKU ano, pali njira zambirimbiri zolankhulirana, monga kuimbirana foni, kutumizirana mauthenga pa foni ndi pa kompyuta, ndiponso kucheza ndi anthu osiyanasiyana pa Intaneti. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri, ana ndi akulu omwe, amasungulumwa. Chifukwa chiyani?

Anthu ena ochita kafukufuku, John T. Cacioppo ndi William Patrick, analemba buku limene linafotokoza zambiri zokhudza kusungulumwa. M’buku lawolo, iwo ananena kuti kafukufuku winawake anasonyeza kuti “anthu akamagwiritsa ntchito kwambiri Intaneti m’malo moonana pamasom’pamaso, akhoza kukhala osungulumwa kwambiri komanso akhoza kuyamba kudwala matenda ovutika maganizo.”—Loneliness—Human Nature and the Need for Social Connection.

Anthu ambiri masiku ano amatanganidwa, ndipo sapeza nthawi yocheza bwinobwino ndi anzawo. Munthu akamalankhula ndi munthu wina pamasom’pamaso, amatha kuona munthu winayo akumwetulira. Komanso munthu akamaona nkhope ya mnzakeyo, amatha kudziwa kuti amamukonda. Koma nthawi zambiri sangathe kuona zimenezi akamalankhula naye pa foni kapena akamawerenga uthenga wake pa kompyuta.

Zimenezi zimachitika kuntchito ngakhalenso kunyumba. M’mabanja ambiri, anthu osiyanasiyana a pabanjapo amabwera n’kuchoka panyumbapo nthawi zosiyanasiyana, ndipo sadyera limodzi chakudya kapena kucheza. Achinyamata amakhala ndi kompyuta yawoyawo ndipo amangodzitsekera kuchipinda, zomwe zimawalepheretsa kucheza ndi abale awo. Komabe, ngakhale kuti achinyamata amakhala ndi zipangizo zamakono zolankhulirana, ambiri amasungulumwa.

Masiku ano ngakhale anthu amene ali pabanja amatha kukhala osungulumwa ndipo nthawi zina zimenezi zimasokoneza banjalo. Ngati mwamuna ndi mkazi wake sakulankhulana, aliyense amayamba kumangochita zake, ngakhale kuti akukhala nyumba imodzi. Zimenezi zingawachititse kuti akhale osungulumwa. Ndipotu kukhala wosungulumwa uli pabanja n’chinthu chopweteka kwambiri.

Makolo amene akulera okha ana, nthawi zambiri amakhala osungulumwa. Mwa zina, masiku ano kuli njira zambiri zolankhulirana zimene zingalepheretse makolowa kucheza bwinobwino ndi ana awo. Komanso anthu ambiri osakwatira amafuna atapeza munthu woti akhale naye pabanja, koma nthawi zina samupeza. Zonsezi zingachititse kuti anthu amenewa akhale osungulumwa.

Kusungulumwa kumachititsa anthu ena kuyamba kuchita makhalidwe osiyanasiyana oipa, monga kumwa mowa mwauchidakwa, kudya mopitirira muyezo, kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo ndiponso kuchita zachiwerewere. Enanso amatha kudzipha kumene. Choncho kudziwa zinthu zimene zimayambitsa kusungulumwa n’kothandiza kwambiri. Munthu akadziwa zimenezi, akhoza kuyamba kuchita zinthu zimene zingamuthandize kuti asamakhale wosungulumwa.