Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chimtengo Chachikulu Chochokera ku Kanthanga Kakang’ono

Chimtengo Chachikulu Chochokera ku Kanthanga Kakang’ono

Chimtengo Chachikulu Chochokera ku Kanthanga Kakang’ono

Kanthanga kakang’ono kwambiri kooneka ngati kadzira kanathothoka mumtengo n’kugwa pansi. Kenako gologolo wina akuthamanga anakakwirira ndipo kanaiwalika. Patapita nthawi, kanthangako kanamera ndipo kanakula n’kukhala chimtengo chachikulu kwambiri ngati mmene chikuonekera pachithunzipa. Mtengo umenewu umakula kwambiri komanso ndi wolimba kwambiri kuposa mitengo yonse yachilengedwe ya ku Britain.

Pali nkhani ndi nthano zambiri zimene zimanena za mtengo umenewu. Mtengowu umatha kukhala zaka zoposa 1,000. Ina imatalika mpaka mamita 40. Mitengo imene yakhala zaka zambiri imakhala ndi thunthu lalikulu kwambiri komanso nthambi zotambalala kwambiri. Ku Britain kuli mitundu iwiri ya mitengo imeneyi koma padziko lonse pali mitundu pafupifupi 450. Mitengo yonseyi anthu amaizindikira mosavuta chifukwa cha kanthanga kake.

Mumtengomu mumakhala zamoyo zambiri kuposa mtengo wina uliwonse ku Britain. Zina mwa zamoyo zimenezi ndi tizilombo tosiyanasiyana. Mbozi zambiri zimakonda kudya masamba anthete a mtengowu. Koma mtengowu umadziteteza ku tizilombo timeneti chifukwa masamba ake akamakhwima amayamba kuchita khambi.

Zamoyo zosiyanasiyana zimapezeka m’mbali iliyonse ya mtengowu. Tizilombo tosiyanasiyana timene timakhala mumtengowu timakopa mbalame zambiri ndi akangaude osiyanasiyana. Tizilombo tina timalowa m’makungwa a mtengowu, omwe amakhala ndi ming’aluming’alu, n’kumakaboola mkati mwake. Mileme ndi akadzidzi amakhala m’mapanga muthunthu la mtengowu. Tinyama ting’onoting’ono monga mbewa, akalulu, ankhandwe ndi tinyama tina timakumba n’kubisala m’mizu ya mtengowu.

Chaka chilichonse, masamba a mtengowu okwana pafupifupi 250,000, amagwera pansi. M’kupita kwa nthawi, masambawo amawola chifukwa cha tizilombo towoletsa zinthu ndipo zimenezi zimawonjezera chonde m’nthaka. M’zaka zina, mtengowo umabala zipatso zokwana 50,000. Nthanga zambiri za zipatso zimenezi zimadyedwa ndi mbalame kapena nyama zina. Nthata ndi tizilombo tina tooneka ngati sesenya timadya nthambi zouma za mtengowu ndipo makungwa ake amadyekadyeka ndi zinthu zina zimene zimamera pamtengowo.

Matabwa a mtengowu amakhala olimba kwambiri. Kwa zaka zambiri, anthu akhala akugwiritsa ntchito matabwa amenewa pomanga nyumba ndiponso popanga mipando ndi zinthu zina zamatabwa zokongola kwambiri. Matabwa amenewa amakhala bwino kwambiri kupangira migolo yosungiramo mowa ndi vinyo kuti zisase. Kwa zaka zambiri, sitima zapanyanja zolimba kwambiri zopangidwa ndi matabwawa zinathandiza gulu la asilikali apanyanja a ku Britain kugonjetsa magulu ambiri a asilikali ankhondo.

Anthu ambiri amakondabe matabwa a mtengowu mpaka lero. Mtengowu, womwe umapezeka ponseponse ku Britain, anthu amaukonda chifukwa ndi wolimba komanso umakhala zaka zambiri. N’zochititsa chidwi kwambiri kuti chimtengo chachikulu chimenechi chimachokera ku kanthanga kakang’ono zedi. Zimenezi zikusonyeza kuti amene analenga mtengowu ndi wanzeru kwambiri.

[Chithunzi patsamba 18]

Mtengowu umatha kukhala zaka zoposa 1,000 ndiponso kutalika mamita 40. Thunthu lake limatha kukula mpaka kuposa mamita 12

[Mawu a Chithunzi patsamba 18]

Tree: © John Martin/Alamy; acorn: © David Chapman/Alamy